cha64-0322 kutenga chipata cha mdani pambuyo pa yesero vgrdownload.branham.org/pdf/cha/cha64-0322...

30
KUTENGA CHIPATA CHA MDA NI P AMBUYO P A Y ESERO Ndikudabwa zimenezo…Inu mukudziwa, ine ndiri ndi lingaliro laling’ono, ndimakonda, kuwawona anthu ataima pamene ife tikuwerenga Mawu. Kodi inu simumazikonda zimenezo? Ife timaimirira kuti tipereke ulemu, ife timaima chifukwa cha fuko lathu, nanga bwanji osaimirira chifukwa cha Mawu tsopano? 2 Pamene ife tiri chiimire miniti chabe. Ine ndinali kuwerenga nkhani, osati kale litali, ndipo ine ndimalingalira usiku watha za anthu amenewo amene anamuimira Khristu. Ngati inu simunachitepo zimenezo, kodi inu simungachite izo lero? 3 Kunali mlaliki wamphamvu, pafupifupi zaka sevente-faivi zapitazo, ine ndikulephera basi kuganizira dzina lake. Ine ndikuganiza anali Arthur McCoy, ndipo iye anali atawolokera kutsidya. Ndipo usiku wina anali ndi loto kuti iye anali atapita ku Ulemelero. Ndipo anati anakafika mpaka pa Chipata, ndipo iye anati iwo samamulola iye kuti alowe. Ndipo anati iye anati, “Ndine Arthur McCoy wochokera ku United States. Ndine mlaliki.” 4 Kotero wapachipata analowa, (tsopano ili linali loto), ndipo iye analowa, anati, “ine ndikulephera kupeza dzina lako.” Iye anati, “Chabwino, ine ndinali mlaliki.” Iye anati, “Bwana, ine…” 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti…Pali chinachake chimene chalakwika.” 6 Iye anati, “Ayi, bwana. Ine ndiri ndi Bukhu apa. Ine ndikulephera kupeza dzina lako ndithu.” Ndipo iye anati, “Chabwino, kodi ine ndingachitepo kalikonse?” 7 Iye anati, “Iwe ukhoza kukachita apilo mulandu wako ku Mpando Wachifumu Wachiweruzo.” Mulungu, andithandize. Ine sindikufuna kuti ndikakhale kumeneko. 8 Iye anati, “Chabwino, ngati ndicho chiyembekezo changa chokhacho, ine ndikuganiza ine ndingochita apilo ndiye.” 9 Ndipo anati ndiye iye akuganiza kuti anapita kutali, ndipo basi…Ndipo pamene iye amayamba, anati unali mdima, ndipo kumawala ndi kumawala, ndipo anati mumawoneka ngati panalibe malo ena amene Kuwala uku kumathera, koma iye

Upload: others

Post on 02-Aug-2020

4 views

Category:

Documents


0 download

TRANSCRIPT

Page 1: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGACHIPATACHA MDANI

PAMBUYO PAYESERO

Ndikudabwa zimenezo…Inu mukudziwa, ine ndiri ndilingaliro laling’ono, ndimakonda, kuwawona anthu ataima

pamene ife tikuwerenga Mawu. Kodi inu simumazikondazimenezo? Ife timaimirira kuti tipereke ulemu, ife timaimachifukwa cha fuko lathu, nanga bwanji osaimirira chifukwa chaMawu tsopano?2 Pamene ife tiri chiimire miniti chabe. Ine ndinali kuwerengankhani, osati kale litali, ndipo ine ndimalingalira usiku wathaza anthu amenewo amene anamuimira Khristu. Ngati inusimunachitepo zimenezo, kodi inu simungachite izo lero?3 Kunali mlaliki wamphamvu, pafupifupi zaka sevente-faivizapitazo, ine ndikulephera basi kuganizira dzina lake. Inendikuganiza anali Arthur McCoy, ndipo iye anali atawolokerakutsidya. Ndipo usiku wina anali ndi loto kuti iye anali atapitaku Ulemelero. Ndipo anati anakafika mpaka pa Chipata, ndipoiye anati iwo samamulola iye kuti alowe. Ndipo anati iye anati,“Ndine Arthur McCoy wochokera ku United States. Ndinemlaliki.”4 Kotero wapachipata analowa, (tsopano ili linali loto), ndipoiye analowa, anati, “ine ndikulephera kupeza dzina lako.”

Iye anati, “Chabwino, ine ndinali mlaliki.”

Iye anati, “Bwana, ine…”5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti…Palichinachake chimene chalakwika.”6 Iye anati, “Ayi, bwana. Ine ndiri ndi Bukhu apa. Inendikulephera kupeza dzina lako ndithu.”

Ndipo iye anati, “Chabwino, kodi ine ndingachitepokalikonse?”7 Iye anati, “Iwe ukhoza kukachita apilo mulandu wako kuMpando WachifumuWachiweruzo.” Mulungu, andithandize. Inesindikufuna kuti ndikakhale kumeneko.8 Iye anati, “Chabwino, ngati ndicho chiyembekezo changachokhacho, ine ndikuganiza ine ndingochita apilo ndiye.”9 Ndipo anati ndiye iye akuganiza kuti anapita kutali, ndipobasi…Ndipo pamene iye amayamba, anati unali mdima, ndipokumawala ndi kumawala, ndipo anati mumawoneka ngatipanalibe malo ena amene Kuwala uku kumathera, koma iye

Page 2: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

2 MAWU OLANKHULIDWA

anali pakati kumene pa Iko. Ndipo anati Iye anati, “NdaniakuyandikiraMpandoWangaWachifumuWachiweruzo?”10 Iye anati, “Ndine Arthur McCoy. Ndine mlaliki, ndatumizamiyoyo yambiri ku Ufumu.”

Iye anati, “Kodi dzina lako silinapezeke pa Bukhu?”“Ayi.”Anati, “Ndiye wachita apilo kuKhothi Langa?”“Inde, bwana.”

11 “Iwe ulandira chirungamo. Ine ndikuweruza iwe pogwiritsantchito malamulo Anga. Arthur McCoy, kodi iwe unayambawanamapo?”12 Iye anati, “Ine ndinkaganiza ndinali munthu wabwinokufikira nditaima mu Kuwala kumeneko.” Iye anati, “Komamu Kukhalapo kwa Kuwala kumeneko, ine ndinali wochimwa.”Ife tonse tidzakhala momwemo. Iwe ukhoza kumadzimvawotetezeka pakali pano, koma udikire mpaka udzafikeKumeneko. Inu mukuganiza kuti zimamveka bwanji kunopamene Iye akudzodza? Momwe iwe umadzimva kuchepa!Nanga zidzakhala bwanji pa MpandoWachifumu wa Chiweruzouwo?

Iye anati, “Kodi iwe unayambawanenapo bodza?”13 Iye anati, “Ine ndimaganiza kuti ine ndinali woona, komazinthu zina zazing’ono zimene ine ndimaganiza kuti tinalitimabodza tating’ono toyera, ito tinakasanduka tatikulu nditakuda Kumeneko.”

Iye anati, “Inde, bwana, ine ndinanenapo bodza.”Iye anati, “Kodi iwe unayambawabapo?”

14 Iye anati, “Ine ndimaganiza kuti ndinali woonamtima za izo,ndipo sindinabepo,” koma anati, “mu Kukhalapo kwa Kuwalakumeneko, ine—ine ndinazindikira kuti panali akatangale enaamene ine ndinachita, amene sanali abwino basi.”

Iye anati, “Inde, bwana, ine ndinabapo.”Iye anati, “Chiweruzo changa…”

15 Ndipo iye anatsala pang’ono basi kuti amve chigamulochake, “Nyamuka waku moto wanthawizonse umeneunakonzedwera mdierekezi ndi angelo ake,” anati fupa lirilonselinali kulekana.16 Anati, “Ine ndinamva Liwu lokometsetsa limenendinayamba ndalimvapo mu moyo wanga.” Iye anati, “Pameneine ndinapotoloka kuti ndipenye, ine ndinawona nkhopeyokometsetsa imene ine ndinayamba ndaiwonapo; yokomakuposa nkhope ya mayi, liwu lokoma kuposa limene amayianga anayamba andiitanirapo ine.” Anati, “Ine ndinayang’anapozungulira. Ine ndinamva Liwu, linati, ‘Atate, izo nzoona, iye

Page 3: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 3

ananenapo mabodza ndipo sanali woona basi. Koma, pansi kudziko lapansi iye amandiimira Ine,’ anati, ‘tsopano Ine ndiimammalo mwake.’”17 Ndicho chimene ndikufuna chidzakandichitikire Kumeneko.Ine ndikufuna kuti ndimuimire Iye tsopano, kuti, pamene nthawiimeneyo idzafika, Iye adzakaimemmalo anga.18 Tiyeni tiwerenge kuchokera ku Genesis 22: 15, 16, 17, ndindime ya 18.

Ndipo mngelo wa AMBUYE anamuitana Abrahamukuchokera kumwamba kachiwiri.Ndipo anati, Pa ndekha ine ndalumbira, atero AMBUYE,

pakuti chifukwa iwe wachita chinthu ichi, ndiposunandikaniza mwana wako, mwana wako yekhayo.Kuti kudalitsa ndidzakudalitsa iwe,…kuchurukitsa

ndidzachurukitsa mbewu zako monga nyenyezi zakumwamba, ndi monga mchenga umene uli mmphepetemwa nyanja; ndipo mbewu yako idzatenga chipata chamdani wake;Ndipo mwa mbewu yako mitundu yonse ya dziko

lapansi idzadalitsidwa; chifukwa iwe wamvera mawuanga.Tiyeni tipemphere.

19 Atate Akumwamba, mutenge mutuwu tsopano, Ambuye,ndipo mutumikire kwa ife. Mulole Mzimu Woyera uwatengeMawu, Ambuye, uwapititse ku mtima uliwonse. Umeneungakomane ndi ziyembekezero zathu masana ano, pakutiizo ndi zopambana, Ambuye. Ndipo Inu munatiuza ife kutitizipempha zochuluka, kuti chimwemwe chathu chikadzadze.Ife tikupempha izi muDzina la Yesu. Ameni.

Inu mukhoza kukhala pansi.20 Ngati ine ndiyenera kuwutchula uwu mutu, kwa mphindipang’ono. Mawu anga ndi ofooka, kotero ndicho chifukwaine ndiyenera kuima pa cholankhulira. Ine ndikudziwa kutimawu akuphokosera, koma ife tipirira pang’ono zimenezo. Inendikufuna kuwutcha iwo:Kutenga Chipata ChaMdani PambuyoPa Yesero.21 Chochitika chathu chikutseguka pa chimodzi cha zochitikazopambana kwambiri kwa Abrahamu. Inu mukudziwakuti Abrahamu ndi atate wa okhulupirika. Ndipo lonjezolinapangidwa kwa Abrahamu. Ndipo kungokhala olandiralimodzi nawo ndi iye, kudzera mwa Khristu, ndi njira yokhayoimene ife timalandirira lonjezo, kudzera mwa Abrahamu.Tsopano, Abrahamu anali munthu wamba chabe, koma iyeanaitanidwa ndi Mulungu ndipo iye anali wokhulupirika kwakuitana kumeneko. Pamene Mulungu analankhula ndi iye,Abrahamu palibe nthawi imodzi imene anakaikirapo Liwu

