kutenga mbali n y - download.branham.orgdownload.branham.org/pdf/cha/cha62-0601 taking sides with...

68
KUTENGA MBALI NDI Y ESU Malo ena ku Louisville, kumene i—inu mumakadyako, ndipo iwo amatchedwa, tiyeni tiwone, Dogpatch Restaurant. Ine ndiri nako kamodzi, lero. Pamene aliyense adya kumeneko, ndiye iwo amatenga ndalama zimene iwe unawapatsa iwo, ndipo amautumizira mpingo chakhumi chochokera pa izo. Ali penapake ku Msewu wa 319 West Jefferson. Ine ndikulinglira ndi chifukwa chake Billy anachiika icho apa, kuti iwo akanakhoza kuchiwona. Izo nzabwino mwamphamvu. 2 Tsopano, abale, ine sindikudziwa kachitidwe kanu k—ka msonkhano wa amuna, basi zimene inu mumachita, kapena momwe inu mumachitira misonkhano yanu. Ndipo ngati ine nditi ndichoke mu dongosolo pano, bwanji, ndikachoka pa kachitidwe kachizolowezi, motero, inu muitane tcheru changa kwa izo. 3 Izo zinalingaliridwa usikuuno, ine ndimaganiza, pamene ine ndinali kutenga n—nkhumaliro osati kale litali ndi m’busa wathu wokondedwa kwambiri, M’bale Neville, ndipo ine ndinali kunena chinachake kwa iye chimene chinali pa mtima wanga. Ndipo ine ndinaganiza, ngati ife tingatenge gulu la amuna palimodzi, ndi atumiki, iwo ndi amzathu kuno a Uthenga, ndi amuna, ife tikanati tiyankhulane kwa wina ndi mzake mwa njira imene ife sitikanakhoza kuyankhula izo pamaso pa gulu. Chifukwa ife tonse ndi…Ndife amuna amene timamvetsa ngati amuna, amuna Achikhristu. Ndipo mwa njira imeneyo, kawirikawiri, mwa osonkhana, gulu, iwe umanena chinachake, n—ndipo wina amatsamiritsa izo pang’ono mwanjira iyi, ndipo wina amatsamira izo mwanjira iyo, n—ndiyeno izo zonse zimangopita kunja. Koma pamene ife tibwera kuti tidzayesere, usikuuno, kuti ndidzakuuzeni inu zimene ndiri nazo mu mtima wanga, zokhudza mpingowu, n—ndi malo ake, ndi udindo wake. Ndiyeno ngati ife titi titsirize mu nthawi, ine ndikufuna kuti ndiyankhule kwa inu pang’ono pokha pa Mawu, ngati ziri zabwino. Kungokhala ngati tizikhazikitse izo, chotero ife titenga gawo lathu lantchito, kapena gawo limene ine ndikufuna kuti ndilifotokoze kwa inu, poyamba. Ndipo ine ndikulingalira mwinamwake inu mutulutsidwa, nthawi yachizolowezi, pafupi hafu pasiti naini kapena inayake monga iyo, monga usiku uliwonse. Chabwino, ine ndiyesera kuti ndisakusungeni inu motalika. Mawa ndi Loweruka, ndipo ndi tsiku lalikulu lamalonda, koma tsopano ife timayenera kukagula zapanyumba zathu ndi zina zotero. 4 Ine ndikufuna kuti ndinene kwa M’bale Neville, mwapagulu. Tsopano i—ine ndikufuna kuti ndinene, kwa aliyense wa

Upload: others

Post on 06-Nov-2019

3 views

Category:

Documents


0 download

TRANSCRIPT

KUTENGAMBALI NDI YESU

Malo ena ku Louisville, kumene i—inu mumakadyako,ndipo iwo amatchedwa, tiyeni tiwone, Dogpatch

Restaurant. Ine ndiri nako kamodzi, lero. Pamene aliyenseadya kumeneko, ndiye iwo amatenga ndalama zimene iweunawapatsa iwo, ndipo amautumizira mpingo chakhumichochokera pa izo. Ali penapake ku Msewu wa 319 WestJefferson. Ine ndikulinglira ndi chifukwa chake Billy anachiikaicho apa, kuti iwo akanakhoza kuchiwona. Izo nzabwinomwamphamvu.2 Tsopano, abale, ine sindikudziwa kachitidwe kanu k—kamsonkhano wa amuna, basi zimene inu mumachita, kapenamomwe inu mumachitira misonkhano yanu. Ndipo ngati inenditi ndichoke mu dongosolo pano, bwanji, ndikachoka pakachitidwe kachizolowezi, motero, inu muitane tcheru changakwa izo.3 Izo zinalingaliridwa usikuuno, ine ndimaganiza, pameneine ndinali kutenga n—nkhumaliro osati kale litali ndi m’busawathu wokondedwa kwambiri, M’bale Neville, ndipo ine ndinalikunena chinachake kwa iye chimene chinali pa mtima wanga.Ndipo ine ndinaganiza, ngati ife tingatenge gulu la amunapalimodzi, ndi atumiki, iwo ndi amzathu kuno a Uthenga,ndi amuna, ife tikanati tiyankhulane kwa wina ndi mzakemwa njira imene ife sitikanakhoza kuyankhula izo pamaso pagulu. Chifukwa ife tonse ndi…Ndife amuna amene timamvetsangati amuna, amuna Achikhristu. Ndipo mwa njira imeneyo,kawirikawiri, mwa osonkhana, gulu, iwe umanena chinachake,n—ndipo wina amatsamiritsa izo pang’ono mwanjira iyi, ndipowina amatsamira izo mwanjira iyo, n—ndiyeno izo zonsezimangopita kunja. Koma pamene ife tibwera kuti tidzayesere,usikuuno, kuti ndidzakuuzeni inu zimene ndiri nazo mu mtimawanga, zokhudza mpingowu, n—ndi malo ake, ndi udindowake. Ndiyeno ngati ife titi titsirize mu nthawi, ine ndikufunakuti ndiyankhule kwa inu pang’ono pokha pa Mawu, ngatiziri zabwino. Kungokhala ngati tizikhazikitse izo, chotero ifetitenga gawo lathu lantchito, kapena gawo limene ine ndikufunakuti ndilifotokoze kwa inu, poyamba. Ndipo ine ndikulingaliramwinamwake inu mutulutsidwa, nthawi yachizolowezi, pafupihafu pasiti naini kapena inayake monga iyo, monga usikuuliwonse. Chabwino, ine ndiyesera kuti ndisakusungeni inumotalika. Mawa ndi Loweruka, ndipo ndi tsiku lalikululamalonda, koma tsopano ife timayenera kukagula zapanyumbazathu ndi zina zotero.4 Ine ndikufuna kuti ndinene kwaM’bale Neville, mwapagulu.Tsopano i—ine ndikufuna kuti ndinene, kwa aliyense wa

804 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

inu, chimodzimodzi ngati kuti ine ndikuyankhula ndi inumwapadera, aliyense basi. Chifukwa, ndinu gulu li—limene…Ine ndikuganiza kwenikweni kuti, ndipo ndimakhulupirirandi kuphunzitsa, kuti, amuna, Mulungu anawapanga amunamu utsogoleri wa Mpingo Wake, kwa anthu Ake. Mukuona?Ndipo ndizo…Monga ine ndimalalikira uko kwa M’baleJunie Jackson, usiku watha, zakuti Mulungu amawatchingiraA—anthu Ake ndi Mawu Ake. Ndipo anali mkazi yemweanaswa nadutsa mzere umenewo ndipo anapereka dangakwa kulingalira, ndipo pamene izo zinatero, Mulungukwanthawizonse wakhala akuziika izo kwa Ake, kwa amunakuti aziusungaMpingoWakemotchingiridwa ndiMawu.5 Tsopano, i—ine ndikufuna kuti ndimulimbikitse M’baleNeville pang’ono pokha, kuyankhula kwa iye mwapadera.Ine ndinazindikira usiku watha, kuzindikira za mu mtimakunandikhudza ine, kawiri kapena katatu, pamene inendinali pa guwa. Ndipo ine ndinapotoloka apo, chifukwa inendikuyesera kuti nditalikire kwa izo momwe ine ndingathere,mpaka ine nditapeza chimene malotowo ankatanthauza kwaine kuno osati kale litali, masabata angapo apitawo. Iwoandikangamira ine kwa nthawi yaitali. Ine ndinadzawanenaiwo kuno mu mpingo, za chinachake cha Uthenga n—ndikuzindikira za mu mtima, ndi zina zotero. Iwo basi sanali,kungoti sizimatulukirapo moyenera. Mwa kulingalira kwanga,nthawi imeneyo yatha, ndipo ine mwina ndikhoza kukhalandikulakwitsa pa izo, koma ine ndinazindikira k—kuti M’baleNeville amakhala ngati wotopetsedwa ndiwokwiyitsidwa.6 Ndipo komabe ine ndimangofuna kuti inu mudziwe,M’bale Neville, kuti inu mukungoyembekezera mu chiyanjanochimenechi. Kodi inu mwazindikira kumene zomwe Satanaamayesera kuti achite mu masiku angapo apitawa kwa atumikiomwe akuyanjana nafe mu chiyanjano ichi? Mungoima kwamaminiti pang’ono, ndi kudabwa. Apa pakhala M’bale Crase,ali apa, usikuuno, pafupi kuti akanaphedwa uko pa msewu.Mwaona? Ndipo ine ndinali pafupi mutu wanga kuphulitsidwandi mfuti, kapena ndi mfuti yaitali. Mwaona? Satana amayeserakuti atitenge ife. Ndipo apo inu munadzigunditsa umo momwe,ndipo mukanakhoza kudzipha nokha ndi mkazi wina wakenso.Mukuona? Atumiki okhaokha, yang’anani pa basi—gulu laotumikira. Mwaona? Ndi Satana, ndipo iye akuyesera kutiatichotsepo ife.7 Tsopano, ife tikuzindikira kuti ife sitinasonkhane pano kutitiyankhule pa mtundu wina wa zamalonda. Ife tiri pano kutitisonkhane, kuti tiyankhule z…zaKhristu, ndimagwiridwe akekuti tigwiritse, ndi zoti tizichita pa nthawi ilipo ino.

Ndipo i—ine ndikufuna kuti ndikulimbikitseni inu, M’baleNeville. Khalani wolimbamtima. Ziribe kanthu zomwe zitizibwerepo, ziti zipite, ziti zichitike, musati mulole chirichonse

KUTENGA MBALI NDI YESU 805

chikukwiyitseni inu. Ingoimani apo monga thanthwe lamibadwo, ndipo Mulungu apangitsa chirichonse chitulukiremwabwino. Iye watsimikizira izo kwa inu. Ndithudi, zijazizikanakhoza kukukwiyitsani inu, izo zikanakhoza kumuphamkazi uja, ndipo izo zikanakhala ziri mu malingaliro anu,masiku anu onse, ndipo apo pakanakhoza kukhala pali zinthuzambiri. Koma Mulungu akadali pa Mpandowachifumu. Iye,Iye amalola zinthu zimenezo kuti zichitike mwabwino. Iyeakanakhoza kutitenga ife, nafenso. Ndipo, chotero, Satanaakumenyana nawo Mpingo.8 Tsopano, pamene ine ndinkaika mwala wapangodya uwommawa uja, ine sindinkamverera kuti ine ndikanadzakhalakonse ndiri m’busa. Izo sizinali mu maitanidwe anga, pachiyambi. Ndipo kuitana kwanga koyamba kunali koti ndikhalendiri mmunda wa uvangeli. Izo zinali zaka zambiri zapitazo.Ndipo ndinayambira, kunomuhema, kungowolokamsewuwu.

Ndipo ine ndikukumbukira pamene M’bale Roy Davis,kumusi uko, ndipo tchalitchi chake chitapsya. Gulu la anthu ilolinali ngati nkhosa zobalalika zopanda m’busa, analibe malo otiazipitako.

Ndipo Bambo Hibstenberg anali Mkulu wa Polisi apo,ndipo iwo anandiitanira ine uko. Iwo anati kwa ine, “Ifetiri pano kuti tikuthandizeni inu.” Anati, “Ine ndi waChikatolika, mwiniwanga, koma,” anati, “anthu awo,” anati,“iwomwinamwake alibe zovala.” Iyo inali nthawi yovuta chuma.Anati, “Iwo akapita ku mipingo ina ndipo iwo akamverera kutisali koyenera, ndipo iwo ndi anthu abwino. Ine ndikuwadziwaambiri a iwo.” Iye anati, “Billy, ngati iwe ukufuna kutiuyambitse mpingo,” iye anati, “ine ndikufuna kuti iwe udziwekuti ife tiri pambuyo pakomu chirichonse chimene ife tingachitekuti tikuthandizire iwe.”Ndipo ine ndinamuthokoza iye pa izo.9 Ife tinali ndi tsiku la chikhomo. Poyamba, ife tinapempherandipo tinawafunsa Ambuye. Ndipo anthu ankabwera kwa inendipo ankafuna kuti timange tchalitchi, chotero kuti akhale ndimalo oti azipitako. Ndipo ife tinalingalira malo ano, ndipo usikuwina cha mu nthawi ino, kapena kupitirira pang’ono pano, pamulu waung’ono wa udzu wa kavalo pomwe pano, ndi madzi alimu chidikha ichi, ndipo panangokhala ngati pa dambo, ngati.Chabwino, Ambuye anayankhula kwa ine mwatchutchutchundipo anati, “Uchimange icho pomwe pano.” Ndiribe khobidila ndalama, ndipo pakati pathu ife tinali ndi pafupi—masentieyite kapena dola. Ndipo ndizo, ndithudi, inu muzingaseke izotsopano, koma, m’bale, izo zinali ndalama ndithu apo.10 Pamene woyandikana nawe ankaphika mphika wa nyemba,ndipo apo nkuti woyandikana naye asanakhale ndi kanthu kwamasiku awiri kapena atatu, nabwera ndi kudzadya pang’ono zaizo, iyo inali nthawi yovuta. Ambiri a anyamata aang’onowa

806 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

sanaziwonepo konse izo, koma uko kunali kupita movuta.Ine ndinawona nthawi yomwe iwe unkakhoza kudutsitsamu mpingo uno mbale ya chopereka, kawiri, kapena katatu,ndi kungopeza masenti sate kuchokera mu malo odzaza,ndi kumapempha pofuna icho. Izo zimakhoza…Iwe mwinaumapeza masenti sate, ndipo icho nkukhala choperekachabwino.Mukuona? Iko ndithudi kunali kupitamovuta.11 Ndipo ife tinalibe chirichonse choti timangire nacho,komabe—chokhumba cha anthu chinali choti timange tchalitchi,kuti ife tikhale ndi malo oti tizipitako. Chifukwa, mu masikuamenewo…Uthenga, chabwino, inu mukuganiza kuti Iwoukuganiziridwa moyipa tsopano. Inu mukanati mudziwe za Iwoapo, pamene panalibe aliyense, ndiyeno za ubatizo wa mmadziuwu mu Dzina la Yesu Khristu, ndi m—madalitso ndi zinthuzimene ife tikukhulupiriramozi ndi kuima nazo.12 Kotero pa mtima wanga ine ndinapanga lonjezo kwaMulungu, kuti ife tikanakhala pano ndi kumangapo kachisi.Mmawa umene ife tinadzaika mwala wapangodya, Iyeanakomana nane cha apo mwa masomphenya, pafupi eyitikoloko mmawa umenewo, pamene ine ndinali nditakhalapamenepo, ndikuyang’ana kwinako, dzuwa likutuluka apo,pafupi cha mu nthawi ino ya chaka. Ndipo Iye anali atandiuzaine, Iye atakomana nane kale uko pa mtsinje, ndi Ujayu,pamene Mngelo wa Ambuye anawonekera mu Kuwala kuja. Inendinakuwona Iko mwa patali. Iko kunkawoneka ngati nyenyezi.Ndipo Iko kunabwera pansi pomwe kumene pamwamba papamene ine ndinali, ndipo mawu odziwika aja analankhulidwa.Ndipo kotero, ndiye, ine ndinalinga ndiye kuti ndiwapezereanthu malo oti azikapembedzamo.13 Tsopano, ine ndinaganiza, mwiniwanga, “Iwo si a ine.Palibepo kanthu ka ine.” Koma apobe chirichonse chimene chiricha kwa Mulungu chiri gawo la ine, ziribe kanthu ngati ch…Chirichonse ch—chimene chiri cha ana a Mulungu, ndi cha ine,kaya ndi ntchito yanga kuti ndichite izi, kapena kuti ndichite izo.Iyo ndi ntchito yanga kuti ndiziyang’anira chuma cha Mulungu,palibe kanthu komwe icho chiri. Mwaona?14 Monga momwe inu munganenere kuti, “Chabwino, mai…”Monga inu mukanakhala mnyamata wamng’ono, nkuti, “N—ntchito yanga ndi kungowaza nkhuni, osati kuzinyamula izo.Msiyeni John anyamulire izo umo. Ine sindikusamala ngatichisanu chikugwera pa izo, mvula. Msiyeni iye atuluke kutiakazitenge izo.” Ayi. Ndi ntchito yako m—monga mwana wa pabanja limenelo kuwonetsetsa kuti nkhuni zimenezo zisanyowe,ndi za amayi ako. Mukuona? Zinyamulire izo umo.15 Ngati iwo atati, “Chabwino, Frank amayenera kuti apitendi kukatunga madzi. Iyo si ntchito yanga.” Koma ngati Franksanakatunge madziwo, ndi ntchito yako kuti usamalire za

KUTENGA MBALI NDI YESU 807

madziwo. Ndi zomwezo. Tsopano, umo basi ndi momwe izozimayendera.

Ndipo umo ndi momwe zimayendera mu banja la Mulungu,namonso. Ngati ena a iwo—ena a iwo ati…16 Wina, osati kale litali, anati, “Siya kulalikira momwe iweukuchitiramu. Mai, kalanga, iwe umuwononga mzako aliyenseyemwe iwe uli naye, ndi chirichonse monga choncho.” Nati,“Zisiye izo zokha. Ine ndikudziwa kuti izo ndi zolakwika, koma,mai, iyo si ntchito yathu.”

Chabwino, nanga kodi iyo ndi ntchito ya ndani ndiye? Ngatiizo ziri zolakwika, winawake ayenera kuti achite izo, koterotiyeni tizingochita izo. Ndipo umo ndimomwe ine ndimamvererapa za Mpingo.17 Madongosolo azomanga ndi zina zotero abwerapo,mmwamba ndi pansi, mmwamba ndi pansi, ndipo pakhalapali ovomereza ndi okana, mu zomanga, ndi zina zotero. Enaamafuna izo, ndipo ena samafuna izo, ndi izi, izo. Inu, inumumazipeza izo monga choncho.18 Inu mumapeza kuti pamene iwe ukuchita pakati pa atumiki,pakati pa amuna amalonda, pakati pa manyumba ogona,kulikonse kumene iwe upita. Kumene iwe uli ndi gulu laamuna, i—iwe umapezako malingaliro osiyana. Ndipo choncho,kotero, iwe umayenera kukhala nayemunthummodzi amene iweungaike chidaliro mwa iye, ndi kumusankha munthu ameneyo.Nonse nkumagwira ntchito ndi ameneyo.

Monga ngati mu ankhondo, inu mumayenera kukhala nayewina monga jenoro, uko ndiye ku likulu. Kaputeni akati izi, iyendi kaputeni wa gulu limenelo, komano jenoro akhoza kusinthakulamulira kwakeko.

Ndipo Jenoro Wamkulu Wolamulira, ndithudi, ndi YesuKhristu, mu Mpingo. Ndipo atumiki Ake ndi makaputeni Ake amagulu, a—amene akumuimira Iye kuno padziko.19 Ndipo iwo ayesera zinthu zambiri, kachisi wamng’onoyukuno. Ndipo potsiriza…ine ndakhala ndiri chete mu izo,kungofuna kuti ndiwone, ine nditatha kumumanga iye. NdiyenoAmbuye anandiitanira ine kuti ndipite kwina ku minda,pafupi zaka fifitini, sikisitini zapitazo, ndipo ine ndinausiyampingowu.

Koma, apobe, ine sindikanati ndingoutembenuzira iwokunja. Ine nthawizonse ndasiya dzina langa likhale pa iwo,chotero kuti ine ndikhoza kukhala ndi voti nthawi zinangati chinthu cholakwika chitayambika mkati muno. Inendingakhale nawo ufulu wobwera n—ndikudzaziimitsa izo,chifukwa ine ndawukhetsera thukuta iwo kwa zaka zambirikuseri kwa guwa lino, zaka seventini mkati muno, kutindisunge chinthuchi mowongoka. Pamene mitundu yonse ya

808 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

timalingaliro ndi zolowa ndi zotuluka, ndi mtundu uliwonsewazotsatira munthu. Ndipo pokhala wa azipembedzo zosiyana,chirichonse chimene chimawulukira umu, chimawulukira mbaliino, ndipo mwa kuthandizira kwa Mulungu ife tinaima pano ndiUthenga wosaipitsidwa, ndipo iwo ukuimabe chimodzimodziusikuuno. Kulondola. Kotero ife…Koma zakhalapo nthawizomwe mpingo uno ayesa kuti awugulitse kuwuchotsa pansi paine, ndi chinthu china chirichonse monga choncho. Ngati dzinalanga likanati lisaikidwe kwa iwo kunoko, nkuti, iwo ndithudiutakhala, uli mu vuto loipa usikuuno. Osati…Ndipo sindinaliine, anali Mulungu, ndithudi, amene anachita izo.20 Ndiyeno, pamene ine ndikuuwuwona iwo tsopano, ukufikapa malo pamene iwo uli, ndipo ife tikukhala mu ora lalikulu,ndi chidwi changa panobe kuti ndiyankhulepo chinachakechokhudza mpingo uno, mukuona, chifukwa n—ndi gawo laine. Ziribe kanthu kaya ine ndiripo kuno kapena ayi, iwoukadali gawo la ine. Ndipo ndi ntchito yanga kuwonapo kutiiwo ukugwira ntchito mwachiyero, momveka, ndi mopambanamomwe ine ndingathere kwaUfumuwaMulungu.21 Ndipo ndine woyamikira kwambiri, kuti, mu masiku ano,ine ndikuwona kuti iwo uli ndi nthambi zazing’ono kwa iwo,chimene ine ndikuchiyamikira. M’bale Crase apa, gulu lake laku Sellersburg; ndi m’bale kumbuyo uko, amene wangotengakumene malo a M’bale Snelling ku Utica; ndi M’bale Ruddellkuno; ndi M’bale Junior Jackson; ndi anyamata ofunika awo,amene ali amuna abwino, amuna odabwitsa a Mulungu. Iwoamalalikira Uthenga uwu. Tsopano, iwo mwina, wina akhozakutsutsa pang’ono pokha pa chinachake kapena chimzake, uwondi umunthu chabe pakati pa gulu la atumiki apobe. Ndipo ngatiatumiki ali ndi kusiyana kwakung’ono, apo sipamakhala m—mthunzi wa kusiyana mu izo.

Mwinamwake wina akhoza kunena kuti, “Inendikukhulupirira kuti Zakachikwi zidzabwera, ndipoYesu adzakhala ali pa kavalo woyera.” Wina nkuti, “Inendikukhulupirira, pamene Iye azibwera, Iye abwera pa mtambowoyera.” Chabwino, bola ngati iwo akukhulupirira kuti Iyeakubwera, icho ndicho chinthu chachikulu, mukuona, ziribekanthu momwe Iye akudzera. Basi, iwo akukhulupirira kuti Iyeakubwera, ndipo akukonzekera izo, ndimwa njira imeneyo.22 Ine ndayesera kuti ndipeze tsopano. Ndipo ine ndakhalandikuphunzira. Ine ndinazinena izo pamaso pa osonkhana. Inendakhala ndikuphunzira za Mpingo woyambirira. Ndipo inendapenya momwe anthu ozodzedwa awo ankakonzeketseraNyumba ya Ambuye, ndi dongosolo la kapembedzedweka Ambuye mu Nyumbayo, ndipo izo zinandikhudza inekwenikweni, mwabwino kwenikweni. Ndipo ine ndinalalikirakuno nthawi ina pakale, ndi pa phunziro la Yoweli 2,“Ine ndidzabwezeretsa, atero Ambuye, zaka zonse zimene

KUTENGA MBALI NDI YESU 809

chimbalanga chinadya, ndi anoni, ndi chirimamine ndi zinazotero.” Ndipo ine ndinayamba kuphunzira pa izo, pa zimeneamuna awa ankachita, ndi momwe iwo anali kuusamaliraMpingo umeneMulungu anawasiyira iwo kuti aziwuyang’anira.23 Tsopano ife tikuti tiyambire ndi Mpingo woyambirira, ndikungobweretsa Izo kwa pafupi maminiti asanu tsopano, mpakaku zimene iwo ankachita, ndiyeno ine ndikhoza kukusonyezaniinu masomphenya amene ine ndiri nawo a za mtsogolo. Tsopano,pachiyambi, Mpingo unatseguliridwa pa Pentekoste. Ndipo ukoMzimu Woyera unagwera pa iwo, kumene Yesu anasankhakhumi ndi awiri. Ndipo mmodzi wa iwo anali atagwa, ndipoiwo anamusankha Matiasi kuti atenge malo ake. Ndipo MzimuWoyera unadikira kufikira zonse izi zitakhalamu dongosolo, Iwousanabwere. Iwo anachita kusankha wina kuti atenge ubishopuw—wa Yudasi, yemwe anagwa pa kulakwa, kuti akwaniritseLemba.24 Ndipo ine ndikukhulupirira kuti zinthu zonse izi zirinayo nthawi yolindira, kudikira, koma izo zikuyembekezeranthawi yoti Lemba likwaniritsidwe, mpaka chirichonse chikhalechiri mwabwino, chirichonse chiri mu dongosolo, chikudikirira.Nthawi zambiri ife timakhala o-…osapirira, ngati mwana.Ife zazikulu…timakhala ndi ziyembekezero zazikulu, ndiponthawi zambiri timalumphira patsogolo kwambiri, ndipo i—izo zimangoyitchinga ntchitoyo, mpaka ntchitoyo imagwidwanazo. Mukuona? Ife timayenera kuti tizingoyenda mwaulemu,tizikhala ndi cholinga mu mtima kuti Mulungu, ngati Iyeangakhumbe kuti atigwiritse ife ntchito mwakuti-n-mwakuti,koma kudikirira mpaka Iye atapanga mpatawo, pakuti Iyeayenera kuti azipita patsogolo pathu.25 Mukukumbukira Davide akupita ku nkhondo usiku ujawo?Iye anali atatopa nayo nkhondoyo, ndipo iye anakagona pansipa mitengo ya nthuza ija kufikira iye atawamva Ambuye mukuwayula kwa masamba, akupita patsogolo pake. Ndiye iyeanapita molimbamtima, chifukwa iye anadziwa kuti Mulunguanali atapita patsogolo pake.

Ndipo ngati ife titangomachita izo, abale. Podziwa kutinkhondo iyenera kubwera, koma ife tiyenera kumadikirirampaka ife titawona dzanja la Mulungu likupita patsogolo pathu,kuti litikonzere njira.26 Tsopano, ine ndikuzindikira momwe mipingo, uvangeliunayambira kufalikira kulikonse. Ndiyeno ife titenga, mwachitsanzo, Paulo kukhala mtumwi wamkulu kwa anthu athu.Ife tikupeza kuti iye anapita konsekonse, kulikonse kumeneAmbuye ankamutsogolera iye, ndipo iye anaukhazikitsakompingo. Ndipo icho chinali Chikhulupiriro chatsopano. Mipingoyamasiku amenewo, mongamuAsiaWamng’ono, konse kudutsamu Ulaya, i—iwo sanali kuwukhulupirira Uthenga umenewo.

810 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

Ndipo pamene iye anachita kumalalikira Uthengawo, ndipoambiri anatembenuzikira kwa Iwo, ndiyeno uko kunalibewina aliyense…Ngati iye akanawasiya anthu mu chikhalidwechimenecho, iwo akanabwereranso kupita kwa milungu yawoyachikunja, ndi mu Chiyuda, ndi zinazonse, chifukwa anthuwoanalibe aliyense woti aziwaphunzitsa iwo. O—otembenuka, iwoanalibe malo oti azipitako, chotero Paulo anakhazikitsa mipingoku mbali zosiyana za dzikolo.27 Uliwonse wa mipingo imeneyi, iye ankamusiyako winaamene anali mu dongosolo, mwamuna yemwe anali wodalirika,mwamuna yemwe ankadziwika ngati m’busa, wolishya. Kapena,ndiye, pambuyo pa mpingo uwu ndiye pamabwera…Mipingoina yaing’ono inkachokera mwa iwo. Anyamata ndi amunaaakulu ankaukapo, ndipo ankakhala mipingo yochokera kwaiwo. Munthu yemwe anali woyang’anira pa mpingo woyambawoankatchedwa bishopu. Ndiyeno ake amene ankapita kuchokerakwa iye, ana ake, anali kutchedwa olishya, kapena abusa.Ndiyeno gulu ili la mipingo yaing’ono yonse inkabwerera kwabishopu uyu.28 Monga mu nthawi ya Ireniya, iye anapitiriza chinthuchomwecho. Marteni anapitiriza chinthu chomwecho. Polycarpanapitiriza chinthu chomwecho. Kupitirira nazo mmusi kudutsamu m’badwowo, iwo anali nazo izo. Ndiyeno mtumwi waMpingowo, mtumwi, ameneyo anali Paulo. Ndipo pamene Pauloanachoka, Yohane anatenga ulamuliro pa Mpingowo. Ndipopamene Yohane anachoka, Polycarp anatenga ulamuliro pa Iwo.Pamene Polycarp anachoka, Ireniya anatenga ulamuliro pa Iwo.Ndi mpaka pansi, Marteni, ndi ena oterowo.

Anali kungopitirizabe kupita mpaka mpingo wa RomaKatolika unadzaswa chinthu chonsecho mu zidutswa,ndipo anawawotcha iwo, ndipo anawabalalitsa iwo. Ndipochimbalanga chinadya ichi, ndi chirimamine chinadya icho.Ndi zina zotero zinadya icho, ndi kudya icho, mpaka iwoanawufikitsa Iwommusi momwe ku phata.

Tsopano, koma, Mulungu analonjeza kuti abwezeretsekachiwiri chinthu icho chomwe.29 I—ine ndikukhulupirira, ndi mtima wanga wonse, kutiife tikukhala mu masiku otsiriza. Ine ndikukhulupirirakuti pali—palibe zochuluka kwambiri zikanati ziswe izi,chirichonse…Ndipo kutanthauzira kwanga kukhoza mwinakukhala kolakwika, pa Malemba, kuti Yesu sakanakhozakubwera usikuuno. Ine ndikukhulupirira kuti zapang’onozimene zatsala kuti zikwaniritsidwe, zikhoza kukwaniritsidwakuwala kwa tsiku kusanadze mmawa, ndipo ine ndikanatindikuwone. Ndipo ine ndikhoza kukhala ndikulakwitsa panthawi ya kukwaniritsika uko, koma izo ziri pafupi. I…inendikukhulupirira zimenezo.

KUTENGA MBALI NDI YESU 811

Ndipo, kumbukirani, Paulo ankakhulupirira zimenezo.Yohane ankakhulupirira zimenezo. Polycarp ankakhulupirirazimenezo. Ireniya ankakhulupirira zimenezo. Marteniankakhulupirira zimenezo. Onse a iwo ankakhulupirirazimenezo.30 Bwanji ngati Mulungu akanamuuza Yohane, mvumbulutsi,“Tsopano, zikhala ziri zaka zikwi ziwiri kusanachitike KudzaKwanga?” Yohane akanabwerera apo ndi kudzauwuza Mpingo,“Chabwino, ine ndikulingalira ife tikhoza kumangodya, kumwa,ndi kumasangalala, chifukwa pakhala pali timibadwo tambiri.”Mwaona? “Yesu sakhala atabwera kwa zaka zikwi ziwiri.”Mwaona? Kotero, mwaona, Mpingo ukanakhala uli wolekerera.Pakanakhala palibe za “pa chikhomo.” Pakanakhala palibekuyembekezera.

Ndipo pambuyo pa zonse, ndi ziyembekezero zanu, ngatiinu mungagone mu ulonda umenewo, kuti inu mudzawuka ndiziyembekezero zomwezo. Chifukwa, izo sizidzatchinga chinthuchimodzi. Inu mudzakakhala muli apo pomwe pa nthawi yake,mulimonse.Mukuona?Mukuona chimene ine ndikutanthauza?31 Tsopano, p—pamene Marteni Woyera ati adzauke muchiukitsiro, Paulo Woyera, onse a iwo, izo zidzangokhalamwatsopano basi ngati kuti iwo anali kumene mu nkhondo,akumeya nkhondo nthawi yomweyo, chifukwa iwo anapita pansiali pansi pa ziyembekezero zomwezo, akuyembekezera KudzaKwake. Ndipo apo padzakhala Kufuula kukubwerapo, ndipoapo padzabwera Mpingo wonse. Inu mukuona? Izo zidzakhalanozimenezo. Kotero, izo ziribe kanthu. Mukuona?32 Ife tiyenera kuti tizimuyembekezera Iye pakali pano,ngakhale. Ife sitikudziwa. I—izo zikhoza kutheka kuti izozikhoza kukhala zaka zana kuchokera pano. Izo zikhozakukhala zaka mazana asanu, zaka chikwi, zaka zikwi khumi.Ine sindikudziwa. Palibe amene akudziwa. Koma, tinene, mwachitsanzo, kuti ife tizikhala tsiku lirilonse, ngati kuti Iyeakanabwera tsiku limenelo. Mukuona? Ngati ife tikanamakhalangati kuti Iye amabwera tsiku lino, pamene ife tiziuka, ngatiife titagona, ndipo ife tiuka mu chiukitsiro, izo zidzangokhalamwatsopano ngati kuti ife tinangogona kumene, titangoukakumene. “Lipenga lidzawomba, okufa mwa Khristu adzaukapoyamba; ife amene tiri amoyo ndi kutsalira tidzakwatulidwammwamba limodzi ndi iwo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga.” Mukuona? Kotero izo zidzakhala ziri zamwatsopano basi.33 Koma tsopano, kufikira nthawi imeneyo, mpaka Iyeatabwera, ife tikufuna kuti tizikhala tsiku lirilonse ngatikuti Iye akhoza kubwera miniti yotsatirayo, chifukwa awoakhoza kukhala mathero a moyo wako pa miniti imeneyo. Iwesukudziwa kuti upita liti. Uwu ukhoza kukhala mpweya wathu

812 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

wina wotsiriza, umene ife tiri nawo mwa ife tsopano, kotero iweukufuna kuti uzikhala ngati kuti iwo uli.34 Koma tsopano kuti tipitirize patsogolo, mopitirira, ifetiyenera kuti tiike moponda mapazi kuno pa mchenga wanthawi, kuti ena azikhoza kumuwona. Ngati Paulo akanatiasachokepo momwe iye anachitira, ndiye Yohane sakanatiadziwe momwe akanati atsatirire. Ngati Yohane akanatiasapitepo, Polycarp sakanadziwa momwe akanati. NgatiPolycarp akanati asapitepo, Ireniya sakanati adziwe momweakanatsatirira, Ireniya akanati asapitepo, Marteni sakanadziwamomwe akanatsatirira. Mukuona chimene ine ndikutanthauza?Aliyense ankayenera kuti aike moponda mapazi pa mchenga wanthawi.35 Chabwino, ngati ine ndikanaganiza kuti panali chipembedzokapena gulu lina lirilonse la okhulupirira, limene linalindi chirichonse chabwinoko kuposa chimene ife tirinacho pano, abwenzi, ine ndikanafuna kulumikizana ndithupi laling’ono ili limodzi nalo mwamsanga kumene. Inendadikira, ine ndakhumba, ine ndakhala ndiri pansi paziyembekezero ndi kukhulupirira kuti wamkulu winawakeanali kubwera tsiku lina, kapena mwinamwake mneneriwamkulu amene ine ndikumukamba adzabwera, wa Elisha. Inenthawizonse ndakhala ndikukhulupirira ndipo ndaganizapo,mwinamwake, kuti mwinamwake ine ndikhala moyo kutindidzaliwone tsiku limenelo pamene ine ndikanati ndidzasinthe,pamene ine ndikanadzamuwona munthu ameneyo akuwukapowonekera, ndiye ine ndikanakhoza kuwutenga mpingo wangawaung’onowu ndi kuti, “Abale, uyu ndi mwamuna amenetakhala tikumuyembekezera. Mwamuna uyu, iye ndi ameneyo.”Ine ndakhala ndikuyembekezera zimenezo.

Ndipo ngati mochitika izo zadutsa, ndiye inendikuyembekezera kuti ndidzanene, kuchokera pamwambaapa, “Abale, uyu ndi Ameneyo,” ndikubwera kuchokeraapa, mukuona. Ndipo i—ine ndikufuna kuwuona mpingoutasungidwa monga chomwecho.36 Ine ndiyenera kuti ndaponda pa chinachake, kapenandachita chinachake, ndipo ndaikamoyowochulukamu chinthuicho. [M’bale Branham asuntha choyankhulira—Mkonzi.]37 Kotero tsopano ine ndikufuna kuti ndinene ichi, kuti,tsopano pakuti uno ndi mpingo wokhazikika.38 Ndiroleni ine ndingoima kachiwiri, mphindi yokha.Pamene ine ndinapita ku Bombay, ine ndikuwuwerengeraiwo kukhala ndi msonkhano wanga wawukulu kwambirichifukwa cha kukhudza kumene iwo unali nako pa anthu.Ndipo i…Ngati mu Afrika, iwo amati zikwi sate zinadzakwa Khristu pa nthawi imodzi, ndiye uko kunali handiredin fifite, kapena thuu handiredi sauzande anadza kwa Khristu

KUTENGA MBALI NDI YESU 813

nthawi imodzi, kuchokera pa theka la milioni ilo kumeneko.Mukuona? Kodi ine ndikanachita chiani? Uko kunalibe kanthu.Kapena, mwinamwake, tinene kuti kunali, tingoti, uko kunalizikwi zana za iwo. Uko kunalibe mpingo, panalibe kanthukamene ine ndikanati ndichite. Uko kunalibe aliyense wotindiupereke iwo kwa iye. Uthenga umene ine ndikuukhulupirira,i…Uko kunalibe ngakhale chipembedzo cha Chipentekostechikanagwirizana ndi ine. Ndipomiyoyo yonse iyomwinamwakeinabwerera mmbuyo momwe kupita ku Chishiite, Chijain,Chibuda, kwinakonse kumene iwo anachokerako. Kunalibemalo oti ndiwaikemo iwo. Tsopano, izo ndi za manyazi. Icho ndichonyazitsa. Mukuona? Chifukwa, ine ndinalibe chigwirizano,chifukwa chamaimidwe amene ine ndimatenga.Mukuona?39 Chabwino, mu Afrika, ine ndinapita uko mothandizidwa,ndi a—a A.F. ya M. ndiyo Afrikaans Faith Missions.Ndipo pamene ine ndinatero, chifukwa, ine sindikanakhozakugwirizana nawo. Iwo, iwo amawabatiza anthu mu ubatizowautatu, nthawi zitatu, nkhope cha mtsogolo. Ndipo umodziwa iwo umabatiza katatu, chammbuyo. Kamodzi ka mulungummodzi, Atate; kenako ka mulungu wina, Mwana; kenakoka mulungu wina, Mzimu Woyera; ndi kumabatiza nthawizitatu zosiyana, kwa amulungu atatu osiyana, ndi zinthu zonsezotero monga izo. Ndipo, mwinamwake, msonkhano wakuDurban, posakhala nawo iwo molondola, ndipo anthu powonakumwazikana kotero pakati pa zikhulupiriro za Achipentekostendi zina zotero, anthuwo sankadziwa choti nkuchita. Iwo analibemalo oti apiteko.40 Mwinamwake, bwanji ngati ife tikanangokhala ndichitsitsimutso kuno, abale? Ndiroleni ine ndiziike izo mongachonchi. Bwanji ngati ife tikanakhala titangodutsa ndichitsitsimutso chachikulu, ndipo inu abale mutangotembenukakumene, ndipo kukanakhala kulibe mpingo wa mtundu uwu mudzikoli, kulikonseko; ndipo ine ndikanakhala ndiri mvangeliyo,ndipo tsopano ine nkuchokako, inu mwina simukanatimudzandiwonenso ine kachiwiri? Kodi inu mukanachitachiyani? Inu mukanamverera ngati kuti inu simukudziwachoti nkuchita. Inu simungathe kubwereranso ku matopeawo kachiwiri. Inu simungathe kubwereranso kumusi uko,n—ndi akazi anu kuti azikavala zazifupi, ndi zanu…ndi kumaphwando anu a njuga ndi zovina, ndi zinthu monga choncho,ndi kumakhutitsidwa konse kachiwiri.

Inu mwabwera ku Moyo. Inu mwakwera pamwamba pazinthu zimenezo. Inu mwafika pa malo, mmalo momati, “Akandi kachikhulupiriro kathu,” mukuti, “Awa ndi Mawu aMulungu.” Ndipo inu mwabwera pomakhala moyo ndi Awa,chimene Awa akunena. Ndipo osati zomwe…

Ndipo inu mukapita uko ndi kumakamvetsera kwa iwo, ndikumawamva iwo akupita uko ndi kumakasewera bunco, ndi

814 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

kumakakhala ndi zovina, ndi izi, izo, ndi zinazo, ndi uthengawa pang’ono pokha umene unalibe kanthu kalikonse mwa iwo,wa za ameya ena kapena chinachake, kapena amene akutiasankhidwenso, kapena mtundu wina wa zochitika zandale, ndikudukiza kaye kwa maminiti khumi kapena khumi ndi asanu;inu mutakhala muli pano, tsiku ndi tsiku, ndi phwando lokhetsadovu laMawundi zinthu. Inu simukanatimudziwe zotimuchite.

Inu mukanamakhala olemedwa kwambiri ndi zimenezo,mpaka ena a inu mamembala wamba mukanamverera ngatimuyambitse mpingo, ndi kuyamba kumalalikira mu Iwo nokha,chifukwa mtima wanu ukanati uzitentha pofuna Mawu aMulungu, ndipo inu mukanati muzimverera moipa chifukwacha anthu amene akanamamverera mwanjira yofanana mongainu mumachitira. Tsopano, kodi uko si kulondola? [Abale ati,“Ameni.”—Mkonzi.]41 Ngakhale inu mutadziwa kuti Yesu akubwera,mukanamaganiza kuti Iye akubwera mawa, komabe inumukanafuna kuti muwachitire chinachake kwa lero anthuawo amene, ndi mbadwa zimzanu za Ufumu wa Mulungu, kutizibwere palimodzi. Inu mukanafuna chiyanjano ndi iwo. Ukonkulondola. Kotero ngati izo ziri mwanjira imeneyi…42 Tsopano, ine ndikukhulupirira ndi mtima wanga wonse kutiAmbuye andithandiza ine ndipo andigwiritsa ine ntchito kutinditsogolere chitsitsimutso chachikulu, chimodzi mwa zazikulukwambiri zimene zinayamba zagundapo mdziko chiyambirenimasiku oyambirira, kudutsa mdziko. Ife tikudziwa zimenezo.Uko nkulondola. Izo zonse zinali zitapita pa nthawi imeneyo,n—ndipo Iye anakakomana nane kumusi uko pa mtsinjendipo anandiuza ine kuti Uthenga umene ine ndinali nawoukanati utsogolere kudza Kwachiwiri kwa Khristu. Ndipo inendikulingalira palibe wina aliyense muno usikuuno ameneanalipo kumeneko tsiku limenelo. Izo zakhala ziri pafupi zakasate-thuu zapitapo, pamene Kuwala kuja kunawonekera; ndiponditaima pamenepo, ine ndikuyang’ana kumene pa Iko. Mazanaa anthu ataima, akuyang’ana pa Iko. Iko kunabwera pansipomwe, ndipo Liwu lija linayankhula.43 Zaka kenako, zodabwitsa kuti kamera inajambulachithunzi chomwecho, chikuwoneka monga chinthu chomwechondendende basi zimene ine ndinakuuzani inu, ku mtsinje kuja.Tsopano, ine mwina ndikhoza kukhala ndikulakwitsidwa muzinthu zambiri, abale, koma ine sindikufuna kuti ndikhalewachinyengo. Ine ndikufuna kuti ndikhale woonamtima ndiwolunjika ndi inu.44 Ndiyeno, chinthu china, ngati ine ndikadachokapo, nchiani?I—ife sitikanati timange tchalitchi kuno ngati icho. Ndi zovutakuti tinene chimene ife tikanakhala nacho, mwaona, ngatiine ndikanangoti ndipitirire. Koma Mulungu wa Kumwamba

KUTENGA MBALI NDI YESU 815

anachiyika icho pa mtima wanga kuti timange tchalitchiichi pano. Ndiyeno pamene Iye anandiitanira ine kunja muuvangeli…Ife takhala nayem’busa pambuyo pam’busa ndi zinazotero, koma tsopano ife tiri naye m—m’bale wofunika panoamene ali wa Chikhulupirirochi, akuukhulupirira Uthengawu.Ife tiri nawo abale ena kunja kuno amene akuukhulupiriraUthengawu. Ali nawo…45 Kodi ine ndikufuula mochuluka kwambiri, M’bale Beeler?[M’bale Beeler ati, “Pang’ono chabe.”—Mkonzi.] Chabwino,tiyeni tiwone. [“Ayi. Pitirirani.”] Eya. Anali…

Ife tiri nazo—ife tiri nazo zidazo.46 Ndipo tsopano inu mukuti, “Chabwino, M’bale Branham,ngati iwo sakuzimva zizindikiro izi ndi zodabwitsa za Mulunguwamkulu wa Kumwamba, ife tizizichita motani izi?” Chabwino,tsopano, bwanji ngati Paulo Woyera akanakhala nalo lingalirolomwelo? Mwaona? Bwanji? Koma iye sanatero. Mabishopuamenewo ankakhala omvera basi kwa Uthenga! Ndipo iwo…Ndipo Paulo, kawirikawiri, akatha kuzungulira kwake…Inumwawerengapo mu Baibulo, momwe iye ankakaichezeransomipingo imeneyi, kukayankhula nawo azibusa, ndi mabishopu,ndi ena otero, ndipo ankakapeza chitonthozo kuchokera kwaanthuwo, n—ndipo ankakhala, o, basi ndi nthawi yaikulu yachiyanjano, monga chitsitsimutso kapena nthawi yaikulu yachisangalalo. Ndipo MzimuWoyera unkakhoza kugwera pa iwo,ndipo mauthenga ankakhoza kubwera.47 Taonani pamene iye anapita uko kwa Filipo, ngakhale anaake aakazi analosera. Ndipo anati, “Kuli unyolo ndi ndendezikumuyembekezera m—m’bale wathu pamene iye ati akafikeuko.” Iye asanachoke mochuluka konse pa malopo, ndipoapa panabwera Agabasi, mneneri, akuyenda apo, kuyang’anapatsidya pa msewuwo. Ndipo anali asanayambe wamuwonapoPaulo ndi kale, mpenyi wamkulu, gulu lonse ili la mipingo kuAsia konseko. Ndipo iye anayenda napita uko ndipo anakakokachingwe kuchichotsa pa mbali yake, iye anali atamangira nachochovala chake, anawamanga manja ake ndipo anati, “PAKUTIATERO AMBUYE, unyolo ndi ndende zikumuyembekezera iyeamene ati avale ichi kumeneko.”Mwaona? Kulosera.48 Paulo anati, “Ine ndikudziwa zimenezo. Ine ndikuzidziwaizo. Komamusati muwuswemtimawanga tsopano. Ndiroleni inenditsirize ulendo wanga.” Iye anali atatopa. Iye anali atathedwa.Ndipo iye anali akupitirira ndi kuusiyira ubishopu wake kwaTimoteo.49 Tsopano ife tikuyenera kuganizira za anthu achichepere. Ifetiri ndi ana. Ambiri a ife anthu pano, amuna okwatira, tirinawo ana. Chabwino, nanga bwanji iwo amene akubwerapowa?Mukuona?

816 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

50 Monga ine ndinkakonda kukankha, kumusi uko, za iwopoziponyera nkhoka izo mu mtsinje, nkumakolamo nkholokoloizo; ndi zakumwa, oledzera ndi zinthu. Ine ndinkaziwonaizo zitaunjikidwa mokwera monga padenga ili apa, zazikulu,nkholokolo zazikulu zabwino ziri pamenepo. Fungo lakelinkakhala liri ku mtsinje wonsewo. Ine ndinkapita kumeneko,ngati wolondera zinyama, kuti ndikawaleketse iwo izo. Inendinalandira kalata, “Asiye iwo okha. Iweyo uchita chiani?Izo ndi za ku Kentucky.” Tsopano, wolondera zinyama wakuKentucky sangathe kubwera kuno, chifukwa iye atuluka ku derala kwawo. Wolondera zinyama waku Indiana alibe kanthu kotianenepo, chifukwa madziwo ndi aku Kentucky. Ndi inu apo.Palibe kalikonse kamene kangachitidwe.51 Ine ndinkati, “Ine ndiri naye mnyamata amene akukula,angadzafune kuti azidzaweza. Ndiyetu, iwo akanati aikechithunzi chake mu pepala ngati iye akanaweza themba, zakatwente kuchokera pano; tikazilola izo kumapitirira mongachoncho, nkhoka zimenezo, misampha, china chirichonse.”Ndipo izo zikufika kwenikweni monga choncho pakali pano.Mukuona? Vuto ndi chiani? Inu mukuyenera kumaganizira zaawa amene akubwerapowa.52 Kotero ife tikuyenera kumaganizira za ena ameneakubwerapowo pambuyo pathu, anthu aang’ono awa, ndi enaotero, ndi malo kwa ana athu. Ana athu aakazi, ife sitikufunakuti iwo azikakhala ukomu dziko, mu zinthu izi monga choncho.Ife tikufuna atsikana amenewo aleledwe monga amayi awo.Ndipo ife tikuyenera kuwakonzeketsera pa izo. Ndipo ngatikulibe mawa, ife sitikudziwa izo. Ngati kulibe mawa, ifesitinachite kanthu koma takhala tiri pa ntchito yaAmbuye ndipotipezeka tiri pa malo athu a ntchito pamene Iye ati azibwera.Mukuona?53 Kotero, ine ndikanati ndipereke lingaliro ili. Ine ndinatero,kwa M’bale Neville. Tiyeni tizipitiriza izi patsogolo basi mongaife takhala tikuchitira. Tiyeni tizilole izo basimomwe izi ziriri.

Ndine woyamikira chifukwa cha atumiki aang’ono awa.Mukuona, makamaka, pa Tsiku la Chiweruzo, kwa zigwa zonseizi kudutsa kuno, sipadzakhala pali chowilingula, chifukwaife tiri nayo mipingo yaing’ono ikukhazikika kulikonse uko,yoyang’anira kwina,malo omvetsererako, akuyembekezera.54 Usiku watha ine ndinali mu mpingo wa m’bale, ndipondinafunsa ngati onse mmenemo anali otetezedwa paseri paMawu. Ndipo nkono uliwonse unakwera mmwamba. Tsopano,izo zinandipangitsa ine kumverera bwino. Mwaona?55 Tsopano, chimene ine ndikanati ndiganize, chinali ichi,abale, kuti monga mu mpingo kuno tsopano. I…u…Utumikiwanga wakhala, mwakupambana kwa kuganiza kwanga, zinthuzinai zimene zingati zichitidwe. Ndipo izo mwina zikhoza

KUTENGA MBALI NDI YESU 817

kusakhala zinai, koma awo ndimawonedwe a zinthu okha ameneine ndingathe kuwaganizira; ngati Ujayu amene anayankhulakwa ine kumusi kuja pa mtsinje, ngati izi ndi zonse zimenezinatsalira kwaMpingo wa Amitundu.

Chimene, ife tikuzindikira, mu Chivumbulutso, ndi mituwani, thuu, firii yokha kwa Mpingo. Mpingo ukukwerammwamba, mu mutu wa 4. Iwo suli kubwerera kenanso mpakamutu wa 19, apo ndi itatha Nthawi ya Chisautso pameneMulungu akuitanapo Ayuda. Ndiko kulondola.56 Ndipo monga Enoki, iye anapita mmwamba dontho limodzila mvula lisanagunde konse dziko lapansi. Iye anali atapita,kenako chisautso chinayambikamo. Mukuona? Nowa analimu chombo chisanayambike chisautso chirichonse. Loti analikunja kwa Sodomu chisautso chirichonse chisanakhale umo.Mukuona? Ndipo Mpingo udzakhala utapita isanafike Nthawiya Chisautso iliyonse.57 Tsopano, mu nthawi ya Chisautso awo adzakhala ali,namwali wopusa adzakhala akusakidwa ndi chinjoka, ndikumalavula madzi kuchokera mkamwa mwake, zimenezikutanthauza, “unyinji ndi anthu,” ankhondo ameneadzamfunafuna ndi kumtenga mkazi uyu, otsalira a mbewuyake, ndipo adzamupha iye. Tsopano, izo zidzakhala ziri muNthawi ya Chisautso.