Page 4: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

4 MAWU OLANKHULIDWA

limenelo. Iye anakhala nalo kumene Ilo. Ziribe kanthu kutimavuto anali chiyani, iye anakhalabe ndi Ilo.22 Ndipo kenako iye analonjezedwa mwana. Ndipo iyeanayembekezera zaka twente faivi kuti adzalandire mwanaameneyo, amachitcha chirichonse chimene chinali chotsutsanandi icho ngati kuti panalibepo. Ndiyeno, ndipo mwa mwanauyu, mabanja onse a padziko lapansi anali oti adzadalitsidwa.Ndipo mbadwayo inali yokhulupirika ku kuitana kwake ndiMawu olonjezedwa.23 Iye anali chitsanzo cha chimene ife tiyenera kukhala.Tsopano ife, pokhala akufa mwa Khristu, ife timadzakhalaMbewu ya Abrahamu.24 Tsopano, panali mbewu ziwiri za Abrahamu. Imodzi ya iyoinali yachirengedwe; inayo inali Mbewu yauzimu. Imodzi ya iyoinali yachirengedwe, mwa thupi lake; imodzi inayo inali Mbewuya chikhulupiriro chake, chikhulupiriro, kuti nafenso tidzathekukhalaMbewu yaAbrahamumwaMawu olonjezedwa.25 Ndipo tsopano atatha kuyesedwa kwa zaka twentefaivi zazitali, ndipo, mmalo moti azifooka, iye amakhalawamphamvu. Mwaona, ngati izo sizinachitike chaka choyamba,chaka chotsatira chikanadzakhala chozizwitsa chachikulu,chifukwa icho chinali usinkhu wa zaka ziwiri. Ndipo iye analiakuzisanjikiza zaka zimenezo, pamene iye anali kukalamba,ndipo thupi lake linafa. Ziberekero za Sarah, chiberekero,kapena icho (chinakhala) chinali chosabala. Ndipo choteromphamvu yake inali itatha, ndipo apo panali…Ndi zosathekandithudi.26 Kodi inu munayamba mwalingalirapo zimene Mulunguanachita kumeneko? Mwaona, Iye sanangopanga chiberekerochake chikhale ndi chonde. Pakuti, kumbukirani, ngati Iyeakanachita zimenezo, ndiye kumbukirani ngati Iye akanachitazimenezo…iwo analibe mabotolo athanzi ndi aukhondo,mmasiku amenewo, omuyamwitsira mwanayo, mkaka wang’ombe. Mukuona? Iye analinso ndi…Mitsempha yake yamkaka inali itauma. Kotero Iye—Iye sakanatha…Pankayenerakuchitika chinachake.27 Ndiye, tamuwonani mkazi, wausinkhu wa zaka zana, kupitamu kubala. Mtima wake sibwenzi utapirira nazo zimenezo.Zikumakhala zovuta tsopano kuti mkazi, wausinkhu wa zakaforte, kuti achite zimenezo. Mtima wake sibwenzi utapirira nazozimenezo. Kotero inu mukudziwa chimene Iye anachita? Ngatiinu mungazindikire…28 Tsopano ine ndikudziwa ambiri akhoza kutsutsa. Ngatiizi ziri zolondola kuti ndipange neno ili? Mwaona, ine…Ikokukhoza kungokhala kuganiza kwanga kwanga.29 Mwaona, Baibulo ndi Bukhu lauzimu. Ilo linalembedwa kutilibisidwe kwa masukulu, azamulungu. Ndi angati amadziwa

Page 5: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 5

zimenezo? Yesu anamuthokoza Mulungu. Iye anati, “Inendikukuthokozani Inu, Atate, Inu munazibisa Izo kwa anzerundi aluntha, ndipo mwaziulula Izo kwa makanda ameneangaphunzire.” Ilo ndi Bukhu la chikondi. Pamene chikondi chaMulungu chibwera mu mtima, ndiye iwe umagwa mchikondindi Mulungu, kenako Iye amadziulula Yekha, kutanthauza kwaBaibulo. Kutanthauzira kwa Baibulo ndi Mulungu Mwiniwakekutanthauzira malonjezo Ake. Koma, Baibulo, Ilo linalembedwapakati pa mzere.30 Tsopano, monga mkazi wanga, o, iye ndi mkazi wodabwitsakwambiri mu dziko lonse, ndipo ine ndimankonda kwenikweniiye. Iye amandikonda ine. Kotero ine ndikachokapo pakhomo,iye amandilembera ine kalata, kuti, “Wokondedwa Bill,usikuuno ine ndawagoneka kumene ana. Ine ndachapa lero,” ndizonse zimene iye wachita, ndi zina zotero. Tsopano iye akunenazimenezo mkalata. Koma, inu mukuona, ine ndimamukonda iyekwambiri, ndipo ndife mochuluka kwambiri mmodzi, mpakaine—ine ndimatha kuwerenga pakati pa mizere. Ine ndimadziwachimene iye akufuna kunena, mwaona, ngati iye akundiuza inezimenezo kapena ayi, mwaona. Ine—ine ndimadziwa chimeneiye akutanthauza, chifukwa ndi chikondi changa kwa iye, ndikumvetsa kwanga.31 Chabwino, umo ndi mmene Baibulo linalembedwera.Mukuona? Ma—maphunziro amapita pamwamba pa izo; iwosangazimvetse nkomwe zimenezo. Mwaona, iwe umayenerakukhala mu chikondi ndi Mawu, Iye, “kumudziwa Iye.”Mukuona?32 Tsopano, tsopano apa, penyani zimene Iye anachitakwambiri. Tsopano Abrahamu ndi Sarah onse anali atakula,“atakalamba,” Baibulo linatero. Tsopano izo sizinangokhalabasi chifukwa iwo anali anthu amene anakhala nthawi yaitalikumeneko. Baibulo linanena kuti, “Iwo anali okalambakwambiri mu usinkhu.”33 Tsopano zindikirani, mwamsanga Mngelo uyu atawonekera,ife takhala tikumukamba; amene anali Elohim, Mulungu. NdipoIye anati, anamuuza Abrahamu, “Ine ndidzakuchezera iwemolingana ndi nthawi ya moyo.” Tsopano penyani mmusi monsekudutsa, iwo anali choimira chaMpingo, kudutsa njira yonse.34 Tsopano penyani. Ndi ichi chimene chinachitika. Tsopano,Iye sikuti anangomukonza Sarah, ndi kumukonza Abrahamu.Iye anawasandutsa iwo kukhala mnyamata ndi msungwana.Tsopano izo zikhoza kuwoneka zachirendo, koma tsopanopenyani Mawu onsewo, ndipo muwaike iwo pamodzi. Mawundi odzozedwa, ndipo iwe uyenera kukhala wodzozedwandi Mawu. Tsopano, kumbukirani, mwamsanga zitachitikazimenezo, mwamsanga pambuyo pa kuwonekera kwa Mngelouyu…

Page 6: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

6 MAWU OLANKHULIDWA

35 Ine ndikukhoza kuwona zimenezo, tsitsi la imvi lija laSarah, gogo wamkazi wamng’ono ali ndi shawelo pa phewalake, ndi chotolera fumbi chaching’ono, atagwirizira ndodo,akuyendayenda. “Ine, kukhala ndi chisangalalo ndi mbuyewanga, ndipo iye wokalamba, nayenso?” Mukuona? Ndipo apapanali Abrahamu, ndevu zazitali izi, atagwirizira ndodo, pakutiiye anali, wokalamba kwambiri mu usinkhu.36 Ndipo ine ndikuwona, mmawa wotsatira, mapewa akeanayamba kuwongoka, nsana wake unawongoka. Tsitsilake linayamba kusandulika. Iwo anabwereranso kukakhalamnyamata ndi mtsikana. Basi kungosonyeza chimene Iye atiadzachite kwa Mbewu Yachifumu ya Abrahamu, mwaona,pamene ife titi “tidzasinthidwe mkamphindi, mu kuthwanimakwa diso, ndi kudzatengedwerammwamba limodzi.”37 Penyani zimene zinachitika. Tsopano mundirole inenditsimikizire izi kwa inu. Tsopano iwo anatenga ulendokuchokera pa malo awo amene iwo analipo, uko ku Gomora;ndipo anapita njira yonse mpaka ku Gerar, kutsikira ku dzikola Filisiti. Kodi inu munazindikira? Mukajambule izo pa mapu,kuti ndi kutali chotani. Unali ulendo ndithu kwa banja lausinkhu umenewo.38 Ndiyeno, pambali pa zimenezo, mu—mu dziko la Afilistikumeneko, uko kunali mfumu yaing’ono dzina lake Abimeleki,ndipo iye amafunafuna mkazi. Ndipo iye anali ndi atsikanaonse Achifilisti okongola awo, koma pamene iye anamuwonamgogo, iye anati, “Iye ndi wowoneka bwino,” ndipo iye anagwamchikondi ndi iye ndipo ankafuna kuti amukwatire iye. Ukonkulondola. Uh-huh.Mwaona, iye anali wokongola.Mukuona?39 Iye anali atasanduka kukhala mtsikana. Zindikirani, iyeankayenera kutero, kuti abale mwana ameneyo. Mulunguanamupanga iye kukhala cholengedwa chatsopano. Ndipoiye ankayenera kutero, kuti adzamulere mwana uyu. Ndipokumbukirani, Abrahamu, “thupi lake basi ngati lakufa,” ndipoSarah anafa pamene Abrahamu anali…Isaki anali usinkhu wazaka forte faivi, ine ndikukhulupirira, pamene Sarah ankafa.Ndipo Abrahamu anakwatira mkazi wina ndipo anaberekanaye ana aamuna seveni pambali pa ana aakazi, pambuyo pazimenezo. Ameni.40 Mwaona, muwerenge pakati pa mizere. Icho ndi choimira.Zikusonyeza pamenepo zimene Iye ati adzachite kwa Anaonse a Abrahamu. Basi ife tikuyandikira izo pakali pano,kotero mapewa athu akugwa ndi chirichonse sizipanga kusiyanakulikonse, abwenzi. Ndipo tsitsi lathu la imvi ndi chirichonse,ziribe ntchito tsopano. Ife sitimayang’ana mmbuyo. Tiyenitiziyang’anamtsogolo kwa chimene ife tikufikako.41 Ndipo kumbukirani, chizindikiro ichi chimene ifetikuchiwona, chinali chizindikiro chotsiriza chimene Abrahamu

Page 7: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 7

ndi Sarah wake anachiwona, mwana wolonjezedwayo asanafikepowonekera. Ife tikukhulupirira kuti ife tiri pa ora limenelo.42 Mbadwa, zitachitika kuti mwana uyu wabadwa…Kodiinu mungaganize Isaki, wa pafupi usinkhu wa zaka thwelofu;mnyamata wamng’ono wokondedwa, wa tsitsi la mzindo, masoaang’ono a bulauni? Ine ndikutha kuganiza mmene mayi uyoanamvererera; mtsikana wamng’ono wokongola, ndipo kotero,ndipo bambo ake. Ndipo tsiku lina, Mulungu anati, tsopano,mwachitsanzo; ife tatalikira kwambiri, ora liri nkudza. “Inendakupanga iwe kukhala atatewamafuko, kudzeramwamwanauyu, koma Ine ndikufuna kuti iwe umutenge mwana uyu upitenaye pamwamba pa phiri limene Ine nditi ndidzakusonyeze iwe,ndipo ine ndikufuna kuti iwe ukamuphe iye, ngati nsembe.”Kodiinu mungaganizire zimenezo?43 Tsopano inu simunayambe mwafunsidwapo kuti mupite kumayeso monga choncho. Iye sakuchita zimenezo tsopano. Izozinali zitsanzo, mithunzi.44 Kodi Abrahamu anachita mantha? Ayi, bwana. Abrahamuananena izi, “Ndine wokakamizidwa kwathunthu kuti Iye ndiwokhoza kumudzutsa iye kuchokera kwa akufa, pakuti inendinamulandira iye ngati wina wochokera kwa akufa. Ndipongati lamulo laMulungu ilo landiuza kuti ndichite ichi, ndipo inendakhala moona kwa icho, ndipo zinalipira, kuti anandipatsaine mwana; Mulungu ndi wokhoza kumudzutsa iye kuchokerakwa akufa; kuchokera kumene ine ndinamulandira iye, ngatichoimira.”45 O, mai, mzanga! Ngati Mulungu anakupatsani inuAchipentekoste Mzimu Woyera, kulankhula mmalirime,ndi mochuluka bwanji muyenera inu kuti muzikhulupiriramphamvu Yake yochiritsa, ndi ubwino Wake ndi chifundo!Ngati Iye anachita zimenezo, motsutsana ndi azamulungu onsemu dziko! Iwo anati izo sizingachitike, koma Mulungu anachitaizo chifukwa Iye analonjeza izo. Ndiye muziima ndi Mfuti yanu,Mawu anu, Lupanga lanu, mukhulupirire Mawu a Mulungu.Mulungu ananena choncho, ndipo izo zikukhazikitsa zimenezo!46 Zindikirani, tsopano, iye anamutengera iye ulendowa masiku atatu kuchokera kumeneko, ali ndi abulu.Tsopano ine ndimatha kuyenda, pamene ine ndinalikolondera, ine ndinkayenda mamailosi sate tsiku lirilonse,kudutsa mnkhalango; ndipo ife tinali ndi mapazi a mafuta,mwakulankhula. Koma amuna amenewo, njira yawo yokhayoya mayendedwe, inali kapena kukwera bulu kapena—kapenakuyenda. Ndipo iye anayenda ulendo wa masiku atatukuchokera kumene iye anali, ndipo kenako anadzutsa maso ake,kuyang’anamnkhalango, ndipo anawona phiri patali.47 Iye anamutenga Isaki ndipo anamanga manja ake. Chimene,ife tonse tikudziwa, mu Genesis 22 apa, ndi choimira cha