Koma Mpingo udzapita Kwawo. Tsopano, ng—ngati izozitenga, zikanati zichitike mawa, izo sizikanati zititchinge ifekuti tizipitirira lero. Tiyeni tipangitse lero kuwerengedwa.58 Tsopano, zimene ine ndikuganiza, kumusi kuja, ngatiMngelo uja amene ananena Mawu aja kwa ine, nati, “MongaYohaneMbatizi anatumidwa kuti adzatsogolere Kudza koyambakwa Khristu,” mukuona, “Uthenga wako…” Ine ndinali wotindiutenge Uthenga uwu. “Ndipo Iwo ukanati utsogolere Kudzakwachiwiri kwa Khristu.” Chabwino, ngati Izi zakhala ziriZimenezo, ndiye ife tiri kwenikweni, pafupi kwenikweni, abale,chifukwa ora ndi Kuwala kwaUthenga zangotsala pang’ono kutizifike pakutha.59 Kodi inu munazindikira pamene Pentekoste inagwa, ndipoabale amenewo anadzazidwa pa Pentekoste, ndi MzimuWoyera?Izo sizinali nkomwe nthawi iliyonse mpaka kuti Uthengaunayamba kuzirara, ndipo iwo anayamba kukhazikitsa mipingokuti igwire linga, la Khristu, kuyembekezera kuti Iye abwere.Chabwino, ndi chinthu chomwecho chimene chikuchitika lero,ngati Lemba liri loona, “Ine ndidzabwezeretsa, atero Ambuye,zonse zimene achirimamine ndi chimbalanga zinadya.” Tsopano,ngati izo ziri zimenezo, ngati umenewo uli Uthengawo, ndipo,Mulungu andikhululukire ine, i—ine sindiri kudziwa. Ngati izoziri zimenezo, ndiye nthawi ili pafupi poyandikira, kwenikweni,chifukwa Uthenga watha.

818 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

60 Ndipo usiku wina, ine ndinali kulota kuti ine ndinapitakukakhala ndi kuzindikira za mumtima kumene khamu lalikulula abwenzi anga anali atasonkhana, zikwi za iwomumsonkhano.Uko kunali munthu yemwe anabwera, ndi kudzanditengeraine umo. Ndipo Billy kawirikawiri amabwera, kudzanditengaine, chifukwa inu simumayankhula kwa ine. Ndipo bambouyu ankangoyankhula mosalekeza. Ndipo ine ndisanakafikekumeneko, kudzoza konse kunali kutandichokera ine, kwaizo. Ndiyeno ine ndinati, “Chabwino, ine ndingopita ukon—ndi kukalalikira Uthenga, wa kuwauza anthu amenewo,‘Musamapusitsidwe ndi zipembedzo izo,’ ndi zina zotero, ndi,‘Tulukanimo, monga chonchi.’” Ndipo pamene ine ndinafika kunsanja, izo zinali zitandichokera ine.61 Ine sindikudziwa chomwe izo zinkatanthauza, koma inendinali kupitirirabe nazo. Ine sindikudziwa basi. Awo akhozakukhalamathero amseuwanga. Uko kukhoza kukhala Kubwerakwa Ambuye. Uko kukhoza kukhala kusintha kwa tsiku.Uko kukhoza kukhala kubwera kwa wamphamvu uja, ngatipati padzakhale wina pambali pa amene wabwera kaleyu.Izo zikhoza kukhala zimenezo. Zinthu zonse izo, ife tiyenerakuti titenge kuchokerako, izo zikanakhoza kukhala. Ndipopamene ine ndaima pano usikuuno, pamaso pa Mulungu ndiinu abale, ine sindikudziwa. Ine sindikanatha kukuuzani inu.Ngati ine ndikanatero, ine ndikanakuuzani inu, kapena inesindikanatchula, kubweretsapo chirichonse chonga ichi, ngatiine sindikanati ndidziwe njira yake. Ngati ine ndikanaidziwanjira yomwe chinthucho chinali kupita, i—ine ndikananenaizo, koma ine sindikuidziwa. Ine sindingathe kukuuzani. Inendikupita pakali pano pa misonkhano mopanda chidutswachimodzi cha kutsogolera. Ine ndikupita chifukwa inesindikufuna kuti ndikhale ndiri apo. I—i—ine ndimakondakumapita kwina kuthengo chimodzimodzi ndi aliyense. Ngatiine ndikulakwitsamu izi, Mulungu andikhululukire ine.62 Pali zinthu zitatu zimene zikanakhoza kuchitika kwa ine.Awo mwina ndi mathero a mseu wanga, ndipo msiyeni wina uyuabwerepo; ine ndamutsegulira iye mseu kuti atenge ulamuliro,chifukwa, kumbukirani, amene akubwerayo kuti azidzalalikira,adzakhala ali pa Mawu, “Kubwezeretsa Chikhulupiriro chaana kubwerera kwa makolo.” Awo akhoza kukhala mathero aulendo wanga. Izo zikhoza kukhala kuti Iye akusintha utumikiwanga kuti ndibwerere ku uvangeli, waku tsidya kwa nyanja.Kapena, izo zikhoza kukhala kuti Iye sandiitana ine kenansongati mvangeli, ndipo Iye akunditengera ine ku chipululukwinakwake, kuti akandidzoze ine, kuti akanditume ine apongati iye wolonjezedwa amene ali nkudzayo, ine ndikuganiza.Izo zikhoza kukhala chirichonse cha zinthu zimenezo.63 Ine sindingathe kumapitirira momwe ine ndakhalandikupitira. Chifukwa ndine…Anthu andikhulupirira ine.

KUTENGA MBALI NDI YESU 819

I—ine ndiyenera kuti ndinene izi. Ine ndikunena izi pamasopa amuna. Anthu, nthawi zambiri, amanditenga ine ngati kutindine mneneri. Ine sindimadziwona ndekha chomwecho. Ayi,bwana. Ine sinditero. Ine ndakhala…Ine sindikunena izo kutindikhalewodzichepetsa. Ine ndikunena izo kuti ndikhalewoona.Ine sindimadziwona ndekha kuti ndikhale mneneri wa Ambuye.I—ine ndiribe ulemu umenewo.64 Ine ndikukhulupirira kuti Ambuye andigwiritsa ine ntchito,mu zinthu pang’ono zapadera, kuti ndithandizire mwinamwakekuyika maziko a mneneri yemwe ati abwere. Koma mnenerisamagwira ntchito momwe ine ndikuchitira. Tsopano, inumukudziwa zimenezo. Mneneri si mvangeli, ndipo mvangeli simneneri. M’busa si mvangeli, ndipo mvangeli si m’busa. “KomaMulungu waika mu Mpingo, poyamba atumwi, kenako aneneri,kenako aphunzitsi, kenako abusa,” ndi ena otero. Mulunguanawaika iwo mu Mpingo, ndipo Mulungu anawapatsa iwoudindo.65 Koma, mmawa umene ine ndinkaika mwala wapangodyauja! Chifukwa, tsopano, ngati muli auzimu, inu muzimvetsa izo.Chifukwa cha kulira kwa anthu! Ngati inu mungathe kuswaapo, kapena kulitenga bukhulo ndi kuziwerenga izo, ilo linati,“Zichita ntchito ya mvangeli.” Sanandiitane ine kuti ndikhalemvangeli, koma anati, “Zichita ntchito ya mvangeli, pakutinthawi idzabwera pamene iwo sadzapirira nacho Chiphunzitsochomveka, koma adzaziunjikira okha palimodzi, aphunzitsipokhala ndi makutu oyabwa, ndipo adzapotoloka kuchokakwa Choonadi kupita ku nthano.” Mukuona? AnabwerezaLemba limenelo ndipo anandiuza ine pamene ndingazipezeIzo. Ananena Izo katatu. Ndipo ine ndinatenga Baibulondipo ndinatembenuzira pamene Iye anandiuza ine, ndipo izozinali apo. Ndiyeno inu mukudziwa za zibekete ziwiri, zaUmodzi wa Chipentekoste ndi Apentekoste a Assemblies. Inesindinawabalanitse iwo. Ine ndinabyala mitengo yawo yawoapo pomwe iwo anali, chifukwa ine ndikuganiza onsewo alikulakwitsa. Koma, kuchokera mu izo, ine ndinali pa mtanda, pakukolola.66 Mulungu amamulemekeza aliyense amene ali woonamtima.Petro ananena zimenezo. “Iye anazindikira kuti Mulungu sanaliwolemekeza munthu, kumafuko onse akuitana, pamene anali kunyumba ija ya Kornerio, pamene iwo analandira Mzimu Woyeramomwe iwo anachitira pa chiyambi.” Mukuona? Mulungusamalemekeza munthu. Ife timawona munthu wozama ndiwoonamtima, iye akhoza kukhala woonamtima molakwika.Koma ngati iye ali woonamtima, Mulungu adzamutsogolera iyeku Kuwala, kwinakwake. Iye adzabwera kwa Iko, chifukwaMulungu ndi wokakamizidwa kuti achite zimenezo.67 Ndipo ife tikuganiza za Kudza kwa Ambuye, pokhalachotero—chinthu chachikulu; ndipo Uthenga, suli kuposa

820 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

Umene unapitapo. Kumbukirani, pali gulu lokonzedweratu lotilikhale liri kuno pamene Ambuye azibwera, ndipo iwo mwinasangakhale oposa khumi ndi awiri. Mukuona? Ife sitikudziwa.Iwo akhoza kukhala mamilioni zana; akhoza kukhala zikwikhumi. Koma ngati…Okonzedweratu adzaumva Uthengawondi kuukhulupirira Iwo, ngati Uwu uli Uthenga wotumidwa ndiMulungu, chimene ife tikukhulupirira kuti Iwo uli.68 Tsopano, ife tiri apa, ndiye, apa pomwe mpaka kutha kwanthawi. Pamene, ngati Mulungu anandiitanadi ine…Tsopano,mvetserani, izi si zoti zibwerezedwe. Ngati Iye anandiitanadi inekuti ndikhale mneneri Wake, ndiye ndithudi ine sindikugwiraudindo wa iye. Aneneri samachita uvangeli. Mneneri amadzibisayekha mu chipululu, kwa yekha, ndi Mulungu, kufikira iyeatapeza ndendende, molunjika chimene Mulungu akufuna kutiiye achite. Ndipo iye amatulukira mwamdidi apo ndi kuperekaUthenga wake, ndipo kubwerera ku chipululu iye amapitakachiwiri. Iye si mvangeli, kumachititsa misonkhano, ndikumapeza migwirizano, ndi zinthu zonse izi momwe avangeliamachitira. Iye samaphunzitsa ngati avangeli. Iye amakhalandi PAKUTI ATERO AMBUYE, ndipo ndi zokhazo, ndipondizo zonse. Iye amazipereka izo, amaponyera izo panja, ndikulola zibanthu zizigwera kumene zingathe, ndiyeno kwina iyeamapita kachiwiri. Palibe amene amadziwa kumene iye ali. Iyeamakakhala modzipatula, kwinakwake.69 Tsopano, ine sindingathe, kapena ngati Iye anandiitana inekuti ndikhale chimenecho, ine sindingathe kukhala mvangeli.Ndipo ngati Iye anandiitana ine kuti ndikhale mvangeli,ine sindingakhale ndiri mneneri. Tsopano, inu mukumvetsazimene ine ndikutanthauza? Ine sindikudziwa choti ndichite. Inendachita, molemekeza, pamene Iye anandiuza ine, poyamba, zakumagwira dzanja la anthu ndi kumawapempherera iwo, ndiyenkumadziwa chinsinsi cha mtima wawo, zinthu zonse zosiyanaizi. Ndipo, abale, izo ndi zosalephera. Inu mukudziwa kuti izondi Choonadi. Aliyensewa inu akudziwa zimenezo.Mukuona?

Ndi momwe Iye anandiuzira ine kuti Iwo ufala kudutsamdziko lonse, ndipo Iwo wachita izo ndendende basi!Fuko lirilonse pansi pa miyamba lamvapo Iwo, kulikonse,manyuzipepala, kujambula kwa matepi, kulikonse. Inesindikudziwa momwe Iwo wachitira izo konse. Koma,konsekonse mdziko lonse, makalata akumabwera kuno,ndipo anthu kuchokera kutali komwe uko mu Thailand, ndikwa Akafula mpaka kumeneko. Momwe aumishonare awoadzaziranira kumeneko ndi matepi amenewo, ndi kumaperekaapo kutanthauzira kwa Mawu. Ndipo tsopano ife tikumvakuchokera konsekonse mdziko, mukuona, kuzungulira mdziko.Tsopano, iwo, Mpingo, ndi wokonzedweratu kulikonse,konsekonse. “Adzakhala awiri pa kama; awiri mmunda,”mukuona, kutengammodzi ndi kusiya mmodzi.

KUTENGA MBALI NDI YESU 821

70 Tsopano, monga ine ndachitira ntchito ya mvangeli. Ndiponali pempho langa. Ngati izo ziri zomukondweretsa Mulungu,ndipo ine ndaichita ntchitoyo bwinobwino, ndikudalira kuti inendimamukondweretsa Iye, ndikupempha chikhululukiro kwazolakwitsa zanga zonse, ndiye Iye akhoza kuti akundiitana inekundichotsa ku munda wa uvangeli, kuti ndikhale mneneriWake. Ndiye ngati ziri zimenezo, ine ndisiya uvangeli. Komangati Iye akundiitana ine kuti ndikhale mneneri, ine sindingathekukhala mvangeli. Ngati ine ndiri woti ndikhale mvangeli, inesindingati ndikhale mneneri.

Ine ndikusakaniza maudindo awiriwo. Ndi pamene inenthawizonse ndakhala ndikukangana napo. Ndikaima pansanja, izo sizinayambe zakhala zabwino, zochita mopambana.Mulungu wazigwiritsa ntchito izo, koma ine sindinayambendaganiza kuti icho chinali chifuniro Chake cholunjika.Icho chakhala chiri chifuniro Chake chongololera. Ndikaimapa nsanja, masomphenya kapena awiri amakugwetsa iwe,pafupifupi. Mukuona? Ndiyeno ngati iwe umuuza munthu uyumomwe angadzikonzere yekha, ndi zoti achite; ndiyeno munthuwotsatira kuima apo, iye akuyembekezera chinthu chomwecho.Ndipo iwe sungathe kumuuza iye kupatula Chinachakechitakuuza iwe kuti umuuze iye. Ndiyeno anthu enawoamamverera ngati kuti ndiwe wokondera, kapena wobwererammbuyo, k—kapena chiwanda kapena chinachake, chifukwa iwesukuwawuza iwo zimene iwo akufuna kuti azidziwe. Mukuona,uwo si udindowo, momwemneneri amachitira.

71 Mneneri amakhala kuseri kuno mpaka iye atakafika kuchipatala, kapena kulikonse kumene iye apita, ndi PAKUTIATERO AMBUYE, ndipo amakanena izo, ndi kubwereransommbuyo. Iye si mvangeli, konse. Iye samachititsa misonkhanondi kumakambirana zinthu. Iye ali ndi Mawu a Ambuye kwaaliyense yemwe iye watumizidwako.

72 Ngati iye watumidwa ku White House, iye amakafikakumene patsogolo pa White House, ndi “PAKUTI ATEROAMBUYE.” Ngati ziri za kwa kazembe wa chigawo, aliyenseamene ali, ndi PAKUTI ATERO AMBUYE. Iye samadzipusitsandi gulu la mipingo, kuyesera kuti afike powabweretsa iwomkati ndi kuwatenga Mawu, ndi kumalalikira zinthu izi mongamvangeli. Iye si mvangeli.

73 Kotero, inu mukuona, abale, ndicho chifukwa inesindimadzitcha ndekha mneneri. Ine sindiri konse mu udindowa iye. Mukuona? Tsopano inu mukumvetsa zimene inendikutanthauza?

Tsopano, pangakhale zochuluka zomwe zikuchitika mongachoncho kwa nthawi yaitali, koma ine ndikuyembekeza kutindisatenge nthawi yanu yochuluka kwambiri, mpaka ine

822 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

nditenge pang’ono pokha pa Mawu awa amene ine ndikufunakuti ndiwawerenge usikuuno.74 Tsopano, izi ndi zimene ine ndikuchita. Ine sindinayambendamvererapo kuti ine ndizikhala mu Indiana. Ndine—ndinewo—woyendayenda. Ine sindima…Ine ndimapita ku maloamodzi, ine ndimaganiza, “Ine ndipita uku, ine ndikakhazikikauku. Izi ndizo.” Ine sindingathe kuchita izo. Pamene ine ndipitakwinakwakenso, ine ndimaganiza, “Ine ndipite uku.” Pameneine ndichita izo…

Mkazi wanga amanditcha ine…Ndi nyimbo yanji ijaimene iwo amaimba? Mphepo Zosakhazikika. Inu munaimvapoiyo, ine ndikulingalira. Pafupi nonse a inu munawamvaiwo akuiyimba. Chabwino, ndi chimene iye amanditcha ine,“Mphepo Zosakhazikika.”

Pafupi nthawi imene ine ndifika kuno, ine ndimaganiza,“Mnyamata, ine ndikungoyenera kuti ndikafike kwathu.Ine ndikuyenera kuti ndikamuwone mkazanga ndi ana. Inendikungoyenera kuti ndipite ku tchalitchi kamodzinso ndikukalalikira.” Ine ndikafika kuno, ndi kubwera kudzalalikirakamodzi. Kumupsyopsyona mkazi wanga ndi kuwakumbatiraana onse. Kupita kuseri ndi kumakatchetcha udzu, ndipondege imauluka pamwamba panga. Ine ndimaima, ndikupukuta thukuta pa nkhope yanga, ndipo ine ndimafunakuti ndipite nayo iyo. Kwinakwakenso ine ndimayenerakuti ndipiteko. Chabwino, ine ndimaganiza ine ndikuyenerakuti ndipite kumeneko. Ndipo i—ine ndikapita kumeneko,ndipo ine ndimakalalikira uko kwa kanthawi. Kuyang’anapozungulira, apo pakuulukanso ina mmwambamo. Inendikuyenera kuti ndipite nayo iyo. Mukuona, palibe malookhazikika kwa ine. Ine sindingathe basi kuchita izo. Ndinewosakhazikika, wosunthasuntha, malo ndi malo, chinachake.Ine sindingadziletse izo. Ndi chinachake mkati mwanga. Ndipoine ndimadziwa kuti ine ndimayenera kuti ndichite zimenezo.75 Tsopano, ku mpingo, momwe iwo uliri pakali pano,ine ndingamverere moyipa kuti ndichokepo pano. Ndipo,ndikaganiza, za amuna nonse inu mwakhala pano, ameneine ndikuganiza kuti ndidzakakhala nanu Mmuyaya, ukoku dziko Laulemerero. Ife tiri nawo amuna abwino, zidazabwino, okhazikika, anthu ochita zabwino. Posachedwapakunali chitsitsimutso chinafalikira muno mu mpingo kunopakati pa anthu. Mzimu unabwera pakati pa iwo, unayambakupereka mphatso. Ine ndinali kuuyang’ana iwo, kuti ndiwonengati izo ziti zipite mu zotentheka. Nthawi iliyonse iwoakayamba kusunthira njira imeneyo, Mzimu umaziletsa izondi kuzibweretsanso izo kuno. Ine ndinaganiza, “Ambuyealemekezeke.” Mukuona? Inu ingogwirani malo anuwo apo. Izoziri bwino. Mukuona?

KUTENGA MBALI NDI YESU 823

76 Tsopano, chimene malingaliro anga ali, ndi ichi, ngatikungakhale kotheka kuti, pamene ine ndiyamba kupitakwinakwake, ine sindimadziwa kumene ine ndikupita. Komaine sindingathe kukhala phee. Ine sindikhala ndiri kuno. Inesindingathe basi kuchita zimenezo. Ine ndiyenera ndisunthirekwinakwake. Ndipo mwinamwake ine sindingakakhalekumeneko koma masiku owerengeka, ndikhala ndikusunthirakwinakwakenso. Ine ndimayenera kuti ndipite kwinakwake. Inesindidziwa kumene ine ndiri kupita. Ngakhalenso Abrahamusankadziwa kumene anali kupita. Iye anangowoloka mtsinje ndikuuyambapo. Ndizo zonse.77 Ine ndikumverera kuti zimene ife tikuyenera kuti tizichitakuno, mu nthawi ino, ine ndikukhulupirira kuti ife tikusowatchalitchi. Ine ndikuganiza—ine ndikuganiza nyumba yaMulungu…Inu mukati, “Chabwino, chifukwa chiyani, kuikandalama zonsezo mu zimenezo ngati Ambuye ati abwere?”Chabwino, nchaubwino wanji kusunga ndalamazo ngatiAmbuye akubwera? Mukuona? Ndipo ngati anthu aziikandalamazo kuti zikhale za tchalitchi, ndi ntchito yathu ndivoti ya zana pa zana kuno, imene ine ndinaipanga usiku ujawu,kuti timange tchalitchicho. Kotero, mangani icho. Ine ndikuti,mangani icho. Inde, bwana.78 Ine sindinayambe ndafotokozapo izi ndi kale, komaine ndikufuna kuti ndichite izi pamaso pa inu amuna.Sindinawafune akazi muno, chifukwa wina amatsamira mbaliiyi, ndi mbali iyo. Tsopano ine ndikuyesera, kuti ndikuuzeniinu chifukwa chimene ine ndikufunira kuti tichite izo.Ine ndikuganiza, ngati Ambuye akubwera sabata yamawa,tiyeni tichiyambe tchalitchicho sabata ino. Ndithudi. Tiyenitimusonyeze Iye. Tiyeni tiyime pa malo athu antchito. Inde,bwana.Ndiyeno ngati ife…pamene tchalitchi chimangidwa.79 Bwanji? Titi ngati Iye…Bwanji ngati Iye ali zaka khumikuchokera pano? Bwanji ngati Iye ali zaka makumi awiri?Kapena bwanji ngati Iye ali zaka zana? Chirichonse chimenechiri, pamene Iye ati abwere, izo ziribe kanthu. Ife tikudziwakuti Iye akhala akutidzera ife isanafike nthawi imeneyo,chifukwa ife sitingathe kuzikhala izo konse, zaka zana zina.Iye akhala akudzera ife, koma ife tiyenera kuti tisiye malekanommbuyo mwathu. Ndipo ine ndaganiza izi. Nanga bwanjiosalilola gulu la mpingo kuno, kuyankhula kwa iwo tsopano,amange tchalitchi chimenecho? Achiimike icho pano. Achipangeicho chikhale chabwino, ndi malo abwino kumene anthu akhozakumabwerako.80 Ine ndikunenapo, kuti M’bale Neville akhale m’busawa tchalitchicho, utali wonse pamene mpingo uti unenekuti iye akhale m’busa. Imeneyo ndi voti ya mpingo. Utaliwonse pamene iye azigwira malo a ntchitoyo ndi kukhalandi Chikhulupirirochi, akufuna kuti abwerepo, akumverera

824 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

kutsogolera kwa Ambuye, ndiye kutsogolera kwa Ambuye nkotiiye akhale nako, ngati mpingo umuvotera chimodzimodzi.81 Ndiye ine ndikuti, aliyense wa amuna awa kuno, amunaena awa, monga M’bale Crase, ndi M’bale Junior, onse aiwo, utali wonse pamene iwo akumverera kuti ndi ntchitoyawo pa malo amenewo, ndipo iwo akuthandizana nafe kunopalimodzi. Inu simungathe kupita uko ndi kumakakomana ndiAmethodisti. Inu mulibe chiyanjano ndi iwo. Abaptisti, inumukapita, ndi kumakayankhula za kuyankhula mu malirime,ndi ubatizo mu Dzina la Yesu, iwo akakukankhirani inu panja,mwamsanga chomwecho. [M’bale Branham akhwatchitsa chalachake—Mkonzi.] Uko nkulondola. Iwe ukhoza kukakhalakumeneko, iwe uzikakhala ngati—nkhunda pakati pa gulula akhwangwala. Iwe sukakhala ndi chiyanjano, konse.Iwe ukafa. Ine sindikuwatonza Amethodisti ndi Abaptisti,tsopano. Kumbukirani zimenezo. Ine sindikunena zimenezo. Inendikungopanga kufanizitsa. Alipo, ambiri, Amethodisti awo ndiAbaptisti amene ali amuna abwino, amuna aumulungu. Komaine ndikuyankhula za chiyanjano. Pali M’bale…

Dzina lake ndi ndani? Kumbuyo uko usikuuno, m—mlalikiwakhala kumbuyo uko, M’bale J.T. Parnell. M’bale Beeler,ndikukhulupirira, m’bale uyu wakhala apa. Ena a…Ambiri ainu pano ndinu amuna a Mulungu, kuitana mu moyo wanu.Inu mukanakhoza kumachita chinachake. Musati muzingokhalapansi. Tiyeni tizichita chinachake. Inu simukupeza kuposamoyo umodzi wokha utapulumutsidwa, mfikitseni ameneyopopulumutsidwa. Aliyense wa ife.82 Tsopano, ine ndikuganiza, mpingo uno, ngati amuna inumungati, pamene inu muzimanga tchalitchi ichi, muchipangeicho ngati likulu lanu, ndipomongaM’baleNeville kuno pokhalangati mkuluwa akulu pakati panu.Mukuona? Ndipo nthawizinainu muzipeza funso limene inu simungathe kulikambirana ndimpingo wanu kumeneko, ndiye zilibweretsani ilo kuno kwaM’bale Neville, ndipo inu nonse muzikambirana ilo palimodzi.Ngati inu simungathe kufika pa kugamula kulikonse, inendizikhala ndikubwerapo, mwa posakhalitsa, ndiye ife tonsetizibwera palimodzi ndi ilo.83 N—ndiyeno, mmenemo, ziwaphunzitsani mu magulu anuomwe, atumiki ena, amuna amene inu mukuwaona kuti alinako kuitana mu moyo wawo, kwa utumiki. Ziwaphunzitsaniamuna aang’ono amenewo. Ziwabweretsani iwo kuno kwamkuluyu. Nonse inu mutakhala palimodzi mu msonkhano waazitumiki, ndipo pamenepo ziphunzitsani zinthu zakuya zaMulungu. Musati muzipita ku mathero oipa. Zikhalani nayewinawake yemwe mungakhale nacho chidaliro mwa iye, kutiazikhala ngati—mtsogoleri wa inu. Ndiyeno, nthawizina, ngatiinu simukuziwona izo ndendende basi momwe iye akuchitira,amapita, izi ziri bwino basi. Inu muli mu Chikhulupiriro,

KUTENGA MBALI NDI YESU 825

mulimonse. Basi zisunthirani patsogolo. Mwinamwake pameneife tidzabwera palimodzi, ndiye, tonse ife palimodzi, ifetidzapemphera; kuzindikira za mumtima kwa Mulungukudzabwera apo, ndipo Iye adzazipereka izo ndendende basichimene icho chiri, inu mukuona, ndi kudzatidziwitsa ifemomwe tingamachitire izo.84 Ndipo mmenemo, mipingo ikhoza kumapita kukamvetsera,ndi kumaliphunzitsa gulu la amuna. Ndipo ngati ine ndiri muntchito ya uvangeli kwinakwake, pali malo amene ine ndingathekukawaikako iwo, ku dziko lonse.85 Nanga bwanji ngati ine ndikanakhala ndiri ku India,kubwerera ku India? Kumeneko ine ndikanati ndinene kwaanthu awa, mwinamwake, ndikanakhoza kukhala nawo zikwiza iwo. Kukakhala kumeneko kwa sabata kapena awiri,ndipo iwo nkuwuona utumikiwu. Iwo nkuukonda iwo. Iwonkuukhulupirira iwo kuti ndi Choonadi. Iwo nkutuluka kuchikunja. Kumeneko ine ndiri…ndipo mwinamwake mumasabata awiri kapena atatu.

Pamene ine ndinali kumeneko, usiku uwiri, ndimwinamwake ote mbenuzidwira kwa Khristu zikwi zana;analibe kwina koti azipitako. Tsiku lotsatira, nkukwera ndegendi kuyamba kubwerera ku Roma, kenako ku United States.Kungowasiya iwomonga nkhosa pakati pa ankhandwe.

Bwanji ngati ine ndikanakhala ndi gulu la amuna, amunaachichepere ophunzitsidwa mu Uthenga, mukuona, ndikanati,“Tsopano, dikirani miniti. Ine ndisanachoke kuno, ife tiika mudongosolo mipingo imeneyi. Ine ndikhala naye munthu. Inendamutumizira kale uthenga iye. Iwo ali nazo ndalama. Iwoali pa msewu akubwera kuno, pakali pano, kuti adzatengeulamuliro pa izi; munthu wabwino. Ali ndi anyamata awirikapena atatu naye amene ati akhale omuthandizira ake ndiogwira naye ntchito”?86 Ndipo mpingo wa Chikhulupiriro ichi ukhozakukhazikitsidwa kumeneko, umene ungakhale malo a kunjamu India, malo a kunja mu Germany, malo a kunja muSwitzerland. Mwakuti, pakali pano, ife tikanakhala nawoiwo konse kuzungulira mafuko kumene ine ndakhala ndiri.Ndipo Uthenga ndiye, kuchokera kumeneko, nkubwera wina,kuchokera kwa wina iwo kubwera wina. Mukuona chimene inendikutanthauza? [Abale ati, “Ameni.”—Mkonzi.]87 Tsopano, mawa usiku, kapena nkucha usiku, inumudzamuwona Mattsson-Boze akubwera kunoko, ameneali bwenzi wanga. Inu mudzawona basi zimene mmodziwamng’ono, wa Chiswede wolumala anakachita ukoku Tanganyika. Iye anapita mmenemo. Ndipo, tsopano,Mattsson-Bose ndi bambo wabwino, koma iye sakhulupiriraChikhulupiriro chimene ife tikukhulupirirachi.

826 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

88 Ine ndamutengera iye panja pomwe, ndipo ndinamutenga iyendi kungomumangira iye pa malo oterowo mu Lemba. Ine nkuti,“Mattsson, iwe ndi mzanga. Tsopano iwe sulumpha kapenakuthamanga. Ife tingoima pano, ndi kugwirana dzanja wina ndimzake, ngati abale Achikhristu, ndi kuyankhulana.”Mukuona?89 Ndipo ndinayalira Uthenga kumene kwa iye, ndipo iyeanangoima pamenepo. Iye anati, “M’bale Branham, i—inundithudi mukulondola.”90 Ine ndinati, “Tsopano, Mattsson, iwe sukukhulupirira izo,kapena iwe ukanazilandira Izo.”91 “Chabwino, M’bale Branham, i—ine ndikukhulupirirazimene inu mukunena kuti ndi Choonadi.”92 “Ndiye nanga bwanji iwe sukuzilandira Izo?” Mukuona?Ndinangomuwotcha nazo kumene Izo kwa iye. Ndipo i—iye, ndiye, mwamsanga pamene iye anachokapo, iye wapita.Mukuona?93 Koma mungopenya zimene munthu ameneyo anachitauko mu umishonare wake kumenekoko, munthu mmodziyekha. Chifukwa, iye amakhoza kutumiza ku Chicago ndikukamutengako Burton ndi onse awo, ndi kuwatumizaiwo kumeneko monga choncho, ndi kukayamba kugwirantchitoyo. Mpaka, tsopano iwo akufika mu makumi a zikwi,a chitsitsimutso chimodzi chaching’ono. Osati munthu wokhalandi mphatso, munthu chabe amene anali ndi kulimbamtimakokwanira kuti apite uko ndi kukayambitsa.

Chikanachitidwa ndi chiani pansi pa Izi? Akanakhozakukhala kuwerengedwera mu mamilioni. Ndithu. Ife taitayanthawi imeneyo. Ndi chimene kulingalira kwanga kukanakhalakuli.94 Tsopano kumbukirani, pochita izi, inu mupeza kuti, zikhozakukhalapo nthawi zimene inu mungadzamatsutsane ndi M’baleWakuti-n-wakuti. Inu mukhoza kusagwirizana cha apa. Ndipokumbukirani, utali wonse pamene inu mufika pa malo, inumungati, “Chabwino, chifukwa iye sakukhulupirira Izo basimonga ine, ine sindipitako,” ndiye pali chinachake cholakwikandi iwe. Si cholakwika ndi munthu winayo. Ndi chinachakecholakwika ndi iwe. Pamene, abale amene akuyesera kutiagwirire palimodzi!95 Pali chinthu chimodzi, ife ma Branham, tiripo naini aife, ndipo ife timakhoza kumenyana ngati tiagalu towetedwa.Koma, pamene ife tatsiriza kumenyanako, ife timakhalabe tirima Branham. Wina amadziwa kuti winayu ndi Branham. Inendimadziwa kuti iye ndi Branham. Iyeyo amadziwa kuti inendi Branham. Mukuona? Koma ife timakhoza kumenyana. Inumumachita zimenezo mu banja mwanu, komabe iwo akadaliabale anu.

KUTENGA MBALI NDI YESU 827

Ndi momwe izo ziriri. Ife tikhoza kusiyana, izo zonsenzabwino, komabe ndife amodzi. Ndife amodzi mwa Khristu.Ife timakhulupirira Uthenga uwu, ndipo tiyeni tizikhalanawobe Iwo.96 Ndipo ine ndikuganiza kuti ndicho chinthu choti tizichita,kuti tizipitirirabe, mpaka Yesu abwere. Ndipo ndi chimene inendimafuna kuti ndinene mwa mtundu woterowo. Ndipo inendikukhulupirira kuti ngati inumungakhale…97 Mukuona, inumuyenera kumakhala otengeka ndi Iwo. Ngatiinu simuli otengeka, ndiye kuti pali chinachake cholakwika.Pali chinachake cholakwika. Inu muyenera, osati kumangoti,“Chabwino, mwezi watha ine ndinali otengeka ndithu, komaine sindikudziwa.” Mukuona, ndiye kuti pali chinachakecholakwika penapake. Inu mukuyenera kuti muzitengeka nazo,nthawizonse, mukuona, ndipo zingopitirirani kukhomerera. NdiMdierekezi, akuyesera kuti akutengeni inu

Monga, ine nthawizonse ndinkamukonda purezidenti wathuwapitayo, Bambo Eisenhower. Ine ndinali ndi kuyamikirakwambiri pa General Eisenhower. Iye anati, “Pamene ife tinalikumenyana,” iye anati, “panali nthawi zambiri ife tinkatolachipolopolo ndi kuchiika icho mumfuti, ndi kukoka kowomberapa icho, nkuchilola icho chiwombere, ndipo icho chinkakanirira.Icho sichinali kuwombeleka.” Anati, “Ife sitinali kugonjera.”Anati, “Ife tinkakhoza kuikamo china, ndipo icho nachonso,chinkakanirira.” Anati, “Ife sitinali kugonja.” Anati, “Ifetinkapitiriza kumawomberampaka chimodzi chiwombere.”98 Ndi zimenezo. Umo ndi momwe mungapambanire nkhondo.Kupitirira kuyesera. Kuika chipolopolo mu iyo ndi kuikoka iyo.Iwe uli ndi cholinga, chandamale choti uchimenye. Ndipo ngatiicho sichiri kuwombera, chitayire icho kunja, ndi kuponyerachina mmenemo, ndi kuyesera iyo kachiwiri. Chiponyeremo ichoumo ndi kuyesera iyo kachiwiri, mpaka chimodzi chiwombere.Chiripo chimodzi mmenemo chimene chiri chamoyo, ndipochimodzi cha izo chiwombera. Koma umo ndi momwe ifetikuyenera kumachitira. Tizingopitirira kuwombera uko,kuwombera uko, mpaka chinachake chichitike.99 Kodi ine ndikuchita chiani? Ine ndikuwombera kwina pano.Ine ndikupita uko, ndisali kudziwa ngakhale…kunja kwakutsogolera kulikonse

Udindo! Mamilioni a anthu akuyang’ana pa iwe, “Kodi iweuchita chiani? Kusuntha kwina ndi chiani?” Ena akuganiza kutiine ndafa. Ena akuganiza ichi. Ngakhale mfuti inaphulika ija,tsiku lina, akuti ine ndimayesera kuti ndidziphe. Chirichonse,mukuona, kunjako kuzungulira dziko, ndi chirichonse.Mukuona? Koma iwe uli nazo izo zonse kuti ulimbane nazo.Ndiye, iwe uli nako kulemedwera anthu.

828 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

100 Ndipo tangolingalirani, bwanji ngati Mulungu akanaika painu, kuti inu muzidziwa mtima wa anthu amene inu munalikuyankhula nawo? Taganizani za zimenezo. Mukuona? Abale,mwinamwake, ine ndikudziwa inu muli nazo zilemetso, komainu simukumvetsa. Ndipo pambali pa izo, kuno, iwe uli nawoudindo kuno.101 Inu mukuti, “Chabwino, izo zikuyenera kukhala zophwekakwa inu, M’bale Branham. Chirichonse choti inu muchite,Mulungu amangokuuzani inu.” Ayi. Iye samatero. Inendimakhetsera thukuta izo, monga momwe inu mumachitira,ndipo molimbira kochuluka kwambiri. Zedi. Ine ndimachitakukhetsera thukhuta izo molimba kuposa momwe inumumachitira.

Ndipo padzakhala pali zochulukira ziti zidzafunidwire kwaine. Pamene inu mukuyenera kudzayankhira kwa mpingo,pamene inu mukuyenera kumayankhira kwa banja lanu, kapenamwina kwa inu nokha, mukuona, pali mamilioni a miyoyo imeneine ndikuyenera kudzaiyankhira. Ine ndikuyenera kumadziwamayendedwe anga. Ndipo ngati Satana akukugogodani inu,chifukwa cha moyo umodzi, kapena miyoyo yochepa imene inumukuyigwira, nanga bwanji kuno kumene mamilioni akukhalamu dongosololi? Ndi kuwombera kungati kwina kumene iyeati akuponyere mmenemo? Mukuona? Kotero inu muli nazozochuluka zonsezo zoti muzizikumbukira, abale. Izo, palibezodabwitsa kuti ine ndimakhalawamanjenje nthawizina. Zedi.102 Koma tsopano ine ndikukhomerera kwina pakali pano.Ine ndikuponyera mkati chipolopolo. Ngati icho chiwombera,ndi chimenecho apo. Ngati icho sichiwombera, ine sindisiya.Ine ndichitaya icho, ngati chokugwa, ndi kuyesera china.Chimodzi cha izo chiwombera. Ndizo zonse zimene ziripokwa izo. Chimodzi cha izo chikawombera, kwinakwake.Ndiye i—ine ndikufuna kuti ndikhale ndiri pa chandamale,chotero, pamene icho chiti chiwombere, ine ndimenye chinthuchimene ine ndikuwombera pa icho. Ndipo tsopano inumukudziwa zimene ine ndikutanthauza. Ine ndikutsimikiza.Mukuona? Pali chinachake, kwinakwake. Ine ndikuchokakupita ku misonkhano imeneyi, kungodziponya kutali uko. Inesindikulinga kuti ndizikaphunzitsa zinthu zazikulu izi zimeneine ndikukuphunzitsani anthu inu.103 Inu mukukumbukira zomwe loto lija, limene inendinalipezera kutanthauzira, linati. “Bwerera uko ndikukasunga Chakudya.” Inali kuti nyumba yosungiramoyo?Kachisi uyu. Kodi chiri kuti chirichonse chonga iwo mu dzikoli,kuzungulira kuno kulikonse, chimene chingafanane ndiUthengaumene ife tiri nawowu?

Tsopano, ndithudi, abale athu aang’onowa kuno amene alinafe kuno,mipingo ina yaing’ono iyi, iwo ndi ife. Ndife amodzi.

KUTENGA MBALI NDI YESU 829

Ndikuti kumene inu mukanapita, kuti mukawupeze Iwo?Ndisonyezeni chofanana nawo Chake kulikonse. Inu mupitakumene mpaka mu tizikhulupiriro ta chipembedzo. Inu mupitakumene kuDzina la Ambuye Yesu. Inumupita kumene ku zinthuzina izi. Mukuona? Ndipo kuno ndi kumene Chakudya chakhalachikusungidwa.104 Chabwino, Uthenga umodzi umene ine ndinalalikirakuno kwa inu nonse…Taonani, ine ndakhala ndikulalikirakuyambira wani mpaka maora sikisi kwa inu, pa Uthenga.Chabwino, ngati ine ndikanati ndigwiritse ntchito umodzi waUthenga umenewo, ine ndikamatenga sabata kuti ndiutengeIwo, pang’ono pokha apa ndi pang’ono pokha apo, mukuona,chifukwa Iwo wakhala ukusungidwa kuno.105 Iwo uli pa matepi. Iwo uzipita ku kutambalala konsekwa dziko pa matepi, kumene anthu mu manyumba mwawo.Matepi amenewo azikafika mmanja mwa a okonzedweratu aMulungu. Iye akhoza kuwalondolera Mawu. Iye alondolerachirichonse ndendende basi mpaka ku ntchito yake. Ndichochifukwa Iye ananditumiza Ine kuti ndibwerere ndidzachite izi.“Kudzachisunga Chakudyacho kuno.” Iye anandiletsa ine kutindipite kutsidya kwa nyanja.106 M’bale Arganbright anati, “Chabwino, bwerani, tipite. Inumuli ndi usiku umodzi, koma ife tikakutengerani inu paulendowokawona zinthu kuzungulira ku dziko lonselo.”Momweine ndinamuwonera M’bale Fred ndi M’bale Banks akuyeserakuti apite.107 Ine ndinati, “Ine sindingapite mwanjira imeneyo.”Mukuona? Izo zimasonyeza kuti panali chinthu chinachakenso.108 Ine ndakanikizira mpaka pa malowo tsopano, komaine sindikudziwa njira yoti ndipiteko. Koma pali zida ziripondizungulira ine ponse. Kodi Iye anandiitana ine kutindibwerere ku uvangeli? Kodi Iye wandiitanira ine ku utumwiwakunja? Kodi Iye wandiitana ine kuti ndikakhale mneneriWake? Kodi ine ndiri woti ndizichita ubusa kwinakwake?Chirichonse chimene ine ndiri woti ndizichita, ine ndizingokhalandikungoponyera chipolopolo mkati ndi kukokera ka nyundopa icho. Chimodzi cha izo chiwombera. Koma ine sindingokhalandi kumayang’anira, nkuti, “Ambuye, Inuyo muike chipolopolomu futiyi.” Ineyo ndiika chipolopolocho mu futiyo, ndikuchita kukoka ndekha. Muloleni Iye achite kuwomberako.Iye ndi Amene ati asamalire zimenezo. Ndisiyeni ine ndikhalendikusuntha chamtsogolo.109 Uko, pamene ine ndiri kupita pa misonkhano iyi tsopano,ine ndikungopita uko. Ine sindikudziwa. Izo, i—ine mwinasindingakanene chinthu chimodzi cha Mauthenga awa mongaine ndikuwalalikira kuno. Ine mwina ndikhoza kusakakhala ndiusiku umodzi wa kuzindikira za mumtima. Ine sindikudziwa.

830 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

Ine ndikungopita, ndisakudziwa chimene ine nditi ndikachite.Ine sindingathe kukuuzani inu. Ine ndikungopita, ndipondizo zonse.110 Ndipo umo ndi momwe iwe umayenera kumachitira. Iwe ulindi chinachake mu malingaliro. Anthu kuno akufuna tchalitchi.Mangani icho. Mwamsanga momwe inu mungathere, chiimikeniicho. Tengani aphunzitsi anu ndi zinthu.

Inu abale a kutali uko, ndi mipingo yanu yaing’ono,ndipo inu mukufuna kutero, inu mukugwira ntchito, Mulunguadzakulipirani inu chifukwa cha izo. Zipitani kunja uko,zikalalikirani, zichitani chirichonse chimene inu mungathe.Nonse inu zibwerani palimodzi, inu gulu la amuna, ndikumakhala ndi misonkhano, ndi kumayankhula pa zinthuzakuya za Lemba.

Ndi, kupemphera. M—musati muzingobwera kunopalimodzi, kupatula ngati inu mukudzera msonkhano wapemphero wokha. Zichitani zopemphera zanu mwamseri.Zikakhalani kutali pa malo. Zipitani mu zipinda zanu.Zikabisalani kwinakwake. Ndipo kungogwada pansi, ndikungokhala pamaso paMulungu, ndi kukhala pamenepo.

Ndiye ngati inu mupeza, zikuwoneka ngati chinachakechikusunthira apo, o, inu mukungopita, ndipo inu mukapezakuti izo zikuchoka pang’ono pokha pa Mawu, ndiye khalaniosamala. Ziribe kanthu momwe zikuwoneka zabwino, imaniapo pomwe. Mzimu wolakwika wakukhudzani inu. Chifukwa,Uthenga wa tsiku ili ndi wa ku Mawu. Mukuona? Musati.Mukuona?111 Ngati inu muti, “O, mai, M’bale Branham! Ine ndikukuuzaniinu zakuti-n-zakuti. Mwakuti, Wakuti-n-wakuti anaima usikuwina, chinthu china ichi chinachitikamonga chonchi.”

Zipenyani izo. Penyani izo mwatcheru. Musati muzinyozetsachinthu china. Ingodikiranni ndi kuwona momwe ichochikuchitira, ndiyeno nkuchibweretsa icho ku Mawu ndikuwona momwe icho chikufanizitsira ndi Mawu. Ndiye, ngatiicho chikufaniziritsira ndi Mawu, ndipo chirichonse chiribwino,zithokozani Mulungu, ndi kupitirira kusunthira mtsogolo ndiye,mukuona, bola ngati icho chikukhala mu Mawu. Ilo ndirolingaliro langa, zimene ine ndikuganiza kuti inumuzichita.112 M’bale Neville, M’bale Ruddell, M’bale Crase, ndi M’baleBeeler, ndi onse inu abale pano, Junie, kulikonse kumeneinu muli, ndi ena nonse inu abale, Mulungu akudalitseni inumolemera.

Ine ndikumuwona Terry, Lynn, Charlie Cox, David, ambiria inu anyamata pano. Mulungu anakudzozani inu. Mai!Momwe ine ndikanakondera kukutengani odzaza dzanja ainu, kuti mukhale avangeli, ndi kukakuikani inu kwinakwake,mukuona, podziwa kuti inu mwabwerapo. Inu mukhoza

KUTENGA MBALI NDI YESU 831

kuima ndi kuwudziwa Uthenga, ndi kuwuphunzira, kutimudzitsimikizire nokha, inu mukumverera kuitana mu moyowanu. Ine ndikuwona amuna awiri kapena atatu, ndi anaikapena asanu, akhala, pa mzere wina kumbuyo pano, n—ndimonga choncho. Ndinu mnyamata. Ine ndayamba kukalamba.M’bale Neville ayamba kukalamba. Ndife amuna a usinkhuwapakati. Ngati nthawi ipitirirabe, ife tidzayenda nkuchokapoonekera pakapita kanthawi. Inu muyenera kudzalowa munsapato zathu. Mukuona? Ndipo kotero inu mukuona. Ndiyeno,mwinamwake, mu tsiku limenelo, mpaka izo zidzakhalazikukula mopambana, ngati mawa liripo.113 Koma pamene lero liripo, tiyeni tizigwira ntchito pameneliri lero. Mawa mwina likhoza kusabwera. Ngati ilo litero,tiyeni tikhale okonzekera kwa ilo. Mukuona chimene inendikutanthauza? Tsopano, ndi zimene ine ndikanati ndilingalire,kwa inu.114 Zikanati zikhale zodabwitsa kumuwona m’bale apowochokera ku Utica, M’bale Crase, nonse inu abale kuno,mukumabwera palimodzi, kukomana, kubwera mu malo.Atumiki inu kukhala pamodzi ndi kumakambirana zinthu.Inu muyenera kumakhala nacho chiyanjano kwinakwake.Inu muyenera kumakhala nacho chinachake, kuti muzibwerapalimodzi, kukhala ngati mukubwera pamodzi nazo. Inu nonsemuzibwera palimodzi ngati gulu la amuna ndi kumakhulupirirammodzi ndi enawo, ndi monga choncho, ndi kumakambiranamavuto awa, ndi kukakhala kwina, mwinamwake, kamodzi pamwezi, atumiki okha basi. Inu muzikumana kwinakwake muumodzi wa mipingo yanu. Kukhala kumeneko ndi kukambiranaizo, ndi kuyankhula izo, aliyense wa inu azibusa, ndi avangeli,ndi chirichonse chimene inu muli.

Ndiyeno ngati vuto lina lalikulu libwerapo, limene inusimungathe kulikonza, ndiye, ngati ine ndingati ndiitanidwireku munda wa uvangeli. Ine sindikudziwa kuti ine ndidzakhalanditatero. Ngati ine ndidzakhala, inu mukudziwa inendidzakhala ndikumabwerera kuno, mowirikiza, nthawi zonse.Ndiyeno ngati inu mupeza zinthu zimenezo, ndiye, pamene inendibwerera kuno, chabwino, ife tizidzakomana palimodzi ndikungokhala pansi pamenepo. Mmodzi wa inu ali nako kuitanamu moyo wake…Ife sitimadzakhala ngati kuyankhulanakwapadera ndi zinthu zimene ife takhala tikukhala nazo. Ifetizidzangobwera molunjika palimodzi, ndi kukhala pamenepompaka ife titakhala ndi PAKUTI ATEROAMBUYE.115 Ndipo ngati inu mungawapange alaliki kuwongoka, ndipoiye nkumapita molondola, muwone zimene iye angati azichita.Iye aziti azikopa…Izo zingati zisamalire mazana a zinthuizi. Ndi zimenezo. Ife tikungomenya pa izo, inu mwaona. Inumuyenera kuzitengera izomudongosolo, dongosolo laMulungu.

832 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

116 Monga Yatero ananena kwa Mose, “Ndiye, iwe sungathekuchita nawo onsewo.” Kapena, ndipo Mulungu anaika akulukumeneko, makumi asanu ndi awiri a iwo. Ndipo anatengaMzimu umene unali pa Mose, ndipo anawuika iwo pa akulumakumi asanu ndi awiri awo. Ndipo iwo ankalosera. Ndipoizo sizinamufooketse Mose mpang’ono. Izo zimamulimbikitsaiye. Iye basi anali nawo uneneri wochuluka mwa iye mongaiye ankachitira asanauchotse Mzimu pa iye, kuti azinenera.Mukuona? Iye anangolekanitsa, anati, “Tsopano, Mose, asiyeiwo aziweruza zinthu zazing’onopo. Ndipo, koma, pamenezizifika pa zinthu zikulu, iwe uzibwera mmenemo ndi iwo ndikuwathandizira iwo monga choncho.”117 Tsopano, iyo ndiyo njira yake. Iyo inali njira ya Mulungukumbuyo uko. Iyo inali njira ya Mulungu m—mu M’badwo waMpingo woyambirira. Ndipo ine ndikukhulupirira kuti iyo ndinjira ya Mulungu tsopano, kulondola, yoti ife tizichitira izo.Kotero, tiyeni tizichita izo. Tingosiya zongoyankhula za izo, ndikumazichita izo. Ndizo zonse. Ife tikhoza kumachita izo mwachisomo cha Mulungu. Kodi inu simukukhulupirira izo? [Abaleati, “Ameni.”—Mkonzi.]

Tsopano, tsopano, tiyeni tiwone. O, ine ndatenga kalenthawi yanga.118 Koma Billy analemba cholemba apa. Miniti yokha, inendiwone chimene icho chiri. “Ndine wochokera ku New Albany.Mwana wamkazi Grace, kuMemorial Hospital, anathyola nkonowake. Akufuna pemphero kwa iye. T-r-o-u-b, W.C. Troub.”Troub, chinachake monga choncho.

Tiyeni tikhale ndi pemphero la kwa donawamng’ono uyu.119 Atate athu Akumwamba, pamene ife tiri chiyankhuliretsopano, ndipo ine ndikuganiza kuti mwinamwake pameneIrenias anayang’ana uko pa gulu lake laling’ono la amuna,mwinamwake ilo linali gulu laling’ono kwambiri kuposa limeneliri panoli usikuuno. Ndipo iwo analibe mpando woti akhalepo.Iwo anakhala pa zimakonkire zozira za mwala. Ndipo iwoanakhala pamenepo, ndipo iye anayankhula kwa iwo. Amunaawo ankapita kunja ngakhale pamene, iwo ankapita, iwoankadziwa kuti iwo akanakhoza kukadyetsedwa kwa mikango,mitu yawo kukadulidwapo. Koma Chikhulupiriro cha makoloathu chikanali chamoyo, ngakhale kunali kumidima,malawi ndilupanga.120 Ine ndikukuthokozani Inu chifukwa cha amuna awa,Ambuye. Ine ndikupemphera kuti Inu muwadalitse iwo.Tsopano, mudalitseni aliyense wa iwo, mu Dzina Lanu, kuti Inumuwasunge iwo mu Chikhulupiriro chimene chinaperekedwapoyamba kwa oyera, kuti iwo asadzapatuke konse kwa icho.Ndipo kuchokera ku gulu lino Inu mutumizepo azibusa,aphunzitsi, avangeli. OMulungu, perekani izi. Ndipo mulole iwo

KUTENGA MBALI NDI YESU 833

azikagwira lingalo, kulikonse, konse kumene iwo ali. Mulole iwomopitiriza azikagwira ntchito mpaka Yesu atadza.121 Ndipo tsopano, Atate, ine ndikupempherera chirichonsecha zopempha izi zimene zabwera kuno usikuuno, ndipo inendikupempha kuti Inu mumkumbukire dona wamng’ono uyukomwe kuno, amene wathyola kumene nkono wake. Mulolemphamvu ya Mulungu Wamphamvuzonse imuchize iye ndikumupanga iye kukhala bwino. Perekani izi, Ambuye. Inendikupemphera kuti Inu mumuthandize iye ndi kumudalitsaiye. Mudalitse okondedwa ake chifukwa cha kuimba. Ndipomulole mphamvu imene inamudzutsa Yesu kuchokera mmandaimudzutsemsungwana uyu.Mulole nkonowake ukhale bwino.122 Zopempha zonse izi zimene zinatchulidwa usikuuno!Mnyamata wosauka uja wagona apoyo, amene ali ndi ichi,ine ndinamumva m’bale akulengeza izo, kuti m—matenda aHodgkin amudya iye mpaka nkhope yake yawotcheka, ndirediamu ndi zinthu zimene iwo akumupatsa iye. Mulungu,muchitire chifundo mnyamata ameneyo. Muloleni iye akhalemoyo.