Page 8: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

8 MAWU OLANKHULIDWA

Khristu. Anamutsogolera iye ku phiri, atamumanga, mongaYesu anatsogoleredwa ku phiri, Phiri la Kalvare; choimira chaMulungu akumperekaMwanaWake, zoona.48 Koma pamene iwo anakafika pamwamba apo, ndipo iyeanali womvera, Isaki anayamba kukhala ngati wodabwa. Iyeanati, “Bambo, nkhuni ndi izi, guwa ndi ili, moto ndi uwu, komansembe yake ili kuti?”49 Ndipo Abrahamu, akudziwa mu mtima mwake, komabeMawu a Mulungu ataima kumeneko, iye anati, “Mwanawanga, Mulungu ndi wokhoza kudzipatsa Yekha nsembe.” Iyeanawatcha malowo, “Yehova-Yire.”50 Ndipo pamene anamumanga mwana wake, iye analiwomvera mpaka ku imfa; anamugoneka iye paguwa, anasololampeni kuchokeramchimake, ndipo anayamba kuti achotsemoyowa mwana wake wamwamuna. Ndipo, pamene iye anatero,Chinachake chinagwira dzanja lake, ndipo anati, “Abrahamu,letsa dzanja lako.”51 Ndipo pa nthawi imeneyo, nkhosa inaphupha, kumbuyokwake, ili ndi nyanga zake zitakodwamu ziyangoyango.52 Kodi inu munayamba mwaganizirapo, kodi nkhosaimeneyo inachokera kuti? Kumbukirani, dzikolo ndi lodzadzandi mikango ndi mimbulu ndi ankhandwe, ndi nyamazolikhwira nkhosa izo. Ndipo iye anali atatalikirana bwanjindi chitukukuko? Ndipo, ndiye, pamwamba pa phiri, kumenekulibeko madzi. Ndipo iye anali atatola miyala, pozunguliraponse, kuti amange guwa. Kodi nkhosa imeneyo inachokerakuti? Mukuona?53 Koma awo sanali masomphenya. Iye anaipha nkhosayo; iyoinali ndi magazi. Kodi iye ananena chiyani? “Mulungu ndiwokhoza kudzipatsa Yekha nsembe.”54 Kodi inu muchokamo bwanji mu mpando umenewo? Kodimwana wa khunyu uyo akhala bwino chotani, kapena inukudzuka pa mpando umenewo, inu kuchoka pamenepo, inu ndivuto lamtima? Lirilonse limene liri vuto, “Mulungu ndi wokhozakudzipatsa Yekha.”55 Abrahamu anakhulupirira izo. Mbadwayo inakhala moonaku lonjezolo. Ndipo Iye anapereka lonjezo, lakuti, “Mbewu yako!Chifukwa iwe wakhulupirira Mawu Anga, ndipo mosalabadirazochitikazo,mbewu yako idzatenga chipata chamdaniwake.”56 Bwanji? Mdani aliyense amene amabwera, ngati choimira,kudzamenyana ndi Abrahamu, Abra-…Mdani wa, “Iye ndiwokalamba kwambiri. Ndine wokalamba kwambiri. Zonse izi,ndi china chirichonse.” Iye anakhalabe moona kwa lonjezolimenelo.57 Tsopano, munthu amene amakhala ndi chikhulupirirochimenecho, adzawatengabe Mawu a Mulungu mosalabadira

Page 9: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 9

zochitikazo. Tsopano, ngati inu simungathe kuchita zimenezo,ndiye kuti sindinu Mbewu ya Abrahamu. Ndicho chikhulupirirochimene Abrahamu anali nacho, Mbewu yake.58 Lonjezo la Abrahamu linali lakuti yake “Mbewu,” tsopanoMbewu yake yachifumu, aponso, monga ine ndinakuuzaniinu kanthawi kapitako. Ndipo chisindikizo ichi chimeneIye anamupatsa Abrahamu, chinali chisindikizo cha lonjezo.Ndipo Mbewu yachifumu, malingana ndi Aefeso 4:30, ili“kusindikizidwa ndi Mzimu Woyera,” pambuyo pakuima ndiyesero. Kuyesera kuganizira za izo.59 Ambiri amaganiza kuti iwo ali nawo MzimuWoyera. Ambiriamadzinenera kuti ali nawo Mzimu Woyera. Ambiri akhozakusonyeza maumboni ochuluka ndi zizindikiro za izo. Komabe,apo, ngati iwo sangathe kukhala ndi Mawu awa, iwo si MzimuWoyera. Mukuona?60 Iwe ukakhulupirira Mawu aliwonse, ndiye iweumasindikizidwa pambuyo pa yesero. Pamene ife tikhulupiriralonjezo lirilonse mu Mawu, kenako ife timasindikizidwandi Mzimu, kuti akatsimikizire lonjezo. Ndicho chimene,ndi chimene Abrahamu, momwe iye anachitira izo. Ndiye,ndipo ndiye ndi apo pokha, pamene ife timakhala ndi ufuluwotenga chipata cha mdani wathu. Inu simungathe kuchita izompaka poyamba mutakhala Mbewu imeneyo. Kumbukirani, muBaibulo…61 Ine ndinalankhula pa izo, ku Houston kapena kwinakwake,lina…kapena, ine ndikutanthauzaDallas.Chizindikiro.62 Mwaona, m—Myuda akhoza kusonyeza, uko mu Israeli,kuti iye anali Myuda mwa mdulidwe. Koma Mulungu anati,“Pamene Ine ndiwonamagazi! Ndipomagazi adzakhala kwa inuchizindikiro.”63 Moyo umene unali mmagazi sumatha kubwera pawopembedza, chifukwa, chabwino, iwo unali moyo wachinyama, iwo unali kokha mthunzi ukubwera ku Moyoweniweni. Ndiye, madzi, magazi enieniwo, pamayenera kukhalapofiira pa chitseko ndi pa nsanamira ya chitseko.64 Amapakidwa ndi hisope, umene uli udzu wamba chabe,kusonyeza kuti iwe sukusowa kukhala ndi chikhulupiriro chinachapamwamba. Iwe ukungoyenera kukhala ndi chomwecho,chikhulupiriro chimene iwe uli nacho, monga mmene ungaliziregalimoto yako, pobwera ku tchalitchi. Mukuona? Anthu ambiriamaganiza kuti iwo ayenera kuti akhale chinachake…Koma,ayi, ayi, uko nkulakwitsa. Chikhulupiriro wamba chabe ndichochimene iwe uyenera kupakira nachoMagazi. KumvaMawu, ndikuwakhulupiriraMawu, kuwapaka Iwo, ndizo zonse. Kungozulamaudzu paliponsepo uko mu Palestina, anali a hisope, basiudzu pang’ono omera mming’aru ya makoma, ndi pozungulira,

Page 10: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

10 MAWU OLANKHULIDWA

kuviikidwa mmagazi awo ndi kuwapaka iwo pa mphutu ndimmbali mwa zitseko.65 Ndipo, kumbukirani, ine sindikusamala kuti analimochuluka chotani mu phanganolo, mochuluka bwanji Myudaamatha kudziwonetsera kuti iye anali wodulidwa, anali munthuwabwino bwanji iyeyo, phangano lonselo limakhala lopandantchito kupatula—chizindikiro chikhalepo apo. “Pamene inendidzawona magazi,” basi.66 Tsopano, Magazi tsopano, Chizindikiro, si madzi, madzia Magazi a Khristu, chifukwa Iwo anakhetsedwa zaka zikwizapitazo.67 Koma, inu mukuona, pamene…amayenera kukhalamadzi apo, moyo wa chinyama sumatha kubwera pa munthu,chifukwamoyowa chinyama ulibe solo. Chinyama sichimadziwachabwino ndi choipa. Ndimunthu amene ali ndi solo.68 Tsopano, koma pamene Yesu,MwanawaMulungu, wobadwamwa namwali, anakhetsa Magazi Ake, Moyo umene unalim’Magazi amenewo unali Mulungu Mwiniwake. Baibulo linati,“Ife timapulumutsidwa ndi Moyo, Magazi a Mulungu.” Osatimagazi a Myuda, osati magazi a Wamitundu; koma Moyo waMulungu. Mulungu analenga khungu la Magazi ili, wobadwakwa namwali. Iye sanamudziwe konse mwamuna aliyense,komanso iye…komanso dzira silinachokere kwa iye.69 Ine ndikudziwa ambiri a inu anthu mukufuna kukhulupirirakuti dziralo linatero. Dzira silingapezeke pamenepo popandazogirigisha,Mulungu angachitirenji ndiye?Mukuona?70 Iye analenga zonse ziwiri dzira ndi khungu la Magazi, ndipoameneyo anali kachisi wa Mulungu, woyera. “Ine sindidzalolaWoyera Wanga Uyo kuti awone chivundi.” Mukuona kumenedzira likuchokera? “Komanso Ine sindidzasiya solo Yake mugehena.” Thupi Lake linali loyera! O, mai! Iwe suma, inusimungathe kukhulupirira zimenezo, inu mungadzitche nokhabwanji Mkhristu?71 “Ife timapulumutsidwa ndi Magazi a Mulungu.” Ndikumene kuli chikhulupiriro changa. Osati kuyendera kumenekommagazi a mneneri, osati kuyendera kumeneko mmagazi amunthu wamba, kapena mphunzitsi, kapena wazamulungu. Ifetimayenda kupita uko m’Magazi a Mulungu. Mulungu ananenachomwecho. Iye anadzakhala munthu. Iye anasintha malo Ake.Iye anadzafunyulula hema Wake kuno, limodzi nafe, ndipoanadzakhalammodzi wa ife. Iye aliWoombola wathuWachibale.Iye anachita kudzakhala wachibale kwa ife, chifukwa lamulolake linali limenelo. Mulungu anadzakhala munthu ndipoanadzakhala pakati pathu.72 Zindikirani momwe izo ziliri, pochita izi, Iye kubwerakuchokera kwa Iye, anali Mulungu, Mzimu, ndipo Mzimuumenewo umabwera pa wokhulupirira. Chotero, Moyo umene