Ife tikuganiza za bambo uja amene sanakonzekere kutiakakomane ndi Inu, ndipo wapita tsopano; mkazi wake ali ndimutuwophwanyidwa.Mwanawomulera! Ena onse awa!

Mlongo Bruce, akutunga madzi aja. Iye akukalamba, Atate.Ndipo apo iye anawotchamikono yake, ndimuntunda ndimmusimwa thupi lake. Ife tikumupempherera iye. Iye mwinamwakewagonekedwa mchipatala. Ndipo ife tikupemphera kuti Inumumupulumutse iye ndi kumutulutsako iye. Perekani izi, Atate.Ife tikupempha madalitso awa mu Dzina la Yesu Khristu.Ameni.123 Tsopano ine ndikufuna kuti ndikufunseni inu chinachake,ndipo ndikukupemphani inu n—ngati inu mukukhulupirira kutitiri nayo nthawi pang’ono pokha pa Mawu. Kodi inu muli nayoiyo? [Abale ati, “Inde.”—Mkonzi.] Basi kwa…Tsopano ndizo,ine ndikudziwa tiri mochedwa pang’ono, koma ine ndinali nakokenakake kakang’ono pano kamene ine ndimakaganizira pa zalero, kamene ine ndikanakonda k—kuti ndiyankhule pa iko, basikwaminiti, ndipo izo zikhoza kukuthandizani inu.

Ndipo ine ndimaganiza, poyamba, kuti ine ndingatindilengeze izi. Tsopano, izo ziri pa tepi iyi. Ndipo ngati aliyenseangafune konse kuti alozere kwa izo, Jim akhala ali nazoizo, mwaona, pa zimene ine ndikuganiza kuti zikuyenera kutizizichitidwa, ndipo tsopano zomwe zikuyenera kumachitidwakwa…kwa inu abale.124 Tsopano, kodi inu mukudziwa, pamene amuna oyambiriraaja ankapita kunja, nthawizina uko kunkakhala pafupi asanundi mmodzi okha kapena asanu ndi atatu a iwo, palimodzi?Ndipo iwo anali kugwedeza dzikolo. Chabwino, inu mukudziwa,

834 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

pamene Akwila ndi Priscilla, chitsitsimutso chachikulu chijachimeneApollo anali nacho kumeneko, uko kunali pafupi amunaasanu ndi mmodzi okha kapena asanu ndi atatu ndi akazimu gulu limenelo. Mpingo wonsewo, unkatanthauza asanu ndimmodzi kapena asanu ndi atatu. Inu muli nawo kasanu kapenakasanu ndi kamodzi, kuchulukitsa kasanu ndi kawiri kuchulukakwake pano usikuunomomwe iwo analiri nawo kumeneko.125 Inu mukudziwa, Yesu anali ndi ophunzira khumi ndi awiriokha. Ife nthawizonse timaganiza za chinachake chachikulu.Koma Mulungu samachita mu ziwerengero zazikulu zimenezo.Ndi mu magulu aang’ono awa ndi kumene Iye amazipeza izo.Mukuona? Tayang’anani konseko kudutsa mu m’badwo, panthawi iliyonse Iye anayamba wakomanapo ndi anthu. Iwo analimu magulu aang’ono, mwaona, ndipo ankayankhula nawo iwo,ndipo ankawadzoza iwo. Ndi kukondweretsedwa bwino kwaMulungu kuti azichita izo. Umo ndi momwe Iye ankakonderakuchita izo. Ndipo tsopano ife tikungofuna kuti tizimusungaMulungu pakati pathu, ndi kumapita, kumakachita zinthuzimenezi.126 Tsopano, Lamlungu mmawa, Ambuye akalola, inendikufuna kuti ndidzayankhule kwa inu pa Uvangeli wa NthawiYamadzulo. Ndiyeno ine ndidza, ngati Ambuye aloleza, inemwinamwake ndidzakhala ndikuchokapo mpaka mochedwa munthawi yolakatika masamba iyo, ndipo ine ndisanati ndibwererekachiwiri. Ine mwinamwake ndidzabwerera nthawi ina, cha muSeputembala.

Ndipo tsopano ine ndikuyembekeza, pofika apo, kutichirichonse chizikhala chikukuyenderani modabwitsa kwainu abale, ndipo misonkhano yanu izikula mu ziwerengero,ndipo chisomo cha Mulungu chikhala pa inu nonse,mpaka ife tidzakomane. Ndipo ine ndikudalira kuti inumuzindipempherera ine, ndi kuchita bwino.

Kumbukirani ndi mapemphero anu kwa ine. Izozikutanthauza kuti inu ndi ochita nane. Inu—ndinuamzanga, ondithandizira anga. Ndipo, palimodzi, ife tiriothandizira mwa Ambuye. Ndipo tsopano, pamene inendiziima kunja uko pamaso pa mdani, i—ine ndikufuna kutindizikumbukira asilikari okhulupirika, owona aja, ameneamayankhidwa pemphero pa odwala ndi osautsika, ndipoamuna amenewo ali kundipempherera ine. Ine ndi amenendikuwasowa iwo kunja uko. Ine ndikuwasowa kwenikweniiwo. Kotero, inu nonse muzindipempherera ine pamene inumuzisonkhana. Musati muzindiiwala ine, mu msonkhanouliwonse. Muzindipempherera ine.127 Tsopano, mu Yohane Woyera, mutu wa 9, ine ndikufunakuti ndiwerenge kuyambira pa ndime ya 26 mpaka ya 35,tsopano, kwa maminiti ochepa okha. Ndiyeno i—ife titseka mu

KUTENGA MBALI NDI YESU 835

maminiti twente kapena sate otsatirawa, kapena mwinamwakeisanafike nthawi imeneyo, Ambuye akalola. Ine ndikufunakuti ndiwerenge Malemba awa tsopano kuchokera mu YohaneWoyera, 26mpaka…YohaneWoyera 9:26-35, ine ndazilemba izoapa, chinachake basi chimene ine ndimachiganizira.

Ndiye iwo anati kwa iye kachiwiri, Kodi iye anachitachiani kwa iwe? iye anakutsegula chotani iwemaso ako?

Ndipo iye anawayankha iwo, ine ndakuuzani inukale, ndipo inu simumamva; mukufuniranji inu nangakuti mumve…kachiwiri? kodi inunso mufuna kukhalaophunzira ake?

Ndiye iwo anamlalatira iye, ndipo anati, Iwe ndiyewophunzira wake; koma ife ndife ophunzira a Mose.

Ife tikudziwa kuti Mulungu ankalankhula kwa Mose:koma za munthu uyu, ife sitiri kudziwa kumene iyeanachokera.

Bamboyo anayankha nati kwa iwo, Ndiyetu apa palichinthu chozizwitsa, kuti inu simuli kudziwa kumeneiye anachokera, ndipo komabe iye wawatsegula masoanga.

Tsopano ife tikudziwa kuti Mulungu samamumveraochimwa: koma ngati munthu aliyense akhalawopembedza wa Mulungu, namachita chifuniro chake,amamumvera ameneyo.

Chiyambireni cha dziko sizinamvekepo kuti munthuwina aliyense anatsegula maso a wina amene anabadwawakhungu.

Ngati munthu uyu akanati asakhale wa Mulungu, iyesakadakhoza kuchita kanthu.

Ndiye anayankha…Iwo anayankha nati kwa iye, Iweunabadwa kwathunthu mu tchimo, ndipo ukuti iweutiphunzitse ife? Ndipo anamponyera iye kunja.

Ndipo Yesu anamva kuti anali atamtaya iye kunja;ndipo pamene iye anamupeza iye, iye anati kwa iye,Kodi iwe ukukhulupirira pa Mwana wa Mulungu?

128 Tsopano ine ndikufuna kuti ndiyankhule kwa maminitiochepa okha kwa inu abwenzi, podziwa kuti, kuyankhulakwanga kwapang’onoku pano, ine sindikudziwa chomwe chitichikhale kwa iko. Ndikudalira kuti Mulungu azigwiritsa ntchitoizo mwa njira ina. Ndipo tsopanomu izi, mwaMawuAke, koteroine ndikudziwa kutiM’bale Sink,M’bale Neville kapenammodziwa inu atumiki, kawirikawirimumalalikira. Ndipo akungokhalakuno ndi inu, inu mundikhululukira ine, ine ndikungofuna kutindiyankhule kwa inu pang’ono pokhamwa njira iyi.

836 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

129 Tsopano ine ndikufuna kuti nditenge phunziro apa la:Kutenga Mbali Ndi Yesu. Afarisi ndi atsogoleri a tsikuLake nthawizonse ankayesera kuti azimuchepetsa Iye pamasopa anthu. Iyo inali njira chabe imene Mdierekezi analinayo yogwirira ntchito. Afarisi onse ndi aphunzitsi a tsikuLake mosalekeza ankayesera kuti amuchepetse Yesu. Iwo,zoponyerapo zonse zimene iwo akanapereka kwa Iye, iwoankazichita izo. Iwo ankamuyang’anitsitsa Iye, mowirikiza, kutiapeze pamene iwo akanati apeze cholakwa. Ndipo iwo sanalikuyankhula konse za zinthu Zake zabwino. Iwo nthawizonseankamupezera Iye chinachake chimene iwo akadamuchepetseranacho, ndi kuti, “Inu mukuona, tayang’anani apa. Ngati iyeakanakhala mwamuna wa Mulungu, Iye sakanati achite izomwanjira iyi.” Kapena, “Ngati iye akanakhala munthu waMulungu, iye sakanati achite izo mwanjira imeneyo.” Iwoanali kuyesera kuti aponyere mthunzi pa Iye, kuti awafikitseanthu pakuti asamukhulupirire Iye. Imeneyo ndiyo ntchito yaMdierekezi.

130 Ndipo kachitidwe kachikale ako sikanayambe katha. Palinthawi zambiri pamene mtumiki angati alakwitse. Ndipongati iye abwera mwa oyandikana nawo, m’bale wofunikaamene akuyesera kuti azichita zimene ziri zolondola, ndikumawatsogolera anthu molondola; chirichonse chimeneMdierekezi angalozere kwa wosakhulupirira kapena wotchedwaMkhristu, mwa woyandikana amenewo, kuti awaponyerekumbali pamunthu ameneyo, iye amazichita izo.

Inu mukudziwa, njira yeniyeni ya Mkhristu ndi kubisachirichonse chimene iwe ungathe cha m’bale uyo. Usatiunene zinthu zoipa zake. Zingomanena zinthu zake zabwino.Zingonena zimene iwe ukuzidziwa za iye zomwe ziri zabwino.Ngati chirichonse chiri choipa, zichisiya icho chokha. Munthuwosaukayo ali nazo zokwanira zomutsutsa iye, mulimonse.Musati muziyesera kutenga chimtengo ndi kumulaishilamunthuyo kutali mu dzenje. Kachitidwe ka Mkhristu ndi kutiumutenge iye ndi kumuchotsa iye mu dzenjelo. Mukuona?Musati konse muziyesera kuti mumulaishile iye pansi. Iye alipansi, kale. Ziyeserani kuti mumuthandizire iye atulukemo.Ndipo, koma, ochuluka kwambiri a ife lero, anthu ochulukakwambiri lero, ine ndikhoza kunena, amayesera kuchitazimenezo, ngati iwo angakhoze kungopeza chinachake chimeneiwo angakhoze kunena, chimene chinali choipa kwenikweni.

131 Tsopano, mwa chitsanzo, n—ngati mmodzi wa inu abaleangapange cholakwika ndi kuchita chinachake cholakwika;chimene, inu muli woti mukhoza kuchita izo; ine, ndingathenso;mmodzi aliyense wa ife. Koma, pamene ife tikupitirira nazo,tiyeni tizikumbukira ife ndi abale. Ife ndi abale. Ndipo ngatiife tiri ndi ndewu iliyonse, tiyeni tizimenyana wina ndi mzake.

KUTENGA MBALI NDI YESU 837

Muzizibweretsa izo palimodzi. Muzizibweretsa izo pamaso paabale athu ndi kuzithetsa izo.132 Tsopano, iwo ankakonda kuzichita, mu banja la aBranham, ngati mmodzi wa aang’ono achita chinachake, iwoankakamuuza Bill za izo, chifukwa ine ndinali wamkulupo.Ndipo ine ndinkayenera kuti ndiime pamenepo ndi kuwonaamene akulondola ndi kulakwitsa. Chabwino, lingaliro langalinali kuti, ngati iwo…ndani amene akulondola ndi kulakwa.Ngati iwo sanali kukhulupirira izo apobe, ndiye iwo ankapitakuseri kwa nsana wanga ndi kumakamenyana pa izo. Komaiwo amakhala ali abale apobe, inu mukuona. Iwo amakhozakumakamenyana kuseri kwa nyumba, wina ndi mzake; ndikudzamenyana kukhomo kwa nyumba, chifukwa cha wina ndimzake. Kotero umo ndi momwe izo zinaliri, mwaona, ndipo iwoamakhala akanali abale.133 Chabwino, izo, umo ndi momwe i—ife tikuyenera kutitizichitira izi. Mukuona? Ngati iwe uli ndi chinachakechomutsutsa nacho munthu winawake, m’bale wako, usatiumuuze winawake za icho. Ngati izo ziri zolakwika, pita kwa iyendi kukamuuza iyeyo. Ndiyeno ngati iye ati akatsutsane ndi iwe,ndiye kamutenge wina limodzi ndi iwe. Ndiye kazibweretseniizo ku zomwe Baibulo limanena.134 Koma, Yesu, i—iwo ankangoyesera kuti apeze mthunziwawung’ono uliwonse umene iwo akanaupeza, kuti ayesere kutiamuchepetse Iye pamaso pa anthu.

Ndipo izo ndi zimene Mdierekezi amafuna. Iwo amafunakutero. Iwo amafuna kuti apweteke chikoka chako pamaso paanthu. Iyo ndiyo njira yake. Iwe umayenera kuti uziyang’anamosamalitsa zimene iwe ukuzichita. Ziyendani ngati amunaenieni a Mulungu. Kuyankhula ngati amuna a Mulungu.Mukuona? Zichitani ngati amuna a Mulungu. Zikhalani ngatiamuna a Mulungu. Chifukwa, “Mdierekezi, mdani wanu,akuyendayenda ngati mkango wobangula, kuyesera kutialikhwire zimene iye angazithe.”135 Nchifukwa chiani iwo anali kuchita izi? Iwo anali ansanje ndi Iye. Icho ndicho chinali chifukwa chake chimeneiwo ankayesera kumuchepetsera Iye. Iwo ankachitira nsanjepa utumiki Wake. Ndipo icho ndi chifukwa chake iwoanali kuyesera kuti azimuchepetsa. Ndithu, Iye anali ndiutumiki wa Mulungu, ndipo iwo ankadziwa zimenezo, komaIzo zinali zotsutsana ndi tizikhulupiriro tawo. Kotero iwoankayesera kuti azimuchepetsa Iye, kupanga chirichonsechimene Iye…cholephera chaching’ono chirichonse chimeneiwo akanachipeza, kuti amuchotsetse Iye pa njirayo. Iwoankafuna kuti Iye asiye. Iwo ankafuna kuti anthu amukane Iye.

Iwo ankafuna kuti aziti, “Tsopano, Munthu uyu si kanthu.Taonani apa. Tsopano, apo Iye ali. I—I—Iye anachita izi, ndipo

838 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

inu mukudziwa kuti izo sizolondola. Ife taphunzitsidwa, moyowathuwonse, kuti ife tiziwakhulupirira akulu. Ndipo apa Iye ali,anaima apo pomwe ndipo amamulalatira mkulu ameneyo. Iyesamagwirizana ndi mwambo wa makolo. Ndipo ife takhala…Ife tikuyenera kuti tizikhulupirira mwambo wa makolo athu.Ife taphunzitsidwa zimenezo, ndi mphunzitsi aliyense, kudutsamu zaka zonsezi. Ndipo pano Munthu uyu akubwera apo ndikumatsutsana ndi iwo. Mukuona? Ndipotu, Munthu wongaameneyo sali woyenera kuti akhalemlaliki.”Mukuona? Iwo analikuyesera kuti amuchepetse Iye.136 Koma, mu zonse izo, iwo amene ankamukhulupiriraIye ndi kumukonda Iye, ndipo anali atawona zizindikiroZake, zozizwitsa Zamwamalemba, sakanati alepheretsedwendi iwo. Ayi, bwana. Iwo amene ankamukhulupirira Iyeankamukhulupirira Iye. Iwo amene ankamukonda Iye anaimapafupi ndi Iye. Iwo sankatha kuwona zimene enawo ankalozerakwa iwo.137 O, ngati ife tikanatha kukhala chimenecho! Ngati ifetikanati tisawone kokha. Ngati winawake akanabwera chakuno, ndi kuti, “Inu mukudziwa chiani? Iwo akuti iwe ndiwe wachipentekoste.”

“Osati mwa chipembedzo.”“Chabwino, iwe unali…Iwe, ndiwe mtundu uwo umene

umabatiza mu Dzina la Yesu.”“Eya. Uko nkulondola.”

138 “Ndiyetu, ndirole ine ndikuuze iwe chinachake. Inendikumudziwa mwamuna, nthawi ina, amene ankabatizidwamonga choncho, ndipo iye anachita zakuti-n-zakuti.”139 Koma taonani, izo ziribe kanthu kochita ndi Izo. Ndimdierekezi, akuyesera kuti aponyere mthunzi pa inu. Iwonthawizonse amayesera kuti akulozereni inu ku chombo chinachakale chimene chinawonongeka pa gombe la nyanja, koma iwosamakulozera iwe kwa icho chimene chinapanga ulendo wakemotetezeka. Ndiko kulondola.Mukuona?Ndiko kulondola.140 Iwo nthawizonse akuyesera kuti aponyere nyambo yakhwangwala kunja uko, ndi kuti, “Ichi ndi chitsanzo. Nachichimene chinachita izo. Ine ndikudziwa za mlaliki wina ameneanali mlaliki wachiyero, ndipo iye anachita izi, izo, kapenazinazo.” Koma iwo samawalozera ena amene sanali achiyero,amene anachita zimenezo nawonso, inu mukuona. Ndipo iwosamalozera ku zinthu zazikulu zimeneMulungu anazichita.141 Monga winawake kuti, “O, kuno bambo uyu anapitanazo patali kwambiri. Iye, iye anapita patali kwambiri.”Iye mwina anachita zimenezo. “Iye anadzipweteka yekha.Iye anapita patali kwambiri. Iye anakhala wotentheka.” Iyemwinamwake anachita zimenezo. Koma pamene iwo akulozera

KUTENGA MBALI NDI YESU 839

kwa amene anapita, wina amene anapita patali kwambiri,nanga bwanji mamilioni awa amene sanapite patari mokwanira?Iwo amalephera kuti awone zimenezo. Mukuona chimene inendikutanthauza? [Abale ati, “Inde.”—Mkonzi.]142 Kotero, anthu ankayesera, Afarisi aja, ndi Asaduki, ndiachinyengo, ndi Aherodia, ndi onse ankayesera kuti aponyeremthunzi pa Yesu. Koma okhulupirira owona aja ameneanakonzedweratu kuti awumve Uthenga umenewo, anaumvaIwo ndipo sanawone cholakwika chirichonsemwa Iwo konse.143 Chimodzimodzi tsopano. Iwo amene akumukhulupirira Iye,akumukonda Iye. Iwo amene akumukhulupirira Iye, sali kuwonacholakwika mwa Iye. Iwo sali kuwona mpatuko uliwonse.Iwo sali kuwona cholakwika chirichonse. Iwo sali kuwonachirichonse cholakwika ndi Mawu Ake. Iwo sali kuwonachirichonse cholakwika ndi anthu Ake. Iwo akungomuwonaYesu. Ndi zokhazo. Iwo, i—iwo ndi okonzedweratu ku MoyoWamuyaya, kotero iwo akungotenga mbali ndi Yesu ndi kukhalapamenepo.144 Ife tinkakonda kuimba nyimbo yaing’ono, M’bale RoyRoberson. Ndipo ife tinkakonda kuimba nyimbo yaing’ono kuno,ine ndikulingalira, nthawi imenemunkabwera kuno.

Ine nditenga njira ndi onyozeka ochepa aAmbuye.

Ine ndayamba umo ndi Yesu, ndipo inendikupyola nazo.

Ine kulibwino kuti ndiziyenda ndi Yesu yekha,Ndi kukhala nao mwa nsamiro wanga, mongaYakobo, mwala.

145 Chabwino, inu munaimvapo nyimbo yaing’onoyo. Ndikokulondola. Ine kuli bwino nditenge njira yosokoneza, nditengenjira yonyozedwa, nditenge njira yonenedwa, ndi kumayendandi Yesu. Osawona cholakwika chirichonse mwa Iyo, konse.Osawona cholakwika cha munthu wina. Kumangopitirira nazokupita. Ndizo zonse.

Tsopano, umo ndi momwe iwo anachitira kwa Yesu. Iwosana—iwo sana…

Ndipo inu muyenera muziwaphunzitsa anthu anu, inuazibusa, kuti azichita zomwezo.146 Ngati wina abwera apo, ndi kuti, “Inu mukudziwa, mpingowanu, iwo analimwakuti-n-mwakuti. Iwo…” Inde, bwana.147 Akhoza kukhalapo khumi ndi awiri a iwo anali apopamenepo, koma nanga bwanji ujayu a—amene—zirizonsezabwino, kukhala ali pamenepo? Mukuona? I—i—inu…Inubasi simukutha kuwona nkhalango ya mitengoyo. Ndizo zonse.Tsopano, ndi zimenezo, kubwerera kumene kachiwiri. Mukuonatsopano?

840 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

148 Ndipo kotero iwo anayesera. Iwo sanali kulolera kutiavomereze kuti Iye anali kuchita ntchito ya Mulungu, koteroiwo anali kuyesera kuti afetse chisokonezeko ndi kuwafikitsaanthuwo poti asakhulupirire. Koma anthu awo amene analikumukhulupirira Iye, anakhala kumene ndi Iye. Iwo anatengambali.

149 Inu mukudziwa, ine ndimaganiza apa, anthu angapo amenendinali nditawalemba apa. Bambo wakhungu uja sakanatiasinthidwe ndi iwo, bambo uyo Iye anali atangomupatsakupenya kwake. Ife tikuidziwa nkhaniyo. Ndipo Iye anawapatsaiwo funso lobaya kwambiri, pambali pake. Tsopano, iwoanabwera mpaka kumeneko.

Ndipo Yesu anadutsa kumeneko, ndipo Iye anali Munthuamene anali kunyozedwa ndi kudedwa. Baibulo linati Iyeakanati adzakanidwe. “Sipakanati padzakhale kukongola paIye, kuti ife timukhumbire Iye. Ndipo tonse ife ngati nkhosatapita mosochera. Iye anali Munthu wazisoni, wozolowerana ndichisoni.” Ndipo momwe Baibulo lonse linanenera zomwe Iyeakanati adzakhale. “Iye akanati adzanyozedwe ndi kukanidwa.”Ndipo ife tikumuwonaMwamuna ameneyo.

150 Tsopano, iwo amene anawakhulupirira Mawu, iwoamadziwa kuti zinthu zomwezo Yesu anali kuzichita, ndi zinthuzomwe zinali za moyo Wake, iwo ankadziwa Yemwe Iye anali.Kotero iwo sakanatha kuika kanthu koipitsa pa Iye, chifukwaiwo sankatha kuziwona izo. Ndipo inu mukudziwa, chikondindi khungu, mulimonse, kwa zinthu zimenezo. “Chikondichimaphimba unyinji wa tchimo,” inu mukudziwa. “Chikondichangwiro chimatayira kunja mantha, ndi tchimo, chisokonezochonse.” Chikondi chimatero.

151 Tsopano, munthu wakhungu uyu anali atakhala pamenepo,ndipo Yesu ndi ophunzira Ake anabwera cha kumeneko. Ndipoine ndikuganiza Yesu anawapatsa iwo phunziro laling’ono apa.Pamene iwo anamuwona munthu wosauka, wakhungu uyu, iwoanaganiza, “Ndithu, tsopano moonadi, pali tchimo kuseri kwaizo, penapake.”

Pamene ife tiwona chinachake chitachitika kwa munthu,ife nthawizonse timati, “Ndithu, iye wachimwa. Iye wachokamu chifuniro cha Ambuye, penapake.” Pamene M’bale Craseanagunda mtengo, “Iye anachoka mu chifuniro cha Ambuye,penapake,” mu kulingalira kwa munthu wina. Pamene mfutiinaphulikira, pa ine, “Chabwino, iye wachoka mu chifuniro chaAmbuye.” M’bale Neville anagunda galimoto, “Iye wachoka muchifuniro cha Ambuye.” Izo si kulondola ndendende. Ayi, bwana.Izo siziri. Mulungu amaloleza zinthu zimenezo.

Yesu anapotoloka apo ndipo anawaphunzitsa iwo phunziro.

KUTENGA MBALI NDI YESU 841

152 Iwo anati, “Atate ake ayenera kuti anachimwa. K—kapena,kodi ndi amayi ake anachimwa? Kapena, kodi ndi iyeyoanachimwa?”

Yesu anati, “Palibe wa iwo amene anachimwa, komakuti ntchito za Mulungu zikhoze kuwonetseredwa.” Ameni.Mukuona? Mulungu amalolela zinthu kuti zichitike basi k…kuti ntchito za Mulungu ziwonetseredwe. Tsopano, ndipochotero Iye anati, anamuuza bamboyo, ndipo anampatsa iyekupenya kwake, ndipo Iye anapita pa ulendoWake.153 Ndipo apa anabwera Afarisi, pamene izo zinangomvekapozungulira. “Apa panali bambo amene anali wakhungu,atakhala pansi apo akupemphetsa, ndipo apa iye amakhozakupenya.” Ndipo iyo inali mphekesera pakati pawo. Ndipo, o,mai, izo zinakondoweza chinachake. Ndipo apa iwo anabwerakumeneko, ndipo iwo anawona kuti munthu wakhungu ujaamakhoza kupenya.

Ndipo choyamba, iwo anapita, ankafuna kuti apeze njiraina yoti aikire mantha pa anthu onse. Chifukwa, iwo analiatanena kale, “Ngati aliyense ati apite motsatira Chiphunzitsochatsopano ichi ndi Mneneri watsopano uyu wotchedwa Yesuwaku Nazareti, nthawi yomweyo iwo adzapatsidwa chikalatachawo ndi chiyanjano kuchoka ku mpingo. Iwo sangati azipitaku sunagoge motalikiranso. Ngati inu muziyanjana ndi iye,kukhala nawo pa uliwonse wa misonkhano Yake kapenachirichonse, inu simungati muzipitako kenanso.”154 Kotero, iwo ankafuna kuti apange kuwonetsera kwakukulukwa izo, chifukwa iwo ankamuda Iye. Iwo sanali kuganiza zabambowosaukawakhungu uja. Koma iwo ankafuna kuti apangekuwonetsera kwakukulu, kuti awapangitse anthu kumatalikirakwa Iye.155 Iwo anati iwo ankafuna kuti akawafunse abambo ake ndiamake, chotero iwo anapita ndipo anakawatenga abambo ndiamake. Iwo anati, “Kodi uyu ndi mwanawanu?”

Iye anati, “Inde, bwana.”“Iye, kodi iye anabadwa ali wakhungu?”“Inde, bwana.”“Ndipo kodi iye wapenya motani?”

156 “Ndipo bambo ake ndi amake anali kuchita mantha,”Baibulo likuti, “chifukwa iwo ankadziwa kuti iwo akanatiachotsedwe ku sunagoge, ngati iwo akanavomereza kuti izozinali…”

Ndipo, onani, apo iwo anali, akuzilemba izo. Iwo anati,“Tsopano, ife tikudziwa kuti uyu ndi mwanawathu.”157 O, mwinamwake anthu zikwi zingapo ataima pamenepo.Koma ngati iye akanakhoza…Ngati Afarisi onunkha awo

842 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

akanangoika kokha choipitsa pa Dzina Lake apo pomwe,kapena akanachita chinachake kuti awawopsyeze anthu, iwoakanati amuthamangitse Iye achoke kumeneko, chifukwacha msonkhano umenewo. Mukuona? Chikoka Chake chonsechikanakhala chitataika.158 Kotero iwo anati, gulu la iwo linabwera apo kumenekolitavala zovala zawo zaunsembe, ndipo iwo anati,“Muyankhulireni iye.”159 Iwo anati, “Ife tikudziwa kuti uyu ndi mwana wathu. Ifetikudziwa kuti iye anabadwa ali wakhungu. Koma tsopano,momwe iye wapenyera, ine sindikudziwa. Inu mufunseni iye.Iyeyu ndi wamkulu.” Mukuona? Chabwino.160 Kotero iwo anapita apo ndipo anakamutenga iye, anati,“Nndani wakupatsa iwe kupenya kwako? Iye anakuchizamotani iwe?”

Iye anati, “Winawotchedwa YesuwakuNazareti wandipatsaine kupenya kwanga.”161 Ndipo iwo anati, “Pereka mayamiko kwa Mulungu.” Anati,“Pakuti, ife tikudziwa Bambo uyu kuti ndi wochimwa.” Anati,ndipo anati, “Kodi ali kuti Iye?”162 Iye anati, “Ine sindiri kudziwa. Iye anangobwera apo ndikudzandichiza ine, ndipo ndi zonse zimene ine ndikuzidziwapa izo. Ine ndikudziwa chinthu chimodzi chimene inendikuchidziwa. Ine sindingathe kukuuzani inu za Iye kuti ndiwochimwa, kapena ayi. Ine sindikudziwa. Ine ndinangokomananaye Bamboyo, lero. Koma ng—ngati Iye anatha kundipatsa inek—kupenya kwanga! Ine ndikungodziwa chinthu chimodzi ichi,kuti, kumene ine ndinali wakhungu nthawi ina, ine ndikukhozakupenya tsopano. Ine ndikutsimikiza za zimenezo. Pakuti, inendinali wakhungu, theka la ora lapitalo, ndipo tsopano inendiri nako kupenya kwabwino basi monga aliyense wa anthuinu. Chotero, ine ndikudziwa kuti ndikukhoza kupenya.”163 O, ndi mbola bwanji imene inaikidwa pa iwo! Chotero iwoanaganiza, “Bwanji…”164 Iye anati, “Bwanji,” anati, “kodi inu nonse mukufuna kutimukhale ophunzira Ake, inunso?” Izo ndi zabwino. Umenewondi umboni wabwino wolimba. Uwo, uwo, uwo ndi wabwino.Awo ndi maziko abwino. Uko, uko, uko ndi kuchitira umbonikwabwino kwenikweni, zimene ine ndinganene. Anati, “Kodinonse…”165 Apa pali uyu membala wamba, munthu wakhungu,ataima pa msewu atakomana naye Yesu, tsopano akuwafunsaophunzira, akuwafunsa Afarisi ngati iwo akufuna kuti akhaleophunzira Ake. “Mabishopu, akuluakulu, kodi inu mukufunakuti mukhale ophunzira Ake, nanunso?”

KUTENGA MBALI NDI YESU 843

166 Iwo anati, “Ayi! Iwe ndiye wophunzira Wake. Ife ndiophunzira a Mose.” Kuyang’ana mmbuyo kutali kudutsa mumbiriyakale, inumukudziwa. “Ife ndi ophunzira aMose.Munthuuyu, ife sitikudziwa kanthu za Iyeyo. Ife sitikudziwa kumeneIye anachokera. Chabwino, ife tiribe muyezo wa iliyonse yamasukulu athu kumene Iye anachokerako. Iye sanabwere konsendi kudzatifunsa ife za zinthu izi. Mukuona? Ife sitikudziwakanthu za Izo. Anthu inu kunja uko, inu mukuzindikirakuti Munthu ameneyo si wodzozedwa? Munthu ameneyo ndiwambwebwe kapena chinachake. Iye ndi Belezebule. Inumwakhalamukulodzedwa. Bwanji, Iye alibe ulamuliro uliwonse.Ife sitinaupereke iwo kwa Iye panobe. Mukuona? Ife sitikudziwangakhale kumeneMunthu ameneyu akuchokera.”167 Mnyamata wachikulire uyu ataima pamenepo akukhozakuwona, anati, “Tsopano, ichi ndi chinthu chododometsa.”Mukuona? Iye watsala pang’ono kuwalefula anthuwo, Afarisiawa anali, amawapangitsa iwo mantha. Mukuona? Koma iyeanali atatenga mbali ndi Yesu, mukuona, kotero iye anati, “Ichindi chinthu chododometsa.”

Ndiroleni ine ndilongosole bwino izo, mawu ena ameneiye akanati awanene. “Tsopano, anthu inu kuzungulira kunomwakhala mukuyendetsa mathero onse a zipembedzo izi kwamazana a zaka. Ndipo inu mumayankhula za Mesiya yemweakudza ndi chinachake chimene chiti chichitike mu mithunzichabe ya nthawi, pamene Muomboli akubwera kuti adzatiwoneife. Ndipo inu mumatiuza ife kuti pamene Iye abwera, i—izo zonse zimene Iye ati adzachite. Ndipo apa, inu, atsogoleriauzimu, ansembe aakulu ndi ansembe a dera lino, mwaima panolimodzi pamaso pa anthu awa, mukuyesera kuti mulidetse DzinaLake, mukuyesera kuti munene chinachake choipa momutsutsaIye. Ndipo Mwamunayo anabwera ndi kudzatsegula maso angaakhungu. Ine ndinabadwa ndiri wakhungu. Bambo anga ndi awandi amayi, akupereka umboni kuti ine ndinabadwa wakhungu.Ndakhala ndiri komwe kuno pakati panu, kwa zaka zonsezi,ndinabadwa wakhungu. Ndipo izo sizinayambe zachitikapochiyambireni cha dziko. Ndipo, apa Mwamuna wakhozakubwera ndi kudzachita chozizwitsa chimene sichinayambechachitidwapo chiyambireni cha dziko, ndipo, inu, atsogoleriauzimu, ndipo simukudziwa kanthu za izo.” Fyuu! Nhu! Anati,“Ine ndikuti ichi ndi chinthu chododometsa.”168 Iye anatenga mbali ndi Yesu. Mukuona? Iye analolezedwakuti akhale wakhungu kuti ntchito za Mulungu zidzathekuwonetseredwa, mukuona, chifukwa iye anabwera ku mbali yaAmbuye Yesu. Iye anatenga mbali ndi Iye.169 Tsopano, iye anaika mbola kwa iwo. Inu mukudziwachimene iwo anachita? Iwo anati, “Tsopano ife tikudziwakuti iwe unabadwa mu tchimo. Ukuyesera kuti uzitiphunzitsaife?” Iwo anamuthamangitsa iye kunja kwa tchalitchi.

844 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

Anamukankhira iye panja. Anamududulizira iye panja.Anamponyera iye panja.

Koma mwamsanga pamene iye anaponyedwera panja, kodiinu munazindikira? Yesu anamupeza iye kachiwiri. Ameni.Ameni. Yesu anamupeza iye kachiwiri. Kotero musamadandaulengati iwo akuponyerani inu panja. Iye akupezani kachiwiri inu.Mukuona? Chabwino.

Ndipo Iye anati kwa iye, “Kodi iwe ukukhulupirira paMwana wa Mulungu?”170 Iye anati, “Ambuye, Ndi ndani Iyeyo?” Iye sanali kudziwankomwe. Koma chinthu chokha chimene iye ankachidziwa,nkuti, pamene iye anali wakhungu, iye tsopano amakhozakupenya.171 Tsopano, ine ndikudziwa chinthu chimodzi ichi, m’bale.Iwo akhoza kumachitcha Ichi kutengeka, ndi chirichonsechimene iwo akufuna. Koma, pamene ine nthawi ina ndinaliwochimwa, i—ine ndabwera mu chisomo tsopano. Chinachakechachitika kwa ine. Mukuona? Chinthu chimodzi ichi i—ine tsopano ndikuchidziwa, pa kudalira Mawu Ake, pakumukhulupirira Iye. Ine ndakankhidwira kunja kwa bungwelirilonse pansi pa nkhope yaKumwamba. Kulibe aliyensewa iwoamene angandilandire ine kenanso. Inu mukudziwa zimenezo.Ena a amuna awo akhoza, komwe kuno. Amuna abwinoangandilandire. Koma bungwe lirilonse likundikanikizira pansiine. Ndiko kulondola. Koma Iye wandipeza ine. Iye adzandipezaine kwinakwake. Ndiko kulondola. Mukuona? Ndiko kulondola.Kubwera apo monditsatira monga choncho.172 Ndipo chotero izo zidzakhala zabwino, chifukwa ifetikufuna kuti titenge mbali ndi Yesu. Ndipo njira yokhaimene iwe ungatengere mbali ndi Yesu ndi potenga mbali ndizimene Iye ananena, kumakhulupirira Mawu Ake. Kotero tiyenitizitenga mbali ndi Iye.173 Bambo wakhunguyo anawapatsa iwo umboni weniweni.Chabwino. Ife tikupeza kachiwiri kuti iwo anayesera kutialiyipitse Dzina Lake.

Kwa pang’ono pokha, ndipo ine ndiyenera kuti ndilumphepa zinthu zina apa.

Kotero, nthawi ina, uko kunali Mfalisi. Ine ndinalalikira paizo kuno nthawi ina yapitayo, ndipo ndinazitcha izo, “KutsukaMapazi a Yesu.” Ine ndikukhulupirira inu nonse munandimvaine ndikulalikira pa izo kuno, pamene Mfalisi anamufunsa Yesukuti abwere ku nyumba yake. Mfalisi wamkulu, wokalamba,wokhuthara, ndipo anamupempha Iye kuti abwere. Ndipo inumukudziwa ine ndinapereka kasewero kakang’ono, momwemthenga anabwera ndipo anadzamupeza Iye. N—ndipo Iyeanabwera kumeneko, komabe Iye ankadziwa kuti Iye analikudedwa. Komabe, Iye anapita, mulimonse. Ndipo pamene iwo

KUTENGA MBALI NDI YESU 845

anamufikitsa Iye kumeneko, iwo sanamusambise konse mapaziAke. Ndipo anamusiya Iye kuti akhale pansi apo, akununkha,ndi chirichonse, chifukwa cha thukuta la pa msewu. Ndipo apoIye anakhala pamenepo.174 Ndipo mkazi wamng’onoyo anabwera umo. Iwo anaganiza,“O, mai, Ambuye ndi abwino kwa ife, chifukwa, taonani, izizikungobweretsa phwando lathu lalikulu!” Iwo anamubweretsaIye kumeneko kuti akangomutonza Iye. Iwo anamubweretsa Iyeuko kuti akangokhala ndi zosangalatsa naye Iye. Ndipo tsopanoiwo ankaganiza kuti Ambuye anali akugwira ntchito ndi iwo,chifukwa chakuti hule wa mbiri-yoyipa uyu anabwera uko,ndipo anali akulira ndi kumasambitsa mapazi Ake ndi misonziyake, ndi kumawapukuta iwo ndi tsitsi lake.

Ndipo Mfalisi wachikulireyo ndi ansembe ena onseataima cha pa ngodya, anati, “M’bale, chirichonse, Ambuyeanachikonza icho ndendende basi kwa ife. Apa ife tikhozakuika chopaka pa dzina Lake pakali pano. Iye akudzitchaYekha Mneneri, ndipo anthu akuganiza kuti Iye ndi Mneneri.Ndipo iwo akumutcha Iye Mneneri waku Galileya. Ndipo Iyempaka akudzitcha kuti ndi Mesiya, ndipo ife tikudziwa Mesiyaadzakhala ali Mneneri. Ndipo ndi Uyu apa, wakhala kumbuyoukoyo. Inu mukuona kumene ife tamufikitsa Iye? Taonani apo.Mnyamata, ife tafika pomupezeketsa iye pakali pano. Ndi Uyoapo, wakhala kumbuyo ukoyo, atawerama pansi ngati mwanawa garu wokwapulidwa kapena chinachake kumbuyo uko.Ndipo hule wina, wa mu gulu Lake lomwe, wakhoza kubweraapo ndi kumadzatsuka mapazi ake monga choncho, ndipotsopano Iye sakudziwa nkomwe. Ngati Iye akanakhala mneneri,Iye akanati adziwemtunduwamkazi yemwe uyo anali. Tsopano,anyamata, ife timwere pa ichi,” anati, “chifukwa, taonani uko.”Mukuona?175 Mukuona, chirichonse kuti ayipitse Dzina Lake, chirichonsekuti awononge chidaliro cha anthu, posadziwa kuti iwo analiatadzazidwa ndi Mdzierekezi kuti azichita zimenezo. Iwo analikugwira ntchito mogwirizana ndi Mdierekezi, kuyesera kutiadetse Dzina la Mwana waMulungu.176 Kodi iwo ankachita motani izi, abale? Chifukwa iwosanafufuze konse Malemba. Yesu anati, “Fufuzani inuMalemba. Mmenemo inu mumaganiza kuti inu muli nawo MoyoWamuyaya, ndipo Iwo ali Amene amachitira umboni za Ine.” O,utumiki wake umene Iye anali nawo! Mukuona? Inde, bwana.“Ngati ine sindikuchita ntchito za Atate Anga, ndiye musatimundikhulupirire Ine.” Mukuona?177 Koma apaMfarisi uyu anati, “Ife tamupezeketsa Iye tsopano.O, tayang’anani apa, mwinamwake pali anthu mazana khumindi asanu pa phwando ili. Tsopano tayang’anani pa Iye atakhalaapo. Apo Iye wakhala ndi hule.”

846 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

178 Ndipo, o, mai, chinthu choipa chomwe icho chinali mu tsikulimenelo. Fyuu! Nhu! Ndipo apo Iye anali ndi mkazi wa mbiri-yoyipa, atalowerera umo (zinkawoneka ngati) Iye analowereraumo. Iye anafika cha pa osambisa mapazi ndi chirichonse, ndipoanakhala pamenepo.179 Ndipo anati, “Ndi uyu apa, ali pamenepo akumusambisamapazi Ake. Tsopano, ngati Iye akadakhala Mneneri? Inumukuona, abale, Mwamuna uyo si Mneneri. Ngati Iyeakadakhala Mneneri, ndiye Iye akanadziwa mtundu wa mkaziamene anali kumusambitsa mapazi Ake.”180 Ndipo Yesu anangokhala ndi kumamupenya iye, sanasunthephazi mpaka iye atatsiriza. Ngati inu mukati mumuchitirechinachake Yesu, Yesu amangokhala ndi kumakupenyani inumukuchita izo, nthawizina. Nhu-hu. Iye amakulolani inukuti mupitirire nazo mpaka inu mutsirize, ndiye mphotoimabwera. Mwinamwake inu muyenda liwiro lonse la moyo,mukumugwirira Iye ntchito, koma, musadandaule, ilipo mphotopamapeto, ngati inumungotenga njira yanu ndimbali Yake.181 Mwina inu simu—simuti mumuwone munthu mmodziatachiritsidwa, amene inu munamupempherera. Zingopitirizanikuwapempherera iwo. Ine kawirikawiri ndakhala ndikunenakuti, “Ngati ine ndikanapempherera mazana asanu usikuuno;mazana asanu onsewo nkufa pofika mmawa; mawa usikuine ndidzakhala ndikulalikira machiritso Auzimu ndikumapempherera odwala.” Mukuona? Ndiribe kanthu kamodzikochita nazo izo. Mukuona?182 Iye azikulolani inu kuti mufike kumene pa kulephera ndichina chirichonse, mpaka inu mufike kumene ku mapeto amsewu ndi kutsiriza ntchito yanuyo, monga Iye anamutsogoleramkazi ameneyo. Iye ankafuna kuti amuchitire Iye ntchito, koteroIye anangogwirizitsa mapazi Ake pamenepo ndi kum—kumusiyaiye awasambitse iwo. O, ngati Iye akanati, “Usati uchite izo,” iyeakanalumpha ndi kuthawa. Koma Iye anamusiya iye kuti achitentchitoyo.183 Ndipo pambuyo pake iye atatsiriza, atatha ntchitoimene amati aichite, ndiye Iye anayang’ana mmwamba kwawachinyengo uja atayima kumbuyo uko, anali kuyesera kutiaponyere mdima pa Dzina Lake. Anati, “Simoni, ine ndiri ndikenakake koti ndinene kwa iwe; osati kwa uyo, koma kwa iwe.Iwe, utaima kumbuyo uko, mu mtima mwako, icho ndi chifukwachimene iwe unandibweretsa Ine kuno. Iwe ulibe chiyanjano ndiIne. Kodi ine sindimadziwa izo? Koma iwe unandibweretsaIne kunoko. Ndipo iwe unandikhazika Ine kumbuyo kuno,kuti uzinditonza Ine. Kundisiya…Iwe sunandipatse konseIne madzi, kuti ndisambitse mapazi Anga. Iwe sunandipatseIne kanthu koti kandiziziritse Ine. Ine ndinakhala pamenepo,ndikutenthedwa ndi kumapwetekeka, iwe sunandipatse konse

KUTENGA MBALI NDI YESU 847

Ine mafuta a pa nkhope Yanga. Iwe unachita manyazi kutiundipsyopsyone Ine pondilandila, kapena kugwedeza dzanjaLanga. Mukuona? Iwe umachita manyazi, pamaso pa gulu lako.Iwe umachita manyazi kuti uchite izo. Mkazi uyu, chibwererenichake muno, iye sanachite china koma kupukuta mapazi Angandi kuwasambisa iwo ndi misozi yomwe ya mmaso mwake,kuwapukuta iwo ndi chopukutira cha tsitsi lake lomwe. Ndiye,Ine ndingokusonyeza iwe ngati ine ndiri Mneneri, kapena ayi.”Ameni. Ine ndikuzikonda zimenezo.184 “Tsopano ine ndikufuna kuti ndiyankhule kwa iwe, minitiyokha. Machimo ako, amene ali ambiri, onsewo akhululukidwa.”Nhu!185 Kodi iwo analiipitsa Dzina Lake? Iwo ankaganiza kuti iwoanali atalitero Ilo. Iwo ankaganiza kuti anali ataliimitsa Ilo. Iwoankaganiza kuti iwo anali atathana naye Iye kuti chitsitsimutsoChake sichikanatha kukhala chiri mmudzi umenewo. Iwoankaganiza kuti anali ataipitsa chikoka Chake. Koma izozinangotengera munthu mmodzi amene anamukonda Iye, kutiasinthe chikhalidwe chonsecho.186 Inumukudziwa bwanji kuti simunthu ameneyo,wa kumudzikwanuko kapena winawake amene inu muti mukomane naye?Tengani mbali ndi Iye. Zimuchitirani Iye ntchito. ZimuchitiraniIye chinachake. Mukudziwa chimene ine ndikutanthauza,abale? [Abale ati, “Ameni.”—Mkonzi.] Tengani mbali yanu ndiYesu. Mutengeni Iye, mupangeni Iye akhale kusankha kwanu.Zimuchitirani Iye ntchito mosalabadira kaya winawakenso,kapena inu mudzalipidwa konse, kapena chirichonse. Sizipangakusiyana kulikonse. Dikirani mpaka ntchitoyo itatha.187 Kodi inu mukanakonda bwanji Iye titi…Ngakhale inumukanawapempherera odwala, ndipo iwo akanati asakhalebwino. Ngakhale iwe unapemphera mpaka iwo kufikapoyankhula ndi malirime, ndipo inu nkusazichita izo. Inumukanapemphera mpaka kulosera; inu osazichita izo. Koma,apobe, chinthu chokha chimene inu munachita ndi kuwauzankhani ya Yesu, mu mpingo wanu, kapena mmudzi wanu, kuntchito kwanu. Inu simukanatha ngakhale kuchita chinthuchimodzi; simunati mumutsogolere munthu mmodzi. Mkaziujayu sanamutsogolere mmodzi kwa Khristu, koma iyeanamuchitira Iye ntchito. Ndipo kodi izo zikupanga kusiyanakwanji, pa mapeto a msewu, ngati Iye adzati, “Ndipo inendikunena kwa iwe, machimo ako onse, ngakhale mwinapalibe pemphero limodzi linayankhidwa kwa iwe. Koma, iweunabwera pa maziko a Mawu Anga. Iwe unabwera chifukwaiwe unandikhulupirira Ine, ndipo iwe unandichitira Inentchito. Ndipo ine ndikunena kuti machimo ambiri amene iweunawachita onsewo akhululukidwa kwa iwe”? Izo zidzakhalazabwinomokwanira kwa ine. Ameni. Inde, bwana. Chabwino.

848 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

188 Iwo akufuna kumanena kuti, “Masiku a zozizwitsa anapita,”n—ndi zina zotero. Asiyeni iwo azipitirira nazo kumanena izo.Koma tiyeni ife tizichitira ntchito kwa Ambuye.

Iwo ankamuda Iye chifukwa iwo ankamuchitira Iye nsanje.Ndicho chifukwa chokha. Iwo ankachita nsanje.

Iwo ankayesera kuti awononge chikoka Chake pamaso paanthu, mofanana monga iwo akuchitira tsopano. Iwo, ngatiiwo angathe basi-… kuwononga chikoka cha Uthenga pamasopa anthu, ndiye iwo akhala atagonjetsa chinthucho. Ndikokulondola. Chifukwa, chifukwa chiani iwo ankayesera kuchitazimenezo? Chifukwa Iye anali kutsutsana ndi tizikhulupirirotawo tonse ndi ziphunzitso zawo zonse za mpingo, ndichirichonse chimene iwo anali kukhulupirira mwa izo, ndipoankazitcha zawo zonse—zikhulupiriro zawo zonse ndi zinazotero. Iye anali kutsutsana nazo izo zonse. Ndipo iwo ankamudaIye chifukwa Iye sanali kugwirizana nawo iwo.189 Tsopano, ngati Iye akanabwera umo, ndi kuti, “O, Kayafa,munthu wonyumwitsa wa Atate Anga. Ine ndine Mesiya. Bwerakuno, Kayafa. Kodi iwe ukuwawona madzi awo apo? Iweukukumbukira, kujaku m—mu Igupto, Mose, mneneri wamkuluanawasandutsa iwo kukh—kukhala magazi. Iwe ukukumbukirazimenezo, Kayafa?”190 “O,Mnyamata iwe, ine ndikuidziwa bwino nkhani imeneyo.”191 “Chabwino, Kayafa, ine ndikuti ndiwasandutse madziwotsopano, kuchokera ku madzi kukhala magazi, kutindikusonyeze iwe kuti Ine ndine Mneneri Ameneyo yemweMoseankamukamba. Ndi izo apotu, Kayafa. Kodi iwe ukuganizachiani za izo?”192 “Kodi iwe ukuganiza chiani za Kayafa kukhala Mfarisi?Kodi iwe ukuganiza chiani za Afarisi?”193 “O, ine ndikuganiza iwo ndi mtundu wonyumwitsa waanthu. O, inu nonse mumasunga miyambo ya makolo ndendendebasi.”

“Iwe ukudziwa, Iwe ukhoza kukhalaMesiyayo.”194 Ayi. Iye sakanati akhale ali. Icho chikadakhala chikhomochomwe choti Iye sanali. Pamene inu mumuwona winawakeakubwera, ndi kuti, “Bwerani kuno ndipo ine ndikuwonetsaniinu zimene ine nditi ndichite. Ndipo bwerani kuno, ine ndichitaizi ndi kuchita izo.” Inu mukumbukire, pomwe pano, palichinachake chamdima pa izo, pa kuyamba pomwe.

Yesu anati, “Ine sindichita kanthu mpaka Atateatandisonyeza Ine, poyamba.”Mukuona? Inde.195 Iye anali motsutsana nawo iwo. Iye ankaphunzitsamotsutsana nawo iwo. Iye ankatsutsa kusunga kwawo kwaSabata. Iye ankatsutsa momwe iwo ankavalira. Iye ankatsutsanjira zonse za moyo wawo, miyambo yawo yonse, kutsuka

KUTENGA MBALI NDI YESU 849

kwawo kwa miphika, ndi kutsuka kwa ketulo, ndi kusamba kwamanja, ndi china chirichonse. Iye ankazitsutsa izo, chaching’onochirichonse. Mavalidwe awo, Iye anati, “Inu mumavala zovalazopetedwa, ndipo mumakhumba mipando yapamwamba, n—ndi kupanga mapemphero aatali, ndi kumawononga makomoa akazi amasiye.” Anati, “Inu mudzalandira chiweruzochochuluka.”

“Chabwino, kumbukirani, ndineDokotalaWakuti!”196 “Ine sindikusamala yemwe inu muli.” O, amuna, Iye anaikaizo apo kwenikweni. Iwo sanati…Bwanji? Chifukwa iwo sanalikumukhulupirira Iye. Iye anali Mawu. Mukuona? Iye analikuyesera kuti aswe gulu la zamalamulolo.