Page 11: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 11

unali mu Nsembe yathu, ife timazindikiritsidwa ndi Moyowomwe womwewo.73 Ndiye zikutheka bwanji kuti iwo akuwuwona Moyo waMulungu ukuyenderera pakati pa anthu, ndipo nkuwutcha Iwochinthu chosayera, pamene Ndicho chotizindikiritsa chathu chaNsembe yathu? “Iye amene akhulupirira pa Ine, ntchito zimeneIne ndikuchita iyenso azizadzichita.” Moyo Wake kubwererapa nsem-…kuchokera kwa Nsembe, pamene ife tiyika manjaathu pa Iyo ndi kuzidzindikiritsa tokha kuti ndife akufaku malingaliro athu omwe. Ndiye ife tingalolere bwanji kutizipembedzo zizitikankhira ife kuti tikalowe mu tizikhulupirirondi zinthu, ndi kumati ife tikukhulupirira Iwo? Ife tiri akufa kwazinthu zimenezo.74 Paulo anati, “Palibe chirichonse cha zinthu izichimandivutitsa ine,” pakuti iye anali atamangiriridwa kwamtheradi, Khristu. Ndipo chopambana choona chirichonsechimamangirizidwa kwa mtheradi, ndipo mtheradi wanga ndiMawu. Ndi wina aliyenseyo, ndizo—amenewo ndi wobadwakwenikweni ndi Mzimu, mtheradi wawo ndi Mawu aMulungu. Ndine womangiriridwa kwa Iwo. Ine ndinaikamanja anga pa Iwo. Ndipo Iwo anatenga malo anga, ndipoine ndazizindikiritsa ndekha ndi Iye. Ife timadziwa kutiIye analonjeza kuti adzazizindikiritsa Yekha ndi ife. Izozimabweretsa chikhulupiriro chenicheni; osati chikhulupirirochanu chanu, koma chikhulupiriro Chake; chinachake chimeneiwe sungachilamulire. Iye amachita izo. Tsopano zindikirani.Ndiye, ndiyeno chokhacho, pamene…ndi pamene lonjezolimapangidwa kwa iwe.75 Ziribe kanthu kuti mwajowina matchalitchi angati, ndinthawi zingati zimene mwabatizidwa; nkhope cha mtsogolo,cha mmbuyo, mulimonse mmene inu mukufunira. KufikiraChisindikizo chimenecho chitaikidwa pa iwe, ndiye iwesumakhala ndi ufulu womadzitcha wekha kuti walumikizidwandi Nsembe yako.76 Ndipo kodi Chisindikizo cha Mulungu ndi chiyani?Aefeso 4:30, amati, “Musawukwiyitse Mzimu Woyera waMulungu, umene inu munasindikizidwa nawo kufikira Tsikula chiwombolo chanu.” Osati kuchokera ku chitsitsimutsochimodzi kupita kwa china, koma kusindikizidwa Mwamuyayampaka Tsiku limene udzawomboledwenso.77 Ndipo, kumbukirani, ngati inu simunayambe mwakhalapokonse mmaganizo a Mulungu, inu simudzakhala konse ndiMulungu. Ndi angati akudziwa kuti Iye anali Muwomboli?[Osonkhana akuti, “Ameni.”—Mkonzi.] Chabwino, ndiye,chirichonse chowomboledwa chiyenera kubwerera kumene ichochinagwera. Kotero ngati Iye anabwera kuti adzatiwomboleife, zingatheke bwanji ife, nthawi ina tinali osasowa

Page 12: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

12 MAWU OLANKHULIDWA

kuwomboledwa, ndipo ife tonse tinali “obadwa mutchimo, owumbidwa mu kusaeruzika, kubwera ku dzikokumadzalankhula mabodza”? Izo zikusonyeza kuti Mkhristuweniweni amakhala khumbo la maganizo a Mulungu,kusanakhale konse dziko, kapena nyenyezi, kapena mpweya,kapena china chirichonse. Ndi Muyaya, ndipo Iye anabwerakuti adzatiwombolenso ife. Ndiro lingaliro la Mulungu,linalankhulidwa kukhala mawu, ndipo anadzawonetseredwandi ku-…kubweretsedwanso ku lingaliro Lake.78 Wowombola Wachibale! Ndicho chifukwa MulunguMwiniwake anabwera kuti adzakhale mmodzi wa ife, kutiadzawombole. Palibe chirichonse chimene chikanatha kuchitazimenezo. Mngelo sakanatha kuchita izo, kunalibe chirichonse.Iye anachita kutsika pansi, anadzayesedwa monga ife, kutiadzatiwombole ife.79 Zindikirani tsopano mbewu yachirengedwe ya Abrahamu.Tiyeni tifufuze zina za mbewu yachirengedwe izo, ndipo tiwonengati Mulungu anasunga Mawu Ake ndi mbewu yachirengedwe,imene inali Isaki. Tiyeni tifufuze zina za mbewu zachirengedwezimene zinakhulupirira lonjezo lathunthu la Mulungu ndipozinalibe funso. Tsopano kumbukirani, kunali zikwi makumikuchulukitsa nthawi zikwi kuchulukitsidwa amene anadulidwandi china chirichonse, ndipo komabe sanakhale Mbewu yaAbrahamu. Zedi, “Chimene chiri Myuda kunja si Myuda;chimene chiri Myuda mkati.” Iwo, ambiri a iwo, analephera,analephera kwathunthu.80 Taonani, mu chipululu, iwo anati, “Ife…” Tsiku la Paskha,kapena pakumwa pa kasupe, Yohane Woyera 6. Iwo onse analiakusangalala.81 Yesu anati, “Ndine Thanthwe lija limene linali mu chipululu.Ndine Mkate wobwera kuchokera kwa Mulungu, kuchokeraKumwamba, ngati munthu adya iwo sadzafa.”82 Iwo anati, “Makolo athu anadya manna mu chipululu, kwazaka forte.”

Iye anati, “Ndipo iwo, mmodzi aliyense, anafa.”83 Anafa, mutenge mawu amenewo ndipo muwayendetseiwo, muwone chimene iwo akutanthauza, “kulekanitsidwaMwamuyaya.” Komabe, iwo anali mbewu ya Abrahamu. Imfaimatanthauza “kulekanitsidwa, kuthetsedwa, kuwonongedwakwathunthu, kuthetsedwa.” Yesu anati iwo anafa, mmodzialiyense wa iwo, komabe iwo anali Ayuda odulidwa.84 Mwaona, anthu osauka, basi pakuti ndife Amethodisti,Abaptisti, Apresbateria, tinalapa pang’ono, ndi zinthu mongachoncho; mdierekezi amakhulupirira mochuluka basi monga ifetimachitira.

Page 13: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 13

85 Koma inu muyenera kuzindikiritsdwa ndi Iwo. Mulunguayenera kuchitira umboni Iwo kwa izo, pakusindikiza ndiMzimuWoyera. Wopanda kuwakaikiraMawu!86 Ngati inu mukuti, “Chabwino, tsopano, zimenezo zinali zatsiku lina,” pali chinachake cholakwika.87 Bwanji ngati munthu atabwera akuthamanga, ndipo inunkumuuza iye kuti kuwala kukuwala, ndipo iye nkuthamangirapansi, nkuti, “ine basi ndikukukana iko. Ine ndikukukanabasi iko. Kulibeko chinthu chotero ngati kuwala. Inesindikukhulupirira izo”? Pangakhale chinachake cholakwikandi munthu ameneyo. Iye angakhale wosokonezeka mu ubongo.Ngati iye akana kufundira kwake ndi gwero lake lopereka moyo,pali chinachake cholakwika ndi iye, mu ubongo.88 Ndipo pamene munthu awawona Mawu a Mulungu,akuikidwa pa mbalambanda pamaso pake, ndipoakuzindikiritsidwa, ndiyeno nkutsekapo ndipo nkukokera pansimakatani ake achipembedzo, pali chinachake cholakwika ndimunthu ameneyo, mwauzimu. Chinachake ndi cholakwika ndiiye. Pali chinachake cholakwika mwauzimu. Iye akulephera basikuti awalandire Iwo. “Wakhungu, ndipo sakudziwa izo,” akupitaku Chiweruzo, ndipoMulungu adzakhalaWoweruza.89 Zindikirani pamene iwo—iwo anachita izi, ndipo mbewuizi tsopano zimene zinakhulupirira Iwo, muwone zimenezinachitika. Tiyeni tifufuze zina za izo tsopano, mbewu yaAbrahamu.90 Tiyeni titenge ana a Chihebri, chifukwa iwo anaimamowona ndipo samalekerera zopembedza mafano. Iwo anakanakuti agwadire fano limene mfumu ya fukolo inapanga. Ilolinapangidwa mofanana ndi munthu woyera, aponso, fano laDaniele.91 Zimasonyeza kutimtunduwaAmitundu unabweretsedwamopansi pa kumbali yabodza, ya kupembedza fano la munthuwoyera. Iwo udzapitanso mwanjira yomweyo, pamene anthuati azidzakakamizidwa kuti apembedze mafano a anthu.Iwo unabweramo mwa vumbulutso, la Daniele kukhozakutanthauzira Mawu, amene analembedwa pa cholembedwapakhoma. Umo ndi mmene iwo unabwerera, ndipo ndi mmeneiwo uti udzapitire,mwanjira yomweyo, ya fano laWamitundu.92 Zindikirani, iwo anakana kuti achite zimenezo. Ndipo kodiiwo anachita chiyani? Iwo anali mbewu ya Abrahamu ikuimamoona ku Mawu, ndipo iwo anatenga chipata cha mdani, chamoto. Iwo anachita izo. Chabwino,Mawu aMulungu ndi owona.93 Daniele, anayesedwa chifukwa chopembedza Mulungummodzi woona. Iye anayesedwa chifukwa cha zimenezo. Ndipomu nthawi ya kuyesedwako, iye anapirira yesero. Ndipo kodiMulungu anachita chiyani, zitatha kuwoneka ngati zibanthuzochokera mwa iyeyo, monga mmene ife tinganenere? Ndipo iwo

Page 14: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

14 MAWU OLANKHULIDWA

sanadziwe kuti achite chiyani. Iwo anali woti akamudyetsa iyekwa mkango. Koma Daniele anakhala woona ku yesero, kutialipo Mulungu mmodzi woona, ndipo iye anatenga chipata chamdani wake. Mulungu anatseka kamwa lamkango.94 Mose anakhala moona kwa Mawu olonjezedwa, pamasopa otsanzira abodza, Ayane ndi Ayambre, mu yesero. Taonani,Mulungu anali atakomana naye iye, ndi chauzimu, anamuuzaiye kuti apite akachite zinthu izi, akasonyeze zizindikiroizi, ndipo chizindikiro chirichonse chikanadzakhala ndiliwu. Mose anatsikira kumeneko, moona basi monga mmeneiye amadziwira. Iye anaponyera pansi ndodo, ndipo iyoinasandulika njoka. Inu mukudziwa chimene chinachitika? Apapanabwera otsanzira ndipo anadzachita chinthu chomwecho.95 Tsopano, Mose sanaponyere mmwamba manja ake, kuti,“Chabwino, ine ndikuganiza zonsezo ndi zolakwika.” Iyeanakhala pamenepo ndipo anayembekezera pa Mulungu. Iyeanakhala moona. Zinalibe kanthu panali otsanzira angatipamenepo, iye anakhala moona. Ndipo pamene iye anakhalamoona ku kutuma kwake, kuti akawatulutse anthu amenewokuchokera ku dziko limenelo, pamene chipata cha madzichinaima panjira yake, Mulungu anamulola iye kuchitengaicho, ndipo iye anatsegula chipata ndi Lawi la Moto limenelinkamutsogolera iye. Iye anawatengera anthu mpaka wakudziko lolonjezedwa.96 Yoswa, mtsogoleri wina wamphamvu. Awiri okha mwa…anapita ku dziko lolonjezedwa, Yoswa ndi Kalebu. Iwo anafikapamalo otchedwa Kadeshi, amene anali pa mchombo pa dzikopa nthawi imeneyo, mochuluka kuti amenewo anali mpandowachiweruzo. Ndipo, o, iwo anatumiza azondi thwelofu kutiakalizonde dzikolo, ndipo thwelofu a iwo anabwererako.97 Teni a iwo anati, “O, ndi ntchito yaikulu kwambiri. Ifesitingathe basi kukaichita iyo. Chabwino, anthu amenewo, ifetikuwoneka ngati ziwala pambali pa iwo.”98 Koma kodi Yoswa anachita chiyani? Iye anawakhalitsabata anthuwo. Iye anati, “Dikirani miniti. Ife tiri oposakulitenga ilo, ziribe kanthu kaya ndife aang’ono chotani, kapenandife ochuluka bwanji mu kuchepa.” Kodi iye anali kuchitachiyani? Iye anali kuima moona kwa lonjezo limenelo, “Inendikukupatsani inu dziko ili,” koma inu mumenyere inchesiiliyonse ya ilo.99 Kodi inu mukukhulupirira zimenezo, amayi? Mulunguwakupatsani inu machiritso anu, koma inu mumenyera inchesiiliyonse ya iwo. “Paliponse pamene mapazi anu adzapondapo,pamenepo Ine ndakupatsani inu kuti mutengepo.” Mapaziamatanthauza “kutenga.” Zonsezo ndi zanu, lonjezo lirilonsendi la inu, koma inu mudzamenyera inchesi iliyonse ya njirayotsopano.