Ndipo ngati Iye akanakhala pano pa dziko lapansi lero, Iyeakanayesera kuti achite chinthu chomwecho.197 Anthu ena amati, “Chabwino, tsopano, dikirani miniti.Ife timasunga Sabata, nthawizonse. Ife timachita izi. Ndipo,inu mukudziwa, ife timasunga zonse izi, ndipo timasungaizo. Ndipo lirilonse…Bwanji, pa Lachisanu Labwino lirilonse,moti, pamene nthawi yosala ibwerapo, masiku makumi anaiisanafike Isitara, ife nthawizonse timakumbukira Mapulusa. Inendimapuma kusuta, kwa masiku makumi anai. Ine ndimapumakumwa, kwa masiku makumi anai, isanafike, mu nthawi yaMapulusa.” O, miyambo ya makolo, za mwamalamulo. Ngatiinu mukumukonda Mulungu, i—inu simumasuta, pa kuyambapomwe. Iwe ukumukonda Mulungu, iwe…i—ine ndinazilembaizo ku chikutiro kwa Baibulo langa laling’ono, loyamba limeneine ndinayamba ndakhalapo nalo. Ine ndinati:

Musati muzindifunsa ine mafunso opusa.Gamulani izi mu malingaliro anu,Ngati inu mukuwakonda Ambuye ndi mtimawanu wonse,

Inu simukhoza, kumwa, k—kapena…Simumakhoza kusuta, kutafuna, kapenakachaso aliyense.

198 Ndipo izo zinali kuima bwino mpakana lero. Inesindimachita izo chifukwa ine ndikuganiza Iye akanatiandiweruze ine pa kuchita izo. Ine ndingasiye izo chifukwandi chinthu chonyansa, ndipo si choyenera kwa mtumiki. Ndikokulondola. Ine sindikanati ndinene…199 Nthawi zambiri ine ndimapita ku manyumba ndipo ukokumakhala akazi ataima kunja uko. Ndipo ine ndimapita kunyumbayo, kugogoda pa khomo, ndipo mlongo nkubwera pakhomo, “Lowani mkati, M’bale Branham.” Ngati mwamunawake Sali mmenemo, kupatula itakhala nkhani ya matendandipo ndiri ndi winawake limodzi nane, ine sindimapitamo.Ndiyeno iwo amandiitanira ine ku chipatala, kapena kuchipinda, nkuti, “M’bale Branham, bwerani kuno. Ine ndi

850 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

Mlongo Wakuti-n-wakuti wochokera Kwakuti-n-kwakuti. Ine—ndiri kuno ku hotelo. I—i—ine ndawabweretsa amayi anga. Iwoakudwala.” Ine ndimatenga mkazi wanga. Ngati ine sinditero,ine ndimamutenga m’bale wina. Mukuona? I—ine sindiri. Inesindiri kuganiza…200 Ine ndikuganiza izo zikanakhala zabwino bwino kuti inendipite mkati umo, koma bwanji ngati winawake andiwona inendikupita mkati umo? Mukuona? Bwanji ngati wina andiwonaine ndikuchita izo? Mukuona? Ndiye, chinthu choyamba inumukudziwa, iwo angati, “Iye anapita mkati umo momwemkazi uja anali. Iye akuthamangira akazi.” Izo, mwaona,icho chikanati chikhale chinthu chimene ine sindimayenerakuchichita. Mukuona? Inu musamachite konse chinthuchirichonse chonga icho, chifukwa iwe umaika chopunthwitsamu njira ya winawake. Mukuona? Ine sindikukhulupirira kutiine ndikanati ndichite chinthu chirichonse cholakwika mkatiumo. Ndikanati, ine ndikanatero, ndi kudalira Mulungu kutindipite mkati umo. Ziribe kanthu chomwe chinthucho chinali,ine ndikanadalira Mulungu. Koma, apobe, mukuona, n—n—ndipo ine ndimawakonda Ambuye bwino mokwanira mpaka inesindikanati ndichite zimenezo. Mukuona? Ndi chikondi chimeneiwe uli nacho. Iwe, iwe suli kuchita izo chifukwa ndi ntchitokuti uchite izo. Iwe ukuchita izo chifukwa iwe umawakondaAmbuye. Iwe sukusowa kuti uzichita izo, koma iwe umachitaizo, mulimonse.201 Paulo anati, “Kwa ine zinthu zonse ndi zololezedwa, komasi zonse zomwe ziri zopindulitsa.” Mukuona? Paulo akanakhozakumachita zinthu zambiri zimene mwinamwake kuti iyeankadziwaAmbuye ankamumvetsa iye, ndipo ankamudalira iye,koma izo sizinali zopindulitsa kwa iye kuti achite izo.

Kotero iyo ndi njira imene amwamalamulo awa, amayeserakunena, “Masikumakumi anai isanafike Isitara, ife nthawizonsetimayamba ndi kusala.” Ndipo iwo amadya mochuluka basimomwe iwo nthawizonse amachitira. Mwinamwake iwo amati,“Chabwino, ine sindimakonda nyemba, kotero ine ndisiyakudya nyemba, kwa Mapulusa.” Ine ndawavapo iwo akunenazimenezo. “Ine sindikonda nkhumba, kotero ine ndingosiyakudya nkhumba, inu mukudziwa. Ine ndikuti ndisiye kumwa,chifukwa cha Mapulusa.”202 Mkazi wina anandiuza ine, anati, “Inu mukudziwa chimeneine ndinasiya, kwaMapulusa chaka chino,M’bale Branham?”

Ine ndinati, “Ayi. Nchiani?”203 Anati, “Maswiti.” Anati, “I—ine sindimasamala kwambiri zaiwo, mulimonse.” Mukuona?204 Ndi inu apo. Tsopano, iwo amakutcha uko kusala. Mukuona?Zamwachilamulo. Iwo amati, “Chabwino, ine ndiyenera kutero.Inu mukudziwa, i—i—i ndakhala ndikuzandima popita ku

KUTENGA MBALI NDI YESU 851

tchalitchi kwa nthawi yaitali. Chifukwa, ine ndikukuuzani inu,ine ndakhala ndikupita ku Sande sukulu kwa chaka chathunthu,chifukwa aphunzitsi anga anati kuti iwo adzapereka Baibulokwa amene sanaphonye tsiku.”205 Tsopano, m’bale, iyo ndi njira ina yopitira. Ine kulibwinondingopita ndikadzigulire ine Baibulo. Mukuona? Ngati iwesumapita ku tchalitchi chifukwa iwe umawakonda Ambuye, iweukanangoti uzitalikirako. Ndizo zonse. Mukuona? Chifukwa,iwe umapita uko pakuti iwe umamukonda Mulungu. Inendikuganiza za nyimbo iyi imene ife timaimba.

Chodala chikhale chimango chimenechimangiriza

Mitima yathu mu chikondi Chachikhristu;Chiyanjano cha a mtima wapaubaleChiri chonga icho cha kumwamba.Pamene ife tipita kosiyana,Zimapereka kupweteka kwa mkati;Koma ife tidzakhala olumikizanabemumtima,Ndi kuyembekeza kuti tidzakomanenso.

206 Mukuona? Ndi zimenezo. “Pamene ife tipita mosiyana,izo zimatipatsa ife kuwawa kwa mkati.” Ine ndawonaponthawi, m’bale. Ndisati ine ndiweruze ife, koma ndiloleni inendingodzutsira ifeyo ku chinachake. Ine ndawonapo nthawi mumpingo uno, zimene pamene anthu ankachita kudikirira mpakaLachitatu usiku kuti akomane wina ndi mzake, iwo ankachitakulirira izo. Ndipo uko ndi kulondola. Ine ndawonapo atumikiakubwera muno ndi kumati, “Kodi inu mumachita bwanji izo?”Chabwino, anthu amenewo, ndi amtima umodzi basi.Mukuona?207 Iwo amakomana pakhomo ndi kuti…Alongo amenewokukomanawina ndimzake kumbuyo uko, ndi kumakumbatiranawina ndi mzake, ndi kumati, “Mlongo, mutsimikize kutimukakhale mukundipempherera ine tsopano. Wokondedwa, inendidzakuwonaninso inu Lachitatu usiku. Inu muzipemphera,sichoncho inu? Inu muzindipempherera ine. Ine ndikakhalandikukupemphererani inu.”Ndi kumapanga izomonga choncho,ndi misozi mmaso mwawo.208 Kuwona abale akugwirana chanza wina ndi mzake, ndipokumalephera kuti achoke kwa wina ndi mzake monga choncho.Chimenecho ndicho chiyanjano chenicheni cha Chikhristu,mwaona, mwaona, kumangoyembekeza, kupemphererana winandi mzake. Inde, bwana. Umo ndi momwe ife tikuyenerakumakhalira tiri. Chabwino.209 Tsopano, amuna awa amene anapanga maneno awa, iwosanali anthu oyipa. Iwo sanali kutanthauza kuti akhale oipa. Iwoankaganiza kuti iwo anali kumuchitiraMulungu ntchito. Afarisiaja ndi zinthu, iwo sanali otcheza mowa ndi zidakhwa. Iwoanali anthu achipembedzo. Iwo sanali oipa. Iwo basi—iwo sanali

852 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

kuvomereza kokhaMawu a Choonadi. Iwo sanali kuwuvomerezaMzimu. Bwanji? Iwo ankagwiritsitsa kwa tizikhulupiriro tawondi m—miyambo ya atsogoleri awo. Mukuona? Izo zinkasonyezakuti iwo ankawakonda atsogoleri awo.210 Apa pali Kayafa wamkulu, wansembe wamkulu. Awo ndiansembe ena onse aakuluwo, ndipo amuna awo ankapitiralimodzi.

Tsopano, inu mutenge, monga Katolika. Iwo…Osatikuponyera panja kwa iwo. Chinthu chomwecho muChiprotestanti. Inu mutenge Mkatolika, iye amamukondawansembe wake. Ndi—ndipo ine ndikamamuuza iye za Mawu aAmbuye, nd—ndipo iye nawona ntchito za Mulungu. Iye amati,“Koma m—mpingo wanga sumakhulupirira Zimenezo.” Ndipoiwe ukapitirira kuyankhula, ndi kumulasa iye. Ine nkuti…

Mkazi anati kwa ine, tsiku lina, anati, “Ndi tchimo kuti inendizimvetsera kwa inu.”Mukuona? Iye sanali kufuna kuti akhalewoipa. Iye ankangoganizamochuluka kwambiri zampingowakendi wansembe wake, mpaka, ngati iye akanati amvetsere kwachina chirichonse. Iye anali womvera kwawansembe ameneyo.211 Amboni za Yehova ndi omvera ku zimene iwoamakhulupirira. Abaptisti ndi omvera ku zimene iwoamakhulupirira. Apresbateria ndi omvera ku zimene iwoamakhulupirira. Ndipo iwo ndi omvera basi kwa abusa awo.Kodi ife sitingathe kukhaka omvera chomwecho kwa Mawu?Mukuona? Tsopano ngati amenewo…212 Ine ndikufuna kuti ndikufunseni inu chinachake. Inumukuti, “Chabwino, M’bale Branham, inu mukudziwa bwanjikuti iwo sali?”

Tsopano, ngati Afarisi aja ndi Asaduki, ndi atsogoleri a tsikulimenelo, akanati achoke ku tizikhulupiriro tawo ndi mbalumezawo ndi kumvetsera ku zimene Mawu ankanena ndi zimeneYesu ankawauza iwo, ndendende basi zimeneMesiya ankayenerakuti adzachite, iwo akanati agwiritsitse kwa Iye. Mukuona?Koma iwo ankaganizamochuluka kwambiri za atsogoleri awo!

Iwo sanali anthu oipa. Iwo sakanati abe, aname, kutukwana,chirichonse monga choncho. Iwo sakanati achite zimenezo.Iwo sakanati achite chigololo. Bwanji, ndithudi ayi. Bwanji,iwo akanati achitire umboni kugendedwa kwa mmodzi ameneakanachita chinthu choterocho. Ndipo iwo sakanatero. Iwosakanati achite zimenezo. Iwo anali anthu abwino.

Koma chinthu chokha icho chinali, iwo sanali anthuauzimu. Mwamakhalidwe, iwo anali abwino, koma izo sizomwe zimawerengedwa. Ndipo kodi Yesu anawauza chiani iwo,ngakhale anthu omvera awo? Iye sanati, “Ndinu a atate wanu,Mdierekezi.”Mukuona?NdiMawu amene amawerengedwa.

KUTENGA MBALI NDI YESU 853

Tsopano ine ndifulumira mwamsanga basi mmenendingathere.213 Tsopano, iwo sanali odzazidwa-Mzimu, koma iwo analiomvera ndipo ankagwiritsitsa ku tizikhulupiriro tamakonota atsogoleri awo. Mukuona? Chabwino. Utumiki wake unalikusonyeza apo chiphunzitso chawo. Ilo ndilo vuto. Tsopanopenyani. Ine ndingotenga izo. Tsopano basi…

Abale, i—ine, ndiri—ine ndikuti ndikufunseni inu,ndikhululukireni ine, pakali pano, chifukwa chotalikitsachomwechi. Ndine…Mwinamwake inu simungafune kuti inekuti ndidzabwerere kwa wina. Koma, penyani. Tamvetseranikwa izi. Mukuona? Ine ndikufuna kuti inu mutsimikize kutimuzimvetse izi.214 Tsopano, iwo anali nato tizikhulupiriro tawo, ndipo ukokunali mipingo yaikulu ndi anthu aakulu, ndi amuna aakulu,amuna oyera, anthu abwino, njonda, anthu abwino, anthuolemekezeka, anthu aulemu, ophunzira, anzeru, achipembedzo.Ndi kulondola uko? [Abale ati, “Ameni.”—Mkonzi.] Ndipoife tonse tikudziwa zimenezo. Mwabwino basi monga inumungazipezere izo kulikonse. Mukuona? Koma pamene Yesuanabwerapo, utumiki Wake unasonyeza apo chiphunzitsochawo, chifukwaMulungu anali akutsimikiziramwa utumiki waYesu Khristu kuti Iye anali naye Iye.215 Kodi Petro sananene mobwereza chinthu chomwecho? Iyeanati, “Inu amuna a Israeli, mulole ichi chidziwike kwa inu,ndipo mvetserani kwa mawu anga.” Iye anati, “Yesu wakuNazareti, Mwamuna wotsimikiziridwa ndi Mulungu pakatipanu.” Mukuona? Mukuona? Ngati iwo…216 Monga munthu wakhungu uyu anati, “Kodi ichi si chinthuchododometsa? Inu ndi atsogoleri auzimu a fukoli, ndipo apapabwera Munthu ndipo watsegula maso anga mwa mphamvuya Mulungu, ndipo komabe inu simukudziwa kanthu za Iye.”Iye anati, “Ichi ndi chinthu chododometsa.” Iye anali ndichinachake. Sichoncho iye? Iye zedi analidi. Chabwino. Iyeanalidi.Mwamuna amene angathe kuchita izi, ndipo komabe iwosanali kudziwa kumene Iye anachokera. Tsopano icho chinalichinthu chododometsa.217 Tsopano yang’anani pa lero, abale. Mukuona? Ife tiri…Ife tikudziwa kuti ife tiri nako kusuntha kwa Mulungu. Ifetikudziwa kuti Iko kukuchita zozizwitsa. Iko kukuchiritsaodwala. Iko kukuukitsa ngakhale akufa. Iko kukutulutsaziwanda. Iko kukuyankhula ndi malirime ndi kutanthauziramalirime. Iko kukutumizapo maulosi; izo zikuchitika.Iye watiwonetsa ife maloto, kutanthauzira; mwangwiro,mosamalitsa. Ndiye kodi si chinthu chodabwitsa kuti atsogoleriaakulu angamanene kuti ife ndife gulu la anthu openga, pamene

854 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

iwowo ali atsogoleri a fuko, atsogoleri a mipingo? Icho ndichinthu chododometsa.218 Kodi ndi chiani icho? Iyo ndi nsanje apabe. Mzimu ndimphamvu ndi Mawu a Mulungu mu masiku otsiriza anozikusonyeza apo mbalume zawo ndi tizikhulupiriro, ndizo zonsezimene ziripo kwa izo, zimene awapangitsa nazo anthu khungu.

Kotero, abale anga achichepere, inu nonse amene mukupitakuno mu mipingo iyi, gwiritsitsani ku Mawu a Mulungu. Inumusati musunthe. Ngati inu simungazifikitse izo poti zichitike,musati muziima mu njira ya winawake. Imani pamenepo, ndikumamenya pa khomo la chipata, kumangolozera kwa izozomwe. Ndiko kulondola. Khalani apo pomwe. Musati muyambekutentheka, chifukwa izo ziwonetsani inu apo. Koma ngati inumukhala woona ndi woyera, ndipo muli ndi Mawu amenewo,Mulungu akutsimikizirani inu. Ndiko kulondola.219 Utumiki wake unali kuyalutsa tiziphunzitso tawondi mbalume. Kotero iwo anatenga mwayi uliwonse kutiamuchotsepo Iye, umene iwo akanati awupeze. Chirichonsechimene iwo akanati achipeze, choti amuchotsere nacho Iye, iwoankachichita icho. Kuyesera kunena kuti, “Chabwino, tsopano,penyani apa. Penyani apa,Wakuti-n-wakuti, mmodzi uyu.”220 Ndi Uyo apo, atakhala apo, tsiku lina, mu nyumba yaSimoni, wakhate. Panalibe mawu amodzi ananenedwa kuti Iyeanamuchiza iye. Iye anali wakhate. Palibe chikunenedwa kutiIye anamuchiza iye. Ndiko kulondola.221 Iye anadutsa pa thamanda la Betsaida, ndipo apopanali pafupi anthu zikwi ziwiri, olumala, akhungu, mbuu,okwinyata. Ndipo Iye anayenda napita kwa mwamuna mmodzindipo anamuchiritsa iye, ndipo anayenda nachokapo. Akuti,“Chabwino, tsopano, ngati Iye akanakhala Mesiya, Iyeakanawachiza onse awo. Ngati Iye akanakhala wodzaza ndichifundo monga inu nonse mukuti Iye ali, Iye akanachitirachifundo pa onse awo.”

Chirichonse chimene iwo akanatha kuchipeza, chotiaponyere chilembo chakuda pa Iye, iwo ankachichita icho.Chirichonse chimene iwo akanachipeza, iwo ankachiponyeraicho pa Iye. Chabwino. Iwo ankatenga mwayi uliwonse umeneiwo akanaupeza, kuti amchotse, kuti amchotsepo Iye.222 Ankafunsa mabadwidwe Ake. Kubadwa kwake kunali pafunso. Iwo ankaziika izo pamaso pa anthu. Iwo sakanathakumvetsa momwe Iye anabadwira mwa kubala kwa namwali,ndipo Yosefe, bambo ake, ankayenera kukhala ampalamatabwa.Ndipo Iye anabadwa Yosefe ndi Maria asanakwatirane. Iwoankaponyera izo pamaso pa anthu. Inde, bwana. Mukuona? Kodiine ndikunena chiani tsopano? Iwo ankaika chodetsa pa Iye.Mukuona?

KUTENGA MBALI NDI YESU 855

223 “Tayang’anani pa iye. Kodi iye anachokera kuti?Tayang’anani pa amayi ake, wosaposa hule la mu msewu,anabala mwana uyu. Ndipo mwanayo atabadwa…Iye analikale ndi pakati, mwanayo anali woti abadwe, ndiye Yosefeanamukwatira iye, kuti abise izo, ndiye nkubwerapo ndimtundu wina. Bwanji, ndi ntchito ya Mdierekezi. Kodi inusimukutha kuwona? Ndi mtundu umenewo wa mabadwidwe.”Iwo ankaponyera izo pamaso pa anthu, osati powerenga muBaibulo.

Yesaya 9:6, “Namwali adzaima.” Mwaona? Kodi chinalichiani icho? Iwo anapita kutali ndiMawu. Ndi zimenezo.224 Iwo anaponyera zilembo zakuda pa ulamuliro Wake.“Njondanu, kodi inu simukudziwa kuti ife ndi ophunzira aMose? Kodi inu simukudziwa kuti ife ndi antchito a Khristu?Kodi inu simukudziwa kuti ife timafufuza Malemba pa tsiku,ndipo ife tiribe chinthu chimodzi?” Iwo ankati, “Mesiya akanatiadzabwere ku kachisi Wake. Palibe mawu amodzi a Iye kubweraku kachisi. Kodi Iye alikuti? Kodi Iye anachokera ku sukulu iti?Funsani aliyense wa abalewo, onse Amethodisti ndi Abaptisti,ndi Aprebateria, inu mukudziwa; Afarisi, Asaduki, ndi enaotero. Kodi iye amayenda ndi khadi yanji ya chiyanjano?Kodi ulamuliro Wake uli kuti ngakhale kuti azilalikira? Iyesanadzozedwe. Iye alibe ngakhale ufuluwoti azilalikira.”225 Iye anati, “Kudzozedwa kwanga nkochokera kwa Mulungu.Ntchito zanga zikutsimikizira chimene ine ndiri.” Ndikokulondola. “Ine sindikusowa kuti ndikhale ndimapepala anu.”226 Mukuona chimene ine ndikutanthauza? Iwo amaponyerazimenezo, Chiphunzitso Chake. Mwakuti, iwo anamutcha IyeBelezebule. Chiphunzitso Chake, iwo samatha kuchimvetsa.227 “Mwakuti, Iye akutsutsana ndi miyambo yonse ya makolo.Iye akutsutsana ngakhale ndi Afarisi. Iye akutsutsana ndiAsaduki. Iye akutsutsana ndi gulu lonse la iwo. Tsopano, kodiIye akuchitenga kuti Chiphunzitso Chakecho?” Kuchokera muBaibulo, ndithudi.

“Chabwino,” inu mukuti, “chabwino, kodi ine ndikudziwabwanji kuti Izo nzolondola?”Mulungu akuyimira kumbuyo izo.

Ndi zimene munthu wakhungu ananena. “Ndi chinthuchachilendo, ngati inu mukulondola ndipo Iye akulakwitsa.Komabe Iye wakhoza kutenga mphamvu ya Mulungu ndikutsegula maso anga, ndipo inu simunayambe mwaziwonapoizo zitachitidwa, ngakhalebe. Icho ndi chinthu chachilendo.”O, mai! Ine ndikukonda kutenga mbali ndi Iye. Sichonchoinu? [Abale ati, “Ameni.”—Mkonzi.] Zedi. “Inu mukuti inu ndiophunzira aMose, ndipo inumukulondola kwambiri ndipo Iyeyoakulakwitsa kwambiri, ndiye ndiroleni ine ndikuwoneni inumukuchita zinthu zimene Iye akuchitazi.” Ameni.

856 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

228 Apa ndi pamene, Chiphunzitso Chake, iwo anamukana Iye,zodzinenera Zake zonse. Iwo anati, “Iye alibe…ZodzineneraZake ndi zolakwika, za kukhala Mesiya. Iye angakhale bwanjiMesiya, nkusamabwera ku tchalitchi? Iye akanakhala bwanjiMesiya? Ndipo ndi ife pano, zonona za Israeli.”

Koma zononazo zinali zitasasa. Mukuona? O! Inde, bwana.Zinali ndi ntchentche mmenemo, kotero i—iwo anachitakuziyengula izo kuzichotsapo.229 Kotero iye anati, “Ndi ife pano, mpingo, osankhidwa.Ndife…Ife tausunga mwambowu. Ife tawasunga malamulo aMose. Ife tachita zinthu zonse izi, ndi konseko monga chonchi.Ndipo apaMunthu uyu akubwerapo ndi kunyozetsa zodzinenerazathu. Ndipo pambali pa izo, wansembe wathu woyera, bambowathu woyera, amene anachita izi ndi amene anachita izo, ndimtundu wonse uwu wa zinthu, ndi amuna athu onse aakulu,ndipo Iye akuzitcha izo ‘za Mdierekezi,’ ndiye akumadzitchaYekhaMwanawaMulungu.” O, mai! Mukuona?230 Iwo ankayesera kuti aponyere mithunzi imeneyo pa Dzinala Yesu, ndi pa Yesu, kuti azitengere izo pamaso pa anthu.Zochuluka zambiri zikhoza kunenedwa pamenepo, koma izozitenga nthawi yochuluka kwambiri. Koma chiani? KomaMawundi ntchito zinkamutsimikizira Iye. Ameni.231 O, kwa okhulupirira owona, okonzedweratu ameneanakonzedweratu kuti adzamuwone Iye ndi kudziwa utumikiWake, apo Iye anali. Ziribe kanthu ngati Iye sanatsegule konsekamwa Yake pa chirichonse, iwo ankadziwa kuti Iye anali.Aleluya!232 Hule wamng’ono wakale uja anayenda napita ku chitsimekuja tsiku lijali, atatenga mtsuko wa madzi. Ndipo Mwamunawausinkhuwapakati atakhala pamenepo, anati, “NdibweretsereIne okumwa.”233 Iye anati, “Bwanji, si mwambo wake kuti inu Ayudamumupemphemkazi wachi Samaria motero.”

Iye anati, “Koma ngati iwe ukanamudziwa Yemwe iweukuyankhula naye!”234 “Tsopano,” iye amaganiza, “apa pali Myuda wochenjera.”Iye anapotoloka, ndipo anati, “Ine ndikuwona InuNdinuMyuda.Ndipo ngati Inu muli Myuda, ndithudi, Ndinu wachipembedzo,ndipo Inu mumati, kumapembedza ku Yerusalemu. Komakholo lathu, Yakobo, ankamwa kuchokera ku chitsime ichi,ndipo ankamwetsera ng’ombe zake pano. Ndipo madziwa ndiokuya, ndipo Inu mulibe kanthu koti mutungire. Ndipo ifetimapembedza mu phiri ili.”235 Iye anati, “Ima miniti yokha. Pita ukamutenge mwamunawako ndipo mukabwere kuno.”

Iye anati, “Ine ndiribe nkomwemwamuna.”

KUTENGA MBALI NDI YESU 857

236 Iye anati, “Iwe wandiuza zoona.” Anati, “Iwe wakhala ulinawo asanu. Iwe unali nawo asanu, ndipo mmodzi amene iweukukhala naye pano si wako.”237 Wachiwerewere wamng’ono uja, wokonzedweratu, inendikutha kumuwona iye akutula mtsuko uja pansi, ndipo iyeakuti, “Bwana, ine ndazindikira kuti Inu ndinu Mneneri.”Mukuona? Mukuona?238 Mbewu ija inali ili mmenemo. Chinthu chokha chimene Iyoinkasowa chinaliMadzi, ndipoMadzi anali atagwera pa iyo.239 Pamene Iwo anagwera pa Afarisi aja, iwo anati, “Iyendi Belezebule.” Sanathe kubalapo kanthu. Munalibe kanthukalikonse umo, komamaudzu, oti atulukiremo.240 Koma pamene mbewu yokonzedweratu ija inakhudza MadziaMoyo aja, iye anati, “Bwana, Inumuyenera kuti ndinuMneneri.Ine ndikudziwa kuti pamene Mesiya adzadza, Iye azidzatiuza ifezinthu zimenezi.”