Page 15: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 15

100 Tsopano, Yoswa ankadziwa zimene Mulungu ananena.Iye anali mbewu ya Abrahamu. Mukuona? Iye anati, “Inendikukhulupirira zimenezo, kuti Mulungu anatipatsa ifedzikolo, ndipo ndife oposa agonjetsi kulitenga ilo.” Ndipochifukwa iye anapirira mayesero, motsutsana ndi gulu lonselo laAisraeli, mafuko onse ndi anthu onse analira maliro ndi kufuula.Yoswa anati, “Khalani bata!Mulungu anapanga lonjezo.”101 Ziribe kanthu kuti ndinu wamkulu chotani, ndipookutsutsaniwo ndi ndani, ndipo adokotala akuti chiyani,Mulungu anapereka lonjezo. Ziri kwa Mulungu kuti akachiteizo.102 Kodi iye anachita chiyani? Pamene iye anadzafika kumtsinjewa Yorodani, iye anatenga chipata. Ndicho chimene iye—iyeanachita.103 Yeriko, anadzitseka ngati kamba mu chigoba. Kodi iyeanachita chiyani? Iye anatenga chipata.104 Ngakhale tsiku lina pamene mdani wake anali kuyesera kutiamutenge iye, iye anatenga chipata chamdani wakemwakuti iyeanaliramulira dzuwa kuti liime nji. Ndipo dzuwa linamumveraiye, ndipo silinasunthe kwamaora twente foro.105 Mulungu ndi woona kwa lonjezo Lake, ziribe kanthu kutiIye ayenera kuchita chiyani; kupangitsa Miyamba kushota Iyeasanapangitse Mawu Ake kuti agonjetsedwe. Iye sanapangekonse lonjezo limene Iye sangathe kulisunga. “Ndine Ambuyendimachiza matenda anu onse. Ngati iwo adzaika manja paodwala, iwo adzachira.” Ameni. “Ngati inu mukhulupirira,zinthu zonse ndi zotheka.”106 Yoswa anakhulupirira izo, ngakhale Mulungu anachitakuimitsa dziko kuti lisazungulire. Analigwira ilo pamenepondi Mphamvu inayake, mphamvu Yake Yomwe; mwakutidziko silinazungulire kwa maora twente foro, mpaka Yoswaanabwezera yekha mdani wake. Iye anatenga zipata. Ndithudi,iye anatero. Mulungu ndi woona nthawizonse.107 Tsopano ine ndikukhumba ife tikadakhala ndi nthawi kutitifike kwa ngwazi zina, koma ine ndatsala ndi pafupifupimaminiti teni tsopano. Taonani, ngwazi zonse zofunika izi,monga iwo anali, ndipo ankhondo amphamvu a chikhulupiriro,iwo onse anafa pa chipata cha imfa. Iwo onse anafera, pa chipatapomwe cha imfa.108 Kenako panadzabwera Mbewu Yachifumu ya Abrahamu.Iwo onse anali mbewu yachirengedwe, kuchokera kwa Isaki.Koma apa panabwera Mbewu Yachifumu ya Abrahamu, ameneanali Khristu, Mbewu ya Abrahamu ya chikhulupiriro; chimeneife tikuyenera kukhala, tangowonani ngati ife tiri kapenaayi. Mbewu yachirengedwe inali kokha choimira. Ena onsewoamabadwa mwa kubadwa kwachirengedwe, koma Iye anabweramwa kubadwa kwa namwali. Mwaona, ameneyo sanali wa

Page 16: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

16 MAWU OLANKHULIDWA

mbewu ya Abrahamu, pamenepo, Myuda. Iye anabwera mwambewu ya chikhulupiriro cha lonjezo. Ndipo, ndiye, ife tiyenerakukhala ana Ake, kudzera mwaMunthu uyu.109 Penyani zimene Iye anachita. Pamene Iye anali pa dzikolapansi, Iye anagonjetsa ndipo anatenga chipata chirichonsechimene mdani anali nacho; Mbewu Yachifumu. Iye analonjezaizo mwa Mawu. Iye anagonjetsa icho. Iye anatigonjetsera ifechipata, cha matenda. Ndicho chimene Iye anabwera kutiadzachite. Iye, mukumbukire, anthu odwala, Iye anagonjetsachipata chimenecho. Inu simukusowa kuti muchigonjetseicho; Iye anachigonjetsa icho. Amuna enawo ankagonjetsachipata chawo. Koma inu simukusowa kuti mugonjetse; ichochinagonjetsedwa kale. Iye anagonjetsa zipata za matenda.Ndipo kodi Iye anachita chiyani pamene Iye anagonjetsa zipataza matenda? Kunena kuti Iye akanadza…Chirichonse chimeneinu mudzapempha pa dziko lapansi, ndi chirichonse chimeneinu mudzachimanga pa dziko lapansi, Iye adzachimanga ichoKumwamba, anatipatsa ife mafungulo aku chipata.110 Iye anagonjetsa chipata cha mayesero, ndi Mawu. Ndipomafungulowo anali, “Mukanize mdani, ndipo iye adzathawakwa iwe.” Iye anagonjetsa izo zonse; anagonjetsa nthendailiyonse.111 Iye anagonjetsa imfa, ndipo Iye anagonjetsa gehena.Iye anagonjetsa imfa ndi gehena. Iye anagonjetsa zimeneena sakanatha kugonjetsa, chifukwa iwo ndi a mbewuyachirengedwe. Iyi ndi Mbewu yauzimu. Iye anagonjetsachipata cha manda, ndipo anawuka pa tsiku lachitatu, kwakulungamitsidwa kwathu.112 “Ndipo tsopano ife tiri oposa agonjetsi.” Ife tikhozakungoyenda kulowa mmenemo, ngati cholandira, “Oposaagonjetsi.” Tsopano ife tikuchita ndi mdani wogonjetsedwa.Matenda anagonjetsedwa. Imfa inagonjetsedwa. Gehenainagonjetsedwa. Chirichonse chinagonjetsedwa. O, mai!Ndikukhumba ine ndikanakhala pawiri usinkhuwanga, tsopanomwinamwake ine ndikumverera ubwino pawiri. Ife tikukanganandi mdani wogonjetsedwa.113 Nzosadabwitsa Paulo anakhoza kunena, pamene iwoankamanga malo, oti adulirepo mutu wake, iye anati, “Oimfa, mbola yako ili kuti? Undisonyeze ine pamene iweungandipangire ine kukhala ndi manjenje ndi kumafuula.Manda, kodi chigonjetso chako chiri kuti, ndipo iwe ukuganizakuti iwe ukandiwumbira ine kumeneko? Ine ndikulozera iwekwa apululu awo kumeneko; ndipo ine ndiri mwa Iyeyo, Iyeadzandidzutsa ine pa tsiku lotsiriza.”Mdaniwogonjetsedwa!114 Mbewu Yachifumu ya Abrahamu! Tsopano, mbewuyachirengedwe siikanakhoza kuloza Kumeneko. Koma MbewuYachifumu ikhoza kugonjetsa, inagonjetsa kale, pakuti Iye

Page 17: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 17

anatsogola kupita ndipo anatigonjetsera ife chipata chirichonse.Iye ali tsopano, patapita zaka zikwi ziwiri, Iye akuima pakatipathu, Mgonjetsi wamphamvu. Sikuti anangogonjetsa matendaokha…Iye anagonjetsa matenda. Iye anagonjetsa mayesero.Iye anamgonjetsa mdani aliyense. Iye anagonjetsa imfa. Iyeanagonjetsa gehena. Iye anagonjetsa manda, ndipo anaukakachiwiri. Ndipo zaka zikwi ziwiri mtsogolo, apa Iye akuimapakati pathu, madzulo ano, akuzidzindikiritsa Yekha, Mgonjetsiwamphamvu! Ameni. Iye akadali pano, wamoyo, akutsimikiziralonjezo Lake, Mbewu Yachifumu ya Abrahamu! O, mai! Ndipomdani adza…115 “Iye adzagonjetsa zipata za mdani wake.” Kwa iwowo,Mbewu, Iye akuima pano wamoyo kuti akazizindikiritse Yekhakwa ndani? Mbewu zokonzedweratu izo zimene zingathekuziwona izo. Iye anagonjetsa zimenezo. Amene, pambuyo pakuyesedwa kwawo, pa lonjezo laMawu, iwo anasindikizidwa ndiMzimu Woyera, kuti akalowe mu Thupi la Khristu, kwa iwowokwatsimikiziridwa (chiyani?) Ahebri 13:8 kuti ali chomwecho.Iwo amakasindikizidwa mmenemo ndi Mzimu Woyera, MzimuWoyera uwo umene unali mwa…Abrahamu anaziwoneratu izo;mwa chikhulupiriro iye anakhulupirira izo. Ndipo tsopano ifetikulandira Iwo, tikuyang’ana mmbuyo kwa lonjezo la chimeneIye ananena. Ndipo Yohane 14:12 akutsimikiziridwa mmasikuotsiriza ano, mwaMgonjetsi wowuka,Mwiniwake.116 Osati kachitidwe kena; koma Munthu, Khristu, Mgonjetsi.Osati mpingo wanga, osati mpingo wanga wa Baptisti, kapenawa Presbateria wanu, Methodisti, kapena wa Pentekoste, osatimwa zimenezo; komamwaYesuKhristu. Iye akukhalamoyo lero.Iye anawuka pa zimenezo, kwa kulungamitsidwa kwathu.117 Ndipo chifukwa Iye ali moyo, Iye anati nafenso tidzakhalamoyo. “Munthu sakhala moyo ndi mkate wokha, koma ndiMawu onse,” osati gawo la Mawu, “Mawu onse otulukakuchokera mkamwa mwa Mulungu.” “Ndine Chiukitsiro ndiMoyo. Iye amene akhulupirira pa Ine, ngakhale iye anali wakufa,komabe iye adzakhala moyo. Yense yemwe akhala moyo ndiponakhulupirira pa Ine sadzafa konse. Kodi inu mukukhulupiriraizi?” Kutenga chipata cha mdani aliyense!118 Kodi iye angathe bwanji kumugonjetsa Bosworth, pameneMulungu…Bosworth anali mwa Mgonjetsiyo. Ndipo ndichochifukwa iye anati, “Ora lokondwetsetsa la moyo wangandi pakali pano.” Uh-huh. Iye ankamudziwa MgonjetsiWamphamvu ameneyo. Chitsimikiziro chake chinali mwa Iyeyo.O, mai! Tsopano ife tikhoza kuimba:

Pokhala moyo, Iye anandikonda ine; pakufa,anandipulumutsa ine;

Poikidwa mmanda, Iye anandinyamuliramachimo anga kutali;

Page 18: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

18 MAWU OLANKHULIDWA

Powuka, Iye anandilungamitsa mwaulerekwanthawizonse;

Tsiku lina Iye akubwera, O tsikulaulemelerolo!

119 Kwa iwo amene ankawoneka ngati agonjetsedwa. EddyPerronet, ine ndikukhulupirira anali, iye ankalephera kutiagulitse nyimbo zake Zachikhristu. Palibe amene ankazifunaizo. Iwo analibe kanthu kochita nazo izo. O, kugonjetsedwa,chikhalirenicho wokhulupirira! Tsiku lina, Mzimu Woyeraunabwera pa iye. Chipata cha mdani wake, chimene amalepherakuti atenge zolemba zake! Mzimu unamukhudza iye, ndipoanatola cholembera, Mulungu anamulola iye kuti alembenyimbo yotsegulira.

Onse yamikani mphamvu ya Dzina la Yesu!Lolani Angelo agwe modzilambatitsa;Bweretsanipo nduwira yachifumu,Ndi kumuveka Iye akhale Ambuye wa onse.

120 Fanny Crosby wakhungu, nthawi ina. Anati, “Kodi izozikutanthauza chiyani kwa inu?” Ena…Iye sanagulitsemaufulu ake akubadwa monga Elvis Presley wa Chipentekosteanachitira, kapena monga a Boone a church of Christ anachitira,kapena monga Red Foley anachitira, kugulitsa luntha lawo kwadziko; iwo ali ndi mdipiti wa ma Cadillac, ndi madola millioni,zimbale za nyimbo za golide. Koma Fanny Crosby anakhalamoona pa malo ake. Iye anakuwa:

Msandipitirire, O Mpulumutsi,Imvani kulira kwanga;Pamene Inu mukuitana ena,Msandipitirire ine.

Ndinu Mtsinje wa chitonthozo changa chonse,Woposa moyo kwa ine,Ndiri ndi ndaninso pa dziko pambali pa Inu?Kapena ndani Kumwamba koma Inu?

121 Iwo anati, “Nanga bwanji ngati inu mudzakhala wakhungumukamadzafika Kumwamba?”

Anati, “Ine ndidzamudziwa Iye, mulimonse.”

Anati, “Mudzamudziwa chotani Iye?”

Anati, “Ine ndidzamudziwa Iye.”

Anati, “Akazi a Crosby, inu mukhoza kupanga mamilioni amadola.”

Iye anati, “Ine sindikufunamamilioni amadola.”122 “Inumudzamudziwa chotani Iye?” Iye anati:

Page 19: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 19

Ine ndidzamdziwa Iye, ndidzamdziwa Iye,Powomboledwera kumbali Yake Inendidzaima;

Ine ndidzamdziwa Iye, ndidzamdziwa Iye.123 “Ngati ine sindidzatha kumuwona Iye, ine ndidzakhudzazipsyera zamsomali mdzanja Lake.” Iye anagonjetsa chipata chamdani wake. Inde.124 Ngati inu muli mwa Khristu! Iye anati, “Ngati inumukhala mwa Ine, ndi Mawu Anga mwa inu; mupemphefungulo limene inu mukufuna, mupemphe chipata chimeneinu mukufuna kuchitenga; mupemphe chimene inu mukufuna,ndipo chidzapatsidwa kwa inu. Ngati inu mukhala mwa Ine, ndiMawu Anga mwa inu, inu mukhoza kutenga chipata cha mdanialiyense amene angabwere kwa inu.” Ndinu Mbewu yachifumuya Abrahamu.125 Kodi pakuima chipata cha mtundu wanji patsogolo panu?Ngati chiri matenda, ndinu woposa mgonjetsi kwa icho. Ndiyeife tikhoza kunena kuti, tiimbe nyimbo yachisomo yakale iyi:

Lonjezo lirilonse mu Bukhu ndi langa,Chaputala chirichonse, ndime iliyonse…ndiZaumulungu kwambiri,

Ndikudalira mu chikondi ChaumulunguChake,

Pakuti lonjezo lirilonse mu Bukhu ndi langa.126 Ndife oposa mgonjetsi, ndipo Mbewu ya Abrahamuidzatenga chipata cha mdani! Pamene iwo akuti Zinthu izisizingathe kuchitika, pamene iwo akufuna kuti adzitche Izomdierekezi, kapena Belezebule, kapena chinachake,Mulungu aliwotsimikiza kuti agonjetsa chipata chirichonse ndi kumutengamdani.

Tiyeni tipemphere.127 Ambuye, mulole Mbewu ya Abrahamu…Ine ndikudziwaiwo awawona Iwo, Ambuye. Mawu amenewo angagwe bwanjiopanda kugunda pa Nthaka yeniyeni iyo? Ine ndikupempherakuti iwo amvetse tsopano. Mulole munthu aliyense amene atiabwere mumzere wa pemphero achiritsidwe.128 Ambuye, ngati alipo ena muno panobe, amene mpakapano sanapangebe chivomerezo chawo, sanaime pagulu ndikumuimira Khristu, okonzeka kuti akane tizikhulupiriro tonsendi kuzizira, kufunda, zinthu zakufa zimene zawatengera iwokutali ndi Inu. Ndipo mulole iwo aime tsopano, ndi kuti,“ine ndimuvomereza Iye ngati Mpulumutsi wanga.” Ndiye Inumudzawaimire iwo pa Tsiku limenelo.129 Pamene ife tiri ndi mitu yathu chiweramire, ngatialipo awo amene akufuna kuti aimirire mphindi chabe,kwa pemphero, anene, “Ine ndikufuna kuti ndimuimire Iye

Page 20: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

20 MAWU OLANKHULIDWA

tsopano, kuti Iye adzandiimire ine pa Tsiku limenelo, muKukhalapo Kwake Kwaumulungu.” Ine ndikukupemphaniinu, ndipo ndikukupatsani inu mwayi wakuti dzina lanulikaikidwe pa Bukhu la Moyo, ngati inu mungaimirire. Inesindikukufunsani inu kuti mudzajowine tchalitchi chirichonse.Ine ndikukufunsani inu kuti mubwere kwa Khristu, ngati inumuli pano ndipo simukumudziwa Iye.130 Mulungu akudalitse iwe, mwana. Kodi alipo wina,nenani, “ine—ine ndikufuna kuti ndiime tsopano.” Mulunguakudalitseni inu, dona. Mulungu akudalitseni inu, mlongowanga. “Ine ndikufuna…”Mulungu akudalitseni inu. Mulunguakudalitseni inu. “Ine nditenga maimidwe anga, madzulo ano.”Anthu abwino awa, amuna ndi akazi, aimirira, “Ine ndiimirira,madzulo ano.”131 Ndipo tsiku limenelo pamene adokotala adzati, “Chabwino,ngozi; magazi ake akuwukha, imfa ili pa iye, kapena pamkaziyo.” Kapena, mmawa wina, inu mudzakumbukira mmenemunkaimira. Inu mumuimire Iye tsopano.132 “Ngati inu mudzandichitira manyazi Ine pamaso pa anthu,Ine ndidzakuchitirani manyazi inu pamaso pa Atate Anga ndiAngelo oyera. Koma ngati inumudzandivomereza Ine pamaso paanthu, ameneyo Ine ndidzamuvomereza pamaso pa Atate Angandi Angelo oyera.”133 Mulungu akudalitseni inu, mlongo wanga. Kodi pangakhalewina mchipinda kwinakwake? Pakali pano, pamene ifetikudikirira. Ena a iwo, ambiri pa chipinda chapansi tsopano?Chabwino. Ine ndikutengani inu pamawu anu,mzanga.134 Ngati Mawu agwera pa Nthaka ya chonde, monga mkaziwamng’ono pa chitsime, iye—iye anamva. Iye anaimiriridwaKumwamba, kuchokera ku mazi-…maziko a dzikoasanakhazikitsidwe. Pamene Kuwala kuja kunaikhudza Iyo,iye anakuzindikira Iko.135 Mulungu akudalitseni inu, m’bale wanga. Kumeneko ndikuchirimika…Mulungu akudalitseni inu, m’bale wanga.Inu mwina munachita zinthu zazikulu mmoyo mwanu; inumukuchita chinthu chachikulu chimene inu munayambamwachitapo, tsopano, mumuimire Khristu.136 Atate athu Akumwamba, mbewu yagwera pa nthaka ina,madzulo ano. Ife tikuwona Moyo ukuthumphukira. Amunandi akazi aimirira kumapazi awo, ndipo diso lowona zonsela Mulungu, Yemwe ali wopezeka ponseponse, wodziwa zonse,wamphamvuzonse, akuwawona iwo. Iwowo ndi Anu, Atate. Inendikuwapereka iwo kwa Inu tsopano, ngati zikho.137 Mulole chowachitikira ichi cha iwo kuima pamenepotsopano, akudziwa chimene iwo achita, akudziwa chimene ichichikutanthauza, kuti iwo aimirira kuti atenge maimidwe awondi onyozeka apang’ono a Ambuye. Mulole iwo nthawizonse

Page 21: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 21

akakhale owona kufikira Tsiku limene iwo adzaime muKukhalapo Kwanu, ndiye Liwu lokoma lija lidzati, “Inde, tsikulina mu Baton Rouge, kapena malo aang’ono otchedwa DenhamSprings, iye anandiimira Ine, Atate, tsopano Ine ndimuimira iye,kapena mkaziyo.” Perekani izi, Ambuye. Iwowo ndi Anu, muDzina la Yesu. Ameni.

Mulungu akudalitseni inu, chifukwa cha maimidwe anu.Mulungu nthawizo-…138 Tsopano mundichitire chinthu chimodzi ichi ine.Mukafufuze, ngati inu mumakhala pafupi ndi kumene azibusaawa akukhala, mukawawone apang’ono, mukalankhule nawoiwo. Ngati inu simunabatizidwebe panobe, mu ubatizowa Chikhristu, mutero. Mukakhale pakati pa okhulupiriratsopano, okhulupirira enieni, osati odzipangitsa kukhulupirira;okhulupirira enieni.

Pamene ife tikupemphera, tiyeni tipemphereremipango iyi.139 Atate akumwamba, mipango iyi ikupita kunja tsopano;kumene, ine sindikudziwa. Mwinamwake bambo winawokalamba wakhungu wakhala kuno mu chithapwichaching’ono kwinakwake, akudikirira kuti mpango uwu ufike;khanda laling’ono lagona kumeneko pa kama wa mchipatala;mayi waima, atasimidwa, akudikirira kubwera kwa mpango.Atate akumwamba, ine ndikupemphera kuti Inu mupite nayoiyo. Ndipo kwa chizindikiro cha Kukhalapo Kwanu lero, ndichikhulupiriro chathu mwa Inu monga ife talalikirira MawuAnu, mulole chikhulupiriro chimene chinali mwa Abrahamu,ndi chikhulupiriro chimene chinatulutsidwa ndi kuperekedwakwa ife mwa Yesu Khristu, mulole icho chipite ndi mipangoiyi ndipo chikamchize aliyense amene iyo iti ikaikidwepo. Ifetikuitumiza iyo, mu Dzina la Yesu. Ameni.140 Tsopano mphindi chabe, ife tisanaitane mzere wa pemphero.Wamphamvuzonse ndi Mulungu wamphamvu, Mmodziwamkuluyo, Mmodzi wokwanira muzonseyo…Chonde,abwenzi, ine—ine ndiyamba kupempherera odwala, ndipoine…Mwinamwake, pamene ife titi titsikire kumusiko, ine—inemwina sinditha kunena kalikonse kwa inu; ena a inu mukhalamutapita nthawi imeneyo isanafike. Chirichonse chimene inumuli, ngati inu simunaime nkomwe, kanthawi kapitako, ndipoinu simukutsimikiza…141 Ngati ndinu membala wa mpingo, chimenecho ndi chinthuchabwino, koma icho si chabwino mokwanira. Mwaona,mnyamata mwini chuma anali membala wa mpingo. Mukuona?Iye anamufunsa Yesu kuti iye achite chiyani kuti akhale ndiMoyo Wamuyaya. Iye sanawulandire Iwo. Iye anachokapo.Ndi chinthu chopusa bwanji chimene mnyamata ameneyoanachita. Musatenge malo ake. Inu mukukumbukira nthawiyotsiriza imene iye anazindikiritsidwa? Mtsogolo kenako, iye