Iye anati, “Ine ndine Iye, amene ndikuyankhula kwa iwe.”241 Iye anausiya mtsuko umenewo, ndipo anapita mu mzinda!Iye anali ndi chinachake choti akanene. Iye anati, “Bwerani,mudzamuwone Mwamuna Yemwe wandiuza ine zinthu zimeneine ndimazichita. Kodi ameneyu si Mesiya yemwe?” Mukuona?Iye anatengambali ndi Yesu. Ndiko kulondola.242 Chinthu chachirendo, sichinali icho? Afarisi onsendi Asaduki sanamudziwe Iye, ndipo wachiwerewereuyu anamudziwa Iye. Mukuona? Bwanji? Iwo ameneankamukhulupirira Iye, ndipo ankamukonda Iye, ndipoatawona zizindikiro Zake, iwo ankadziwa kuti icho chinalichizindikiro cha Mesiya. Panalibe kupita mozungulira icho. Iwoankachidziwa icho.243 Pamene Nataniele wakaleyo anayenda napita uko.Mwinamwake, pamaso pa Filipo, anati, “Tsopano, inesindikudziwa za izi, Filipo. Ine ndawonapo zinthu zambirizikuwukapo mu masiku otsiriza ano. Ine ndikudziwa palizinthu zambiri zimene zikumachitika.” Koma iye anayendanapita kumeneko pamaso pa Iye. Anati, “Ine ndipita kutindikamvetsere kwa Iye, ndi kukawona zimene ati akanene.”244 Anayenda napita kumeneko, ndipo Yesu anati, “TaonaniMuisraeli mwa yemwemulibe chinyengo.”

Iye anati, “Rabbi, inumunandidziwa ine liti?”245 Iye anati, “Filipo asanakuitane iwe, pamene iwe unali pansipa mtengo, ine ndinakuwona iwe.”246 Zinachita chiani? Madzi anayikhudza mbewuyokonzedweratu ija. O, mai! Pamene Iwo anatero, iye anati,“Mphunzitsi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Inu ndinu Mfumuya Israeli.”

858 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

247 Kodi chinali chiani icho? Mbewu inali ili mmenemo,itakonzeka. Mulungu anaifetsa Iyo mmbuyo umo asanaikidwemaziko a dziko, kuti Iyo idzabweretsepo Kuwala pa nthawi iyoyomwe. Aleluya!248 Awo ndiwo maimidwe anga, apo pomwe, m’bale. Apo ndipamene ine ndikukhulupirira, apo pomwe. Ine ndimalalikiraIzo, ndipo Izo zimagwera apa ndi apo, ndipo iwo amapitambali iyi ndi mbali iyo. Izo sizimapanga kusiyana kulikonse.Kwinakwake, Iwo akayigunda mbewu. Ndipo pamene Iwoatero, [M’bale Branham akhwatchisa chala chake—Mkonzi.]iyo idzaulukira mmwamba kwa Moyo, monga chomwecho,motsimikiza basi monga dzikoli. Inde, bwana.249 Monga, “Mnyamata wakhungu uja,” anati, “izi zinachitidwakuti ntchito za Mulungu zikhoze kuwonetseredwa.” Mukuona?Mukuona? Iye ankadziwa zimene zikanati zichitike. Zedi, Iyeanali. Chabwino.250 Tsopano, okonzedweratu, pamene iwo anawonazizindikiro Zake Zamwamalemba, ankazindikira kuti Mawuankatsimikizira ntchitozo, kapena ntchito zinkatsimikiziraMawuwo, kuti Mawu anali kulondola. Iwo analiatakonzedweratu kuti adzawawone Iwo, ndipo iwo anali mumzeremomwe kuti awawone Iwo, ndipo iwo anawatenga Iwo.

Ndiye iwo anati…Iwo atatha kuwona kuti iwo sakanatiafike kulikonse.251 Chifukwa anthuwo anali okonzedweratu ku MoyoWamuyaya, iwo anali woti awupeza Iwo. Ndizo zonse. “Onseamene Atate anandipatsa Ine adzadza kwa Ine. Ndipo onseamene adza kwa Ine, Ine ndidzawapatsa Moyo Wamuyaya ndipoIne ndidzamuwukitsa iye pa tsiku lotsiriza. Iwo sadzakhalammodzi wa iwo adzataike.” Ameni. Ine ndikugwiritsitsa kumenekwa izo.

“Osati mwa ntchito, osati mwa zochitidwa, osati mwanyonga, osati mwa mphamvu; mwa Mzimu Wanga, ateroMulungu.” Osati zimene ine ndachita, chimene ine ndiri, kapenachimene ine ndidzakhale ndiri; koma chimene Iye ali. Ndipoine ndiri mwa Iye. Ndipo chirichonse chimene Iye ali, ine ndinegawo la Iye. Ameni. Ine ndine wopulumutsidwa chifukwa ndinegawo la Iye. Ndipo, Iye, Iye ndi Mulungu. Ndipo ine ndinegawo la Iye, pokhala mwana Wake. Ndiko kulondola. Kotero sizimene ine ndachita, zomwe ine nditi ndidzachite. Ndi zimeneIyewazichita. Ndicho chodalira changa, apo pomwe. Chabwino.252 Kotero iwo anawona kuti iwo sakanafika nazo paliponse. Inendilumpha pang’ono za Malemba awa apa. Iwo anawona kutiiwo sakanafika nazo paliponse, ndi Iye.

Kotero, inu mukudziwa, chinthu chotsatira chimene iwoankayenera kuti achite, kuti ayesere kuti amuchotse Iye kuntchitoyo, iwo anapita ndipo anakati kwa abale Ake ndi mayi

KUTENGA MBALI NDI YESU 859

Ake, “Inu mukudziwa, iye watopa kwambiri. Inu mukuyenerakuti mumutengere iye ku mbali ina, kwa kanthawi.” Gulu lijala achinyengo! Iwo basi sanali…Chinthu, chimene chinali, iwosankafuna basi kuti apeze, chinthu chimene iwo sankafuna kutiachite. Iwo ankafuna kuti amuchotsepo Iye. Izo sizinali kutiiwo ankaganiza kuti Iye anali atatopa. Iwo ankafuna kuti Iyeadzigwiritse ntchito Yekha mpaka afe. Koma nthawi iliyonse Iyeankapita kwina, zozizwitsa zinkayamba kutsanulirika, Mawu aMulungu ankapita kumeneko.

Ine, kodi ine sindikanakonda kumumva Iye ataimapamenepo tsiku limenelo, pa gombe la nyanja, pamene Iyeankamuitana Simoni Petro, ndi kuti, “Nditsatire Ine!” Kodiine sindikanakonda kukafika pa chipika ndi kukakhala pansiapo, nditasiya maukonde anga, ndipo nditasiya ndodo yangayowedzera,M’bale Crase, ndi kukakhala pansi apo, nditatsamirakumbuyo chipika ndi kumamvetsera kwa Iye akulalikira pameneIye analowa mu ngalawa ija! O, mai, mai! Ine ndikanakondakumumva Iye pamene Iye ananena kuti, “Idzani kwa Ine, inunonse mukuvutikira ndi kulemedwa kwambiri. Ine ndikupatsaniinu mpumulo.” Ameni! Ine ndikanakonda kumumva Iyeakunena zimenezo.253 Iwo anayesera kuwatenga amayi Ake ndi iwo kutiamuchotsepo Iye pa ntchitoyo. Iwo anati, “Chabwino,inu mukudziwa, I—Iye wagwira ntchito mopitiriza. Inendikukhulupirira ndibwino inu mumuchotse Iye pa njirapo.”Mulimonse, chinthucho, nkuti amuchotsepo Iye, ndizo zonsezimene iwo ankazifuna. Inde, bwana.254 Kachiwiri, ochuluka amene ankapita ndi Iye, nkutiakangopeza malo oti amukole Iye. Kodi inu mumadziwazimenezo? [Abale ati, “Ameni.”—Mkonzi.] Anthu ankatsatiraapo limodzi ndi Iye, kuti angopeza malowo. Iwo anamupatsa Iye,tsiku lina, ndalama. Ndipo iwo anati, “Rabbi…”

Iwo asanamupatse Iye ndalamayo, anati, “Rabbi, ife ndiAyuda. Ife tikudziwa InuNdinuMunthuwamkuluwaMulungu.”O, wachinyengo uyo! Mukuona? Eya. “Ife tikudziwa Inu NdinuMunthu wamkulu wa Mulungu. Inde, Bwana, Rabbi.” Iwo analiakuyenda apo limodzi naye Iye. “O, mmawa wabwino, M’bale!O, ife ndife okondwa kwambiri Inu muli cha kuno mu dzikolathuli! O, ife ndife okondwa kwambiri kukuwonani Inu! Ifetiri kwenikweni a Inu, mano ndi zikhadabo zakuphazi, M’bale.Ngati inu muti mukhale ndi chitsitsimutso, ife mwina tikhozakuthandizirana ndi Inu.” Mukuona? Zimene iwo akuyesera kutiachite ndi kumuikira Iye khwekhwe. Mukuona?255 Iwo anati, “Tsopano, ife tikudziwa kuti Inu ndinu Munthuwamkulu wa Mulungu. Inu simuwopa kukondera ndi munthualiyense. Inu simumawopa kanthu koma Mulungu. Ndipo ifetikudziwa kuti Inu ndi wolimba mtima. O, Ndinu opanda

860 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

mantha ndi Uthenga Wanu! Ife tikudziwa kuti Inu NdinuMneneri wamkulu, chifukwa palibe munthu amene angachitemonga chomwecho ndi kusakhala wopandamantha ndi UthengaWakemumasiku ngati ano, kupatula ngati Iye atakhalaMneneriwa Mulungu, wodziwa pamene Iye waima. Kotero, ife tikudziwaInu simumalemekeza munthu, palibe munthu. Rabbi, Inu NdinuMunthu wamkulu. Ndife Ayuda. Ife tiri limodzi ndi Inu, M’bale.Ife zedi tiri.256 “Tsopano, Rabbi, kodi ndi kukhoza kumapereka msonkhokwaKaisara?” O, gulu lija la achinyengo! Nha!

Dikirani. Mzimu Woyera unali ndi Iye. Iye anali MzimuWoyera.Mukuona? Iye anati, “Inumuli nayo ndalama?”

Anati, “O, inde, inde. Eya. Ine ndiri nayo ndalama.”Iperekeni iyi kwa Iye.

Anati, “Ndipatseni Ine iyo.” Anati, “Ndi nkhope ya ndani ilipamenepo iyo?”

Anati, “Kaisara.”

Anati, “Ndiye zimupatsani Kaisara zomwe ziri za Kaisara;Mulungu zimene ziri za Mulungu.”257 Kumuikira Iye msampha, kudzinenera kuti anali abwenziAke. Zinkawoneka ngati panalibe mmodzi amene akanathakumumvetsa Iye. Iwo ankayenda limodzi naye Iye kwa kanthawipang’ono, ndiyeno nkufika poyipidwa ndi Iye, ndi kuchoka. Iwoankanena kuti, “O, chabwino, ife tinkaganiza, ife tinkaganizandithudi.” Ngakhale ophunzira anati, “Ife tinkaganiza ndithudikuti uyu anali Iyeyo amene akanati—aka.” Mpaka, ngakhaleYohane anatumiza, nakamufunsa Iye, “Kodi Inu ndi Iyeyo,kapena kodi ife tiziyembekezera wina?” Mukuona? O, moyowake umene Iye ayenera kuti ankawukhala, mukuona, ndipoakudziwa zimenezo! Koma Iye anali ndi cholinga chimodzi,cholinga chimodzi: kuchita ntchito ya Mulungu. Ambiriankapita limodzi naye Iye, kungoti apezemalo oti amukole Iye.258 Tsopano, ine ndikuyembekeza izo si kusinjirira ngati inenditati izo ziri chimodzimodzi lero. Ambiri amabwera munondi kumatsatiramsonkhano, kungoti awapezemalowo, akuwoneiwe ukumupempherera winawake.259 Kuno, osati kale litali, mlongo winawake amene amapitaku mpingo uwu, anali ku mpingo wina kumene Mulungu analikupangitsa chirichonse kumachitika. Ndipo mlongo uyu anatikwa mlongo winayo, anati, “Inu mukudziwa, mwamuna ujaamene akukhoza kumapempherera odwala” anati, “ayenera kutiali n—ndi moyo wachigonjetso kwambiri.” Ndipo anati, “Iyeayenera kuti ndiwopeza bwino basi, banja lake chirichonse,kumachiritsidwa pa mawu olankhulidwa, monga choncho.”[M’bale Branham akhwatchitsa chala chake—Mkonzi.]

KUTENGA MBALI NDI YESU 861

Ndipo dona winayo zinachitika kuti anali wochokera kuJeffersonville. Ndipo ine ndikutsimikiza kuti palibe aliyenseakanati adziwe, koma zimene Yesu anati, “Pakati pa anthuako omwe,” inu mukudziwa, “dziko lanu.” Ndiko kulondola.Ndi chifukwa chake ine…Izo zikhoza kukhala ziri kuti pakalipano, zikudzamoyandikira, kukhoza kukhala kuli kusintha kwanthawi, inu mukuona.

Ndipo iye anati—iye anati, “Inu mukudziwa chiani?” Anati,“Palibe mmodzi wa ana ake angakhale ndi kuyetsemula, ameneiye samutengera kwa dokotala.” Chinthu chosauka, chotsika,chopepusidwa ngati icho, mukuona, mukuona, mkazi ameneamangofuna kuti aponyere kumbali. Anati, “Pamene ana akeadwala, iye amawatengera iwo kwa dokotala.”260 Aliyense amene ali woganiza bwino akanati azichita chinthuchomwecho. Eya. Anthu samatha kumvetsa kuti mankhwala ndiotumizidwa ndi Mulungu. Bwanji, abale, ngati iwo sali, iwo ndia Mdierekezi. Zedi, iwo ali. Mulungu ali kumene mankhwalasangafikire. Zedi. Mankhwala ndi a Mulungu. “Chabwino,”inu mukuti, “ine ndikudziwa madokotala ambiri amene…” O,inde, ndipo ine ndikuwadziwa alaliki ambiri amene ali mwanjirayomweyo, nawonso. Si mwamuna amene akuwagwira iwo, ndichimene iwo ali. Ine ndikudziwa amuna ambiri amene amagwiraMawu a Mulungu, samakhulupirira mu machiritso Auzimu,samakhulupirira ngakhale mwa Mulungu. Kulondola. Komaiwo amawagwira Iwo, chimodzimodzi basi. Alipo amuna ambirikunja uko ali ndi mankhwala, ndi mong’ambira anthu, ndizinthu, amene amamukana Mulungu ndi china chirichonse,koma alipo ambiri amene amamukhulupirira Iye aponso.Kotero ngati izo zikumawathandiza anthu, izo ndi za Mulungu.Ine sindikusowa kuti…ine sindikusowa kuti ndiyitengegalimoto iyo ndi kuyikwera popita kwathu usikuuno. Inendikhoza kuyenda ngati ine ndikanafuna kutero.KomaMulunguanandipangira ine galimoto, kotero ine ndikumuthokozaMulungu chifukwa cha iyo. Zinthu zonse izi zimachokerakwa Mulungu, koma timazigwiritsa izo ntchito mwanzeru.Musamapite nazo mwamisala izo. Mukuona?261 Chinthu chofanana, kotero, izo, ndi zimenezo, inu mukuona.Basi akungoyesera kuti apeze chinachake, kwa wotembenukawamng’ono uyu, kuti anyazitse dzina lawo, dzina l—la ntchito zaMulungu. Mukuona? Iwo ankafuna kuti alinyazitse ilo. “Nthawiiliyonse pamene mwana amadwala, mmodzi wa ana ake, iyeamawatengera iwo kwa dokotala.”

Zedi, ine ndingatero. Ndiye ngati dokotala sangathe…Ine ndimamufunsa Mulungu kuti athandizire ine ndisanapitekumeneko. Ndiye ngati adokotala sangachite kanthu pa izo,ndiye ine ndimamutengera iye pamwamba pang’ono. U-nhu.Ndiko kulondola. Inde, bwana.

862 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

O, chimodzimodzi basi lero, iwo akuyesera kuti apezemsampha penapake.262 Iye ankawadziwa iwo, koma zindikirani, Iyesanawadzudzule konse iwo. Iye ankapita nawo limodzi. U-nhu. Iye akuchita chinthu chomwecho tsopano. Iye akumapitalimodzi nawo iwo, nkumawasonyeza iwo chifundo Chake, ndikokulondola, ngakhale iwo amachita zonse palimodzi motsutsananaye Iye. Bwanji? Chifukwa Iye amawakonda iwo. Ndipo Iyeankapita limodzi nawo iwo.

Koma iwo nthawizonse amakhala okonzeka kuti aitanirepa Iye zikakhala zadzidzidzi. Iwo amamufuna Iye pamenepo.Iwo amamufuna. Iwo akhoza kumuseka munthu winawake,chifukwa chofuula. Iwo akhoza kumuseka munthu winawakechifukwa cholalikira za machiritso Auzimu, kumati iwosakhulupirira mu zimenezo. Iwo basi sanadwale mokwaniraapabe. Ine ndawamvapo ambiri awo.263 Mkazi, akufa, basi pamene ine ndimathamanga pa masitepe,pamene ine ndinali kulalikira komwe kuno. Ndipo bamboyoanaima apo pomwe pa khomo, akuitana kwa ine. Iye analiatayenda chondidutsa. Iye anali pa msewu kuno, ndipo analindi ng’ombe kumeneko. Ndipo iye anati, “Ngati ng’ombe yangaikanakhala ndi chipembedzo cha mtundu uwo chimene Billyali nacho, ine ndikanaipha ng’ombeyo.” Mwa kuchepera kwatheka la ora kuchokera apo, iye anali atakanthidwa ndipoakutengedwera ku chipatala, mkazi wamng’onowokongola.

Ndipo ine ndinathamangira kumeneko. Mwamuna wakeanali Mkatolika. Ndipo iwo anatumiza wina kwa ine. “Iyeakufa. Ndipo iye anapita…Maso ake anayamba kutupirakunja. Iye anati, ‘Muitaneni iye. Muitaneni iye. Muitaneni iye.Mwamsanga. Msanga.’”264 Ndipo mchimwene wake anathamanga ndipo anakaimapakhomo apo, ndipo anadikirira dikirira, ndipo iye anakhalaakulozera pa ine. Ndipo malowo anali atadzaza basi ndianthu. Ndipo patapita kanthawi, winawake anabwera apondipo anaika cholembedwa p—pa desiki apa. Icho ch—chinati,“Winawake akufa ku chipatala.”

Ndipo ine ndikukhulupirira, M’bale Graham Snelling, inendinati, “Utenge malo anga mpaka ine nditapita.” Ndipo iyeakanati angoima apo ndi kumatsogolera kuimba. Iye analiasanaitanidwe nkomwe, ndipo k—kuti azilalikira, pa nthawiimeneyo. Iye anabwera apo kuti azitsogolera kuimbako.

Ndipo ine ndinapita kunja ndipo ndinalowa mu galimotoyanga, ndipo ndinathamangira kumeneko. Ndipo basi pamenendinafika pamwamba pa masitepe, iye anakoka mpweya wakewotsiriza. Ndipo, ndithudi, matumbo ndi impsyo, chirichonse,zinachita zawo. Ndipo ine ndinathamangira mmenemo, ndipoiwo anali atamuphimba kale nkhope yake, ndi nthunzi ikufuka

KUTENGA MBALI NDI YESU 863

chokweramonga choncho. Ndipo namwinowamkulu uyo ataimapamenepo, iye anati, “M’bale Branham, iye amafuula mumpweya wake wotsiriza kufuna inu.” Kuyesera kuti akonzeizo, koma izo zinali mochedwa pamenepo, inu mukuona. Eya.Aponso…Iwe ukhoza kuchimwa nthawi imodzi mochulukakwambiri, inu mukudziwa.265 Ndipo iye anali ngati…wakuya pa nkhope yake. Iye analindi tsitsi lofiira; mkazi wokongola kwenikweni. Ndipo iye—tsitsilake lodulidwa lonse linali chang’alala. Maso aakulu abulaunianali atatong’olokamo, ndipo anali atangotsekedwa mwatheka.Ndipo makwinya pa nkhope yake anali atafika motero,kupanikizika kotero, mpaka iwo basi…?…kungokhala ngatimabampu aang’ono pali ponse pa nkhope yake, ndipo kamwayake inali yasaa. Ndipo ine ndinayenda nkufika apo ndipondinayang’ana pa iye.

Ndipo apo mwamuna wake ataima pamenepo, ndipo anati,“Billy, izi ndi zomwe zinali.” Anati, “Ine ndine wa Chikatolika.Ine ndikufuna kuti iwe umunenere iye pemphero, chifukwa iyewapita ku purigatorio.”

Ine ndinati, “Chiani?”266 Anati, “Nenerani pemphero pa iye.” Anati, “Iye wapita kupurigatorio. Iye anadutsa pa tchalitchi chanu pafupi maoraawiri apitawo, ndipo anati, ‘Ngati ng’ombe yathu ikanakhalakonse ndi mtundu wa chipembedzo chanucho, iye akanaiphang’ombeyo.’”Mukuona? Anati, “Nenerani pemphero pa iye.”267 Ine ndinati, “Izo ziri mochedwa kwambiri. Iye akanatiatsuke moyo wake kuno, osati mpaka iye atakafikakwinakwakenso.”Mukuona? Ndiko kulondola. O, inde.

Koma ife nthawizonse timamufuna Iye mu nthawiya kupsyinjika. Anthu, ine ndawamvapo iwo akuti, “Inesindimakhulupirira mwa Mulungu.” Musiyeni iye adzivulazeyekha moipa kwambiri, kamodzi, muwone Mmodzi woyambayemwe iye ati amuitane.268 Ngakhale ophunzira Ake, nthawi ina pamene iwo analimu mkuntho. Ngakhale, pamene iwo anamuwona Iye, iwoankachita mantha pang’ono ndi Iye. Iwo sanali kudziwandendende basi chimene Izo zinali. Iwo anati, “Ndi mzimu.”Ndipo iwo anafuula apo. Koma, apobe, ziyembekezo zonsezoti angapulumutsidwe zinali zitapita, kotero iwo anamuitaniraIye umo. Eya. Apo, nthawizonse, ngakhale inu mukukaikirapang’ono kapena ayi. Pamene ziyembekezo zonse zitatha, inumumakonda kumuitanira Iye umo. Eya. Iwo anamutengera Iyeumo, chifukwa iwo anali ndi chosowa cha Iye. Ndiko kulondola.269 Inu mukudziwa, ine mowirikiza ndakhala ndikudabwa,nthawi zina, mwinamwake ndi chifukwa chake mikunthoimabwerapo. Kodi inu munayamba mwaganiza za zimenezo?Iye anakhala pamenepo ndi kumawayang’ana iwo mpaka

864 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

iwo atakhala ndi kusowa kwa Iye, ndiyeno Iye anabwerapowonekera. Kotero, ife tikhoza kuwona kusowa kwathu kwaIye tsopano. Ife tikuwona kuti nkuntho ukubwera, abale. Tiyenititengembali ndi Iye usikuuno. Titengembali ndiMawuAke.

I—i—ine ndisiyira apa.270 Tiyeni titenge mbali ndi Iye. Tiyeni ife, inu ndi ine,abale, tilumikizane naye Iye, usikuuno. Mkuntho ukubwera.Ndipo musati mudikire mpaka bwato laling’onolo limire. Tiyenitimutengere Iye pa kakhungwa kathu kakang’onoko tsopano.

Inu mukhoza kuyang’ana kumbali ndi kuti, “Ine sindikuthakuzimvetsa zinthu zonse izi, M’bale Branham.”271 Tiziwona ngati ife tingamanene chirichonse kupatulazimene ziri mu Mawu. Tiwone ngati pali chirichonse pamenepokupatula zimene Iye analonjeza kuti azichita. Izo zikhozakuwoneka mwauchipukwani pang’ono kwa inu, nthawizina. Inumkuganiza, “O, mai. Ine sindikutha kumvetsa Zimenezo.” Komalidzakhalapo tsiku pamene moyo wanu uno uli nkuchoka. I—iwosiwudzawoneka woipa kwambiri kwa inu pamenepo. Pameneinu mukudziwa, inueni, inu mukuyenera kuti mutembenukirekwa Mulungu amene anakulengani inu, inu mudzafunakudzamutengera Iye mkati pamenepo. Tiyeni timutengere Iyemkati tsopano, mkuntho usanafike mwa kuipira kwina kuposachimene iwo uli.272 Ine ndikumufuna Iye alowe mu mtima mwanga. Inendikumufuna Iye mochuluka kwambiri mu moyo wanga,mpaka umunthu wanga wonse usasawire; kuti malingaliroanga, zoganiza zanga, chirichonse changa chimene ine ndiri,chizilamuliridwa ndi kuwongoleredwa ndi Khristu Yesu.Ine ndikufuna kuti ndikhale nditataika kwambiri, kw—kwainemwini, kuti zonse zimene ine ndizidziwa ndi kuziwona ndizoYesu Khristu.

Ndipo ine ndikufuna kuti ndizibwera pamaso pa inu nonse,ngati Mulungu wa Kumwamba aloleza inu kuti mukhalenazo zinthu izi zimene ine ndimazikambazi. Pamene inendizibwera pakati pa inu, ine ndikufuna ndizimudziwa Khristu,Iye wopachikidwayo. I—ine ndikufuna ndizidziwa ulemererondi matamando ofunika a Mulungu. Kukhala pansi pakatipa inu, ndi kumamumva mtumiki mmodzi ataimirira ndikumapereka matamando kwaMulungu, pa zomwe iye waziwonazikuchitidwa mu mpingo wake. Wina, zimene iye waziwonazikuchitika mu mpingo wake. Mmodzi wina, zomwe iyewaziwona zikuchitika mumpingo wake.273 Izo ndi ndendende zimene iwo ankachita. Ndipo pameneiwo ankabwera palimodzi nakomana mu chiyanjano, muMachitidwe 4, iwo anali kupereka ndondomeko ya zimeneMulungu anazichita kuno, ndi zimene Mulungu anali atachitakuno. Ndipo Petro ndi Yohane anali atakwapulidwa. N—n—

KUTENGA MBALI NDI YESU 865

ndipo anapanga lonjezo kuti ngati iwo