Page 22: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

22 MAWU OLANKHULIDWA

analemera. Iye anali ndi chuma. Iye anafika pamalo akutingakhale nkhokwe zake zinadzadza. Komano ife tikudzapezakuzindikiritsidwa kwake kotsiriza, mu gehena, malawiakumuzunza.Musati, musalole kuti zimenezo zidzakuchitikireniinu. Mumulandire Khristu.142 Anyamata inu, atsikana aang’ono inu, anyamataaang’ono, basi pa kusinthika kwa moyo, chonde chitanizimenezo. Mundimvere ine, ngati—ngati m’bale wanu, mmodziamene amakukondani inu. Ine ndiri pano chifukwa inendimakukondani inu. Ine ndimamukonda Mulungu, ndipoine ndimakukondani inu, ndipo ine sindingathe kumukondaMulungu ngati ine sindikukukondani inu.143 Ine ndingakonde, ngati inumukadakhala ndi zakutimunene,muzinenere izo pa mwana wanga uyo, kapena mmodzi waana anga. Mulole ine basi…ine, ine ndipita wopanda izo.Kholo lirilonse lingachite zimenezo; chomwechonso Mulungu.Mukuona? Muzikonda anthu Ake. Muzikondana wina ndimzake.144 Inu mukuti, “Kodi inu mukuwazazira iwo chifukwachiyani?” Chikondi chenicheni chimakonza.145 Ngati mwana wanu atakhala uko pa msewu; inu mukati,“Chabwino, Junior wakhala apoyo. Iye sayenera kuchitazimenezo, koma ine sindikufuna kuti ndimupweteke kumvererakwake kwapang’ono.” Iwe sukumukonda iye. Iye aphedwapamenepo. Ngati inu mukumukonda iye, inu mungamutengereiye mkati ndi kumukwapula iye. Inu mungamupange iye kutiazikumverani.146 Ndi mmene Mulungu amachitira. Chikondi chimakonza,ndipo ndicho chikondi chenicheni.147 Pamene mlaliki aimirira ndi kumakulolani akazi inukuti muzidula tsitsi lanu, ndi kumazipentapenta ndi zinthu,ndipo osakukonzani inu, palibepo chikondi chenichenipamenepo; ndipo osazidzudzula izo. Ndipo nkukulolani amunainu kukwatira katatu kapena kanai, ndi zonse za zinthuzina izi, ndipo nkumapitirira nazo izo, palibepo chikondichenicheni pamenepo. Kukulolani inu kujowina tchalitchi,ndi kumakusisitani inu pa nsana, ndi kukuphimbani inundi kachikhulupiriro kena, ndiye, “Ndizo zonse zimene inumuyenera kuchita, mujowine mpingo woyera,” palibepochikondi pamenepo. Kapena, mwina, bamboyo wataikakwathunthu, mwiniwake, iye sakuwona.148 Chikondi chenicheni chimakonza, ndipo chimakubwezeraiwe ku Mawu a Mulungu.149 Tayang’anani pa Yesu, momwe, zimene Iye ananena,chifukwa Iye ankawakonda iwo, mochuluka kwambiri mwakutiIye anafa mmalo mwawo, pamene ngakhale iwo ankafunaMagazi Ake.

Page 23: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 23

150 Tsopano mulole Mzimu Woyera wawukulu…ine ndikufunandidikirire miniti yokha. Ine ndikudikirira mpaka kudzodzakwaMzimuWoyera kufike pa ine, ife tisanayambe. Ine ndakhalandikulalikira. Zikomo inu, chifukwa chamgwirizanowanu.151 Tsopano, mmodzi aliyense muno, kulikonse kumene inumuli, paliponse mchipinda, mupemphere kwa miniti yokha,kuti, “Ambuye Yesu, mundithandize ine! Mundithandize ine!Mundilole ine ndikhudze chovala Chanu.” Yesu anati, inumukudziwa, pamene mkazi anakhudza chovala Chake, Iyesanamverere izo, mwathupi, koma Iye anapotoloka ndipoanadziwa yemwe iye anali ndi chimene iye anachita. Iye aliYesu yemweyo madzulo ano, Wansembe Wamkulu wokhodzakukhudzidwa ndi kumverera kwa chifooko chathu.152 Kodi inu mukukhulupirira, mmodzi aliyense wa inutsopano, izo nzoona, kuti Mulungu amene anapanga lonjezo ili,kamodzinso (ndipo mulole Iye asonyeze izo) kuti ife tikukhalamoyo mmasiku a Sodomu? Ndi angati akukhulupirira zimenezo,mchipinda chino, ingokwezanimmwamba dzanja lanu.153 Ife tikukhala moyo, monga izo zinali, mu Sodomu.Kachitidwe konseko kakhala kovunda, kachitidwe ka mdziko,chirichonse, kachitidwe ka mpingo, kachitidwe ka ndale.Palibepo kalikonse. Ndale zaipa kwambiri. Kachitidwe,konsekonse, olamulira mwankhanza athu, zonse zawonongeka.Mpingo wasanduka mwanjira yomweyo. Mabanja asandukamwanjira yomweyo. Ndi chivundi basi, Sodomu!154 Ndiye, kumbukirani, Mulungu waziyika zimenezo patsogolopanu, ndiye kumbukirani Iye ananena kuti Iye adzaziimiriraYekha mu mnofu wa munthu, ndipo adzachita monga Iyeanachitira kwa Sodomu, Mwana wolonjezedwayo asanabwerepowonekera. Iye analonjeza kuti adzatumiza mmodzi yemweadzatsogolere Mwana wolonjezedwayo, monga Iye anachitira pamalo oyambirira, zimene ziti zidzamusonyeze; ndipo Iye anati,“PameneMwana wamunthu akuwululidwa.”155 Ine sindikukudziwani inu. Chabwino, Abiti Thompson, vutolachikazi lija ndi zosokonezeka, inu mukukhulupirira kutiMulungu akuchizani inu? Kodi inu mungakhulupirire zimenezo?Inu mutero? Abiti, Abiti Thomas, inu mukukhulupirira kuti Iyeakuchizani inu? Kwezanimmwambamanja anu, ndiye.156 Pali dona wakhala kumbuyo kwanu komwe. Iyeakupemphera. Iye ali ndi nyamakazi.157 Uyo amene wakhala pafupi ndi iye, ali ndi vuto lammimba, akupemphera nayenso. Inu muziphonya izo, inusimukuzisamala. Sindinu wochokera kuno. Ndinu wochokeraku Mississippi. Ndinu Bambo ndi Mayi Stringer. Ngatiinu mukukhulupirira ndi mtima wanu wonse, Yesu Khristuakuchizani inu. Ngati inu mungakhulupirire izo. Mutero

Page 24: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

24 MAWU OLANKHULIDWA

inu? Ndiye inu mukhoza kulandira izo. Chabwino. Kwezanimmwambamanja anu kuti anthu awone kuti ndi inuyo.158 Ine sindikuwadziwa anthu amenewo. Ine sindinayambendawawonapo iwo, mmoyowanga. Inumuyenera kukhulupirira,mzanga. Iye akuzizindikiritsa Yekha. Kodi inu mukukhulupirirazimenezo, ndi mtima wanu wonse? [Osonkhana akuti,“Ameni.”—Mkonzi.]159 Nchifukwa chiyani inu munagwedeza mutu wanu, bwana,ndi kundiyang’ana ine monga choncho? Inde, bwana. Chifukwainu mwachita zimenezo, ine ndilankhula nanu miniti. Ndinuwokhala ngati njonda ya usinkhu mwakhala pomwe apa,mukundiyang’ana ine. Iye anandiyang’ana ine, ndi kuwonamtima kotero. Iye wakhulupirira izo. Inu mukumupemphererawinawake yemwe anali ndi stroko. Koma—koma chinthuchanu chenicheni chimene inu mukuchipempherera, inumukusowa, inu mukufunafuna ubatizo wa Mzimu Woyera. Ukonkulondola. Uh-huh. Izo nzoona. Ngati inu mukukhulupiriraizo! Dona, inu mukufuna ntchito. Pambali pa zimenezo, kuti inumudziwe kuti ine ndi mneneri wa Mulungu, kapena wantchito,inu mwachitidwapo ma opareshoni awiri. Izo zakusiyaniinu wofooka. Zikhalidwe za mitundu yonse, vuto lauzimu.Ine ndikufuna kuti ndikuuzeni inu kuti izo zonse zatha.Chikhulupiriro chanu chakuchizani inu.160 [Malo osajambulidwa pa tepi—Mkonzi.]…wakhala pafupindi inu apo. Iye akupemphera. Yang’anani kuno. Iye wakumvaniinu, ndipo inu mwamukhudza Iye. Sindikukudziwani inu,koma Iye akukudziwani. Ine ndikuuzani inu chimene inumumachipempherera. Inu mukukhulupirira ndi mtima wanuwonse? Inu muli ndi vuto la chikhodzodzo, inu mukupemphera.Kodi inu mukukhulupirira kuti Mulungu akuchizani inu ndipoakupangani inu wabwino bwino? Ndinu Akazi a Smith. Izonzoona. Kwezani dzanja lanu.161 Mwaona, Iye akuzizindikiritsa Yekha. Ndi chiyanichimenecho? Ndi Mbewu ya Abrahamu, chikhulupiriro chimeneAbrahamu anali nacho, Ambuye Yesu Khristu pakati pathu,kutsimikiziraMawuAke, ndi zizindikiro zikutsatira.162 Ndani, ndi makadi angati amene ali oti apemphereredwe,kwezani manja anu, muli ndi khadi lanu? O, ife kuli bwinotiyambe mzere wa pemphero.163 Inu mukuona, inu mukumvetsa sichoncho inu? Tsopanomzimu umenewo sikuti kokha…Umenewo sumachiritsa. Iwoukungomuzindikiritsa kokha Iye kuti ali pano. Azibusa anu alindi ulamuliro womwe womwewo kuti azipempherera odwala.Iwo samachita zimenezo; ayi, ndithudi ayi. Koma iwo—koma iwo ali ndi ulamuliro womwewo basi, “Zizindikiro izozidzawatsatira okhulupirira.”

Page 25: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 25

164 Tsopano ine ndikufuna azibusa amzanga pano. (Kodi ziribwino, kuitana kuchokeramwa omvetsera…?…)165 Ndi azibusa angati pano amene mukukhulupirira ndimtima wanu wonse, azitumiki muno, mukukhulupirira? O,zikomo inu. Ine ndikudabwa ngati inu muti muime? Bweranikuno, mudzaime ndi ine miniti yokha, pansi pomwe pano,mudzapempherere odwala. Mubwere pansi pano. Tsopano inumuwonemachiritso akuchitika,muwone zimene zimachitika.166 Ine ndikufuna kuti inu mubwere, mudzapange—mzerewa pawiri pomwe pano. Ine ndibwera pansipo mu mphindichabe, kuti ndidzapempherere odwala. Ine ndikufuna azibusaokhulupirira amene akufuna kuti azizindikiritse okhangati okhulupirira. Zimenezo, inu mukukhulupirira, kutikubwera kwanu kuno, inu mukukhala moyo woyera, moyowabwino. Kumbukirani, yang’anani kuno amene akutulukira,kudzaimirira Uthenga wa Khristu!167 M’bale Blair, ine ndikukudziwani inu pamenepo, inu kapenaM’bale Pat. Kodi inu mungapange mzere wapawiri uwo momweinu mumachitira nthawizonse, ngati inu mungathe, inu ndiM’bale Pat.168 Azibusa okhulupirira amene ati akhulupirire! Tsopano,taonani, ngati Mulungu angazizindikiritse chomwecho Yekhandi Mawu Ake, ndi Mawu Ake, ndi angati akudziwa kutiBaibulo, Yesu ananena izi, “Zizindikiro izi zidzawatsataiwo amene akhulupirira. Ngati iwo adzaika manja awo paodwala, iwo adzachira”? Azibusa, inu mwabwera kuno kutimudzazizindikiritse nokha ngati okhulupirira. Ndi choncho?Ndinu okhulupirira (sinchocho inu?), inu sibwenzi mutaimapano. Tsopano kodi Yesu ananena chiyani? “Zizindikiro izizidzawatsata iwo amene akhulupirira.” Ndine wokhulupiriralimodzi ndi inu.169 Ine ndikubwera pansipo. Awa ndi anthu athu, ndipondife abusa pa nkhosa izi. Ine ndikubwera mmusimo kutindidzatambasule ukonde wanga limodzi ndi inu tsopano,kudzaika manja anga limodzi ndi anu. Ndipo pamene anthuawa azibwera, ngati inu muli ndi chirichonse chimenemukuchikaikira pang’onommalingaliro anu, chichotsenimo ichopakali pano; kuchitira kuti pamene anthu awa azibwera, ndiyemmodzi aliyense wa iwo akubwera, ndipo ife nkuika manja paiwo, iwo achiritsidwe. Kodi inu mukhulupirira ndi mtima wanuwonse tsopano, aliyense? [Atumiki akuti, “Ameni.”—Mkonzi.]170 Ndi angati muno amene akhale akupempherera ena pameneiwo azidutsa, kwezani mmwamba dzanja lanu, “Ine ndikhalandikupemphera.”171 Kumbukirani, akhoza kukhala abambo anu, amayi anu,mwana wanu wamkazi kapena mwana wamwamuna, mlongokapenam’bale. Ndipo ngati si ali anu, ndi a winawake, amene ati

Page 26: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

26 MAWU OLANKHULIDWA

abwere kudutsa mzere uwu. Ndipo nanga bwanji ngati atakhalaiwowo, ndipo iwo anali akufa ndi khansa, kapena matenda enaowopsya, kodi simungafune amuna kuti akhale woona mtimamwakuya? Ndithudi, ife tingatero.172 Tsopano, ine ndikukhulupirira, inu muchita motani…Tsopano awamumzere uwu apa, kanjira aka, taimanimotsamirambali iyo, muli ndi khadi la pemphero. Muimirire motsamirambali iyo, onse amene ali kumbali ya kumanja. Tsopano, njira,mukhale mbali ya kumanzere; ife tidzadzanamo, inu mukuona,ndipo inu simukudziwa motani, zimene ife tikuchita. Chabwino,onse amene ali mu chigawo ichi, muime uku. Tsopano, onseamene ali ku chigawo cha dzanja lamanja, mungobwera mbaliiyi, chifukwa inumutsikirammusi, mubweramozungulira.173 Ndipo ndi motani, atuluka bwanji, M’bale Borders?Azitulukira chitseko cha mmbali, mubwere chozungulira ndiponkudzalowanso mkati.174 Kotero, pamene mbali iyi iziitanidwa, mu maminitipang’ono, ndipo iwo adzaimirira. Ndipo tiyeni tiwone tsopanochimene…Chabwino, iwo amene ali mu chigawo ichi,tembenukirani mbali iyi cha kuno. Mugwire makadi anu apemphero, mufike ku mbali iyi. Ndipo inu mchipinda, muyendechotsika kuti mukakomane nawo iwo kumapeto kwa mzerepamwamba apo. Tsopano awa amene ali ku chigawo cha dzanjala kumanzere, mupite kumbali ya dzanja lakumanzere. Ndiyeno,inu mukuona, inu mupange mzere wanu ndipo mubwererenjira iyo; potolokani, potolokerani mbali iyo. Mukuona?Ndipo inu mutsatire mzere mozungulira kumanja, zikaterositisakanizikana nkomwe.175 Ndiyeno inu amene muli mchipinda, mungokonza maloanu mtinjira timeneto, ndipo muzingogwera mkati pamene iwoazidutsa.176 Tsopano, tsopano ingoyambani kumayenda chammbuyo,mmodzi aliyense, kaziyendani mukubwerera mmbuyo mpakamukomane ndi mzere uwu mozungulira apa. Kazingobweranimozungulira, pamwamba apa, basi yambani kumayendamozungulira ndipomubwere kumzere uwu pomwe apa.177 O, pangachitike chiyani pakali pano! Pangachitike chiyani!Ino ikhala nthawi imene chinachake chiyenera kuchitika.Chabwino.178 Tsopano, uko nkulondola, mubwerere mmbuyomukuzungulira mbali iyo, ndipo mukalowe mu mzerewo, mongachoncho. Muzipita mukuzungulira kanjira aka. Njira yake ndiimeneyo tsopano.179 Ndipo tsopano pamene inu mukuimirira, aliyense aimirire,ife tipemphera. Ndipo osonkhana awa apemphera ndi ine, kutiinu muchiritsidwe. Mungokhala ndi chikhulupiriro tsopano.Ndipo musati…

Page 27: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGA CHIPATA CHA MDANI PAMBUYO PA YESERO 27

180 Kazibwerani mukuzungulira, kumbuyo komwe mmbuyo,kazibweranibe mozungulira ndipo mudzajowinane ndi mzereuwu kumbuyo uko. Kazibwerani mukuzungulira, mudzapangemzere umodzi wawukulu. Kazibwerani mozungulira mbaliimeneyo, ndipomudzapangemzere umodzi. Ndi zimenezotu.181 Aliyense akhale mu pemphero. Mukhale kwenikwenimu chikhulupiriro tsopano. Basi sindikuzindikira chiguluchitsopano. Kumbukirani, ife tiri—ife tazunguliridwa ndiKukhalapo kwa Yesu Khristu, akudalira pa ife kuti alemekezezimene Iye wachita pakati pathu, pakukhala ndi chikhulupiriromu Mawu Ake.182 Izo nzabwino. Tsopano izo zikhala bwino. Ine ndikuganizamzere uwo ukulowamkati modabwitsa basi.183 Tsopano pamene iwo onse aimirira, ine ndikufuna munthualiyense tsopano, mchipinda muno, kuti muweramitse mutuwanu.184 Ambuye Yesu, zichitika posachedwapa. Chigamulochiyenera kuti chipangidwe pakali pano. Kodi ifetikukhulupirira kuti Inu muli pano? Kodi ife timakukondaniInu? Kodi ife tiri nacho chikhulupiriro, Ambuye, chokwanirandi zimene ife titi tipemphe? Anthu awa akuzizindikiritsaokha poima mu mzere. Ambuye, mulole izo zisakhale pachabe.Mulole izo zikhale, Ambuye, kuti iwo azidutsa apa, mmodzialiyense azidutsa ngati kuti akudutsa pansi pa Khristu, pakutiife tikudziwa Iye ali pano. Ndipo ife tikupemphera kuti iwoalandire machiritso awo. Ine ndikutsimikiza kuti ngakhalemmasabata ndi mmasabata akudzawa, anthu awa akhalaakupita kwa azibusa awo, akazi amene anali ndi vuto lachikazi,vuto la mmimba, amuna okhala ndi thumbo, mitundu yonseya zovuta, achiritsidwa, akukati, “Inu mukudziwa, chinthuchochinangondichokera ine,” pakuti iwo ali mu Kukhalapo Kwanu.Mulole iwo abwere akudutsa tsopano ndipo—ndipo adzatenge izizimene Inumunafera. Iwowo aliMbewu yaAbrahamu, ndipo Inumunawagonjetsera iwo. Mulole iwo abwere ndipo adzalandirezimene Inu mwapereka kwa iwo.185 Ndipo, Satana, iwe wayalutsidwa kwambiri sabata ino,mpaka iwe ukudziwa kuti iwe ndi chinthu chogonjetsedwa.Yesu Khristu anakugonjetsa iwe pa Kalvare. Iye anadzaukapa tsiku lachitatu, kwa kulungamitsidwa kwathu, ndipo Iyeakuima pakati pathu tsopano. Ndipo chikhulupiriro chathuchikuyang’ana kwa Iye, ndipo tachoka kwa iwe kapenachirichonse chimene iwe wachita. Uwasiye anthu awa, muDzinala Yesu Khristu.186 [M’bale Branham ndi azitumiki akuika manja pa odwalandipo akumupempherera mmodzi aliyense mu mzere wapemphero.Malo osajambulidwa pa tepi—Mkonzi.]…?…

Page 28: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

28 MAWU OLANKHULIDWA

187 Ife tachita chimodzimodzi monga Ambuye anatilamulira ifekuti tizichitira. Ndi angati a inu amene munapita kudutsa mzereumenewo, mumakhulupirira kuti mukhala bwino, kwezanimmwambadzanja lanu. Ine ndikujowinitsa langa limodzi nanu.188 Zimene ife timachita pamenepo, potsiriza, ngati gulu laatumiki pamenepo; ambiri a iwo amadwala, ine ndimadziwazimenezo, koma iwo akuyesetsa kuti ayikepo kuyesetsa kwawokuti alowetsemo osonkhana awo, kaya iwo alowa mkati kapenaayi. Amenewo ndi abusa enieni. Ndipo Mzimu Woyera unatikwa ine, “Uwapangitse iwo agwirane manja wina ndi mzake.”Ife tinalumikizitsa mitima yathu ndi maukonde pamodzi, ndimapemphero athu, limodzi.189 Yesu, achiritseni iwo, nawonso. Ndipo muwapange iwoakhale azibusa amphamvu, amphamvumuMawu aAmbuye.190 Mulole Mulungu, abale anga, mulole Iye akupatseniinu zokhumba zanu zonse za mtima wanu. Mulole inumukantumikire Iye masiku onse, ndipo mukakhale ndimphamvu ya Mulungu mmiyoyo yanu, kuti mukatumikire kwagulu labwino ili la anthu. Mulole Yesu Khristu, Yemwe wakhalaali ndi ife, ndipo adzakhala ndi inu nthawi zonse, mulole Iyeadzipange Yekha wokhazikika kwa inu kuposa mmene Iyewakhala akukhalira mmbuyomu.191 Anthu inu, ena a inu amene munalumala, inu mukhozakusawona kusiyana kulikonse kwa kanthawi, inu mukhozakusawona kusiyana kulikonse. Taonani zimene Abrahamuanachita. Sizimapanga kusiyana kulikonse zimenezo; zimenezosi zimene inu mukuyang’anapo. Iwe sumayang’ana pazokuchitikira zako. Umayang’ana pa zimene Iye ananena.Ngati inu mukuti, “Ine ndikumvererabe ululuwo,” izo ziribechochita chirichonse ndi zimenezo. Inu mwachita zimeneMulungu anati muchite. Mwaona, musayang’ane pa zimenezo.Muziyang’ana pa zimene Iye ananena. Mulungu anati zinalichomwecho! Ine ndikukhulupirira izo. Sichoncho inu?[Osonkhana akuti, “Ameni.”—Mkonzi.] Ndi mtima wanga wonse,ine ndikukhulupirira izo.192 Ambuye Mulungu akudalitseni inu mpaka inendidzakuwoneninso inu. Mapemphero anga ndi a inu; usikusumachita mdima kwambiri, mvula siimavumba molimbikakwambiri. Ine ndidzakhala ndikukupemphererani inu. Inumuzindipempherera ine. Mpaka ife tidzakomanenso, Mulunguakudalitseni inu. Tsopano m’bale amene amachita ubusa,mwaona.

Page 29: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

KUTENGACHIPATACHA MDANI PAMBUYO PAYESERO CHA64-0322(Possessing The Gate Of The Enemy After Trial)

Uthenga uwu wa M’bale William Marrion Branham, woperekedwa muChingerezi Lamlungu madzulo, Marichi 22, 1964, ku Denham Springs HighSchool mu Denham Springs, Louisiana, U.S.A., unatengedwa kuchokera pamatepi ojambulidwa ndi maginito nudindidwa mosachotsera mawu ena muChingerezi. Kumasulira kwa Chichewa uku kunadindidwa ndi kugawidwa ndiVoice Of God Recordings.

CHICHEWA

©2017 VGR, ALL RIGHTS RESERVED

VOICE OF GOD RECORDINGS, MALAWI OFFICE

P.O. BOX 51453, LIMBE, MALAWI

VOICE OF GOD RECORDINGS

P.O. BOX 950, JEFFERSONVILLE, INDIANA 47131 U.S.A.www.branham.org

Page 30: CHA64-0322 Kutenga Chipata Cha Mdani Pambuyo Pa Yesero VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA64-0322 Possessing... · 5 Iye anati, “Chabwino, kodi ulipo mwayi wakuti ... 45 O, mai,

Chidziwitso kwa ofuna kusindikiza

Maufulu onse ndi osungidwa. Bukhu ili mukhoza ku printa kunyumba kwanu ngati mutafuna kuti mugwiritse ntchito inuyo kapena kuti mukawapatse ena, ulere, ngati chida chofalitsira Uthenga wa Yesu Khristu. Bukhu ili simungathe kuligulitsa, kulichulukitsa kuti akhalepo ambiri, kuikidwa pa intaneti, kukaliika pakuti ena azitengapo, kumasuliridwa mu zinenero zina, kapena kugwiritsidwa ntchito ngati njira yopezera ndalama popanda chilolezo chochita kulembedwa ndi a Voice Of God Recordings®.

Ngati mukufuna kuti mumve zambiri kapena ngati mukufuna zipangizo zina zimene tiri nazo, chonde mulembere ku:

Voice of God RecoRdinGsP.o. Box 950, JeffeRsonVille, indiana 47131 U.s.a.

www.branham.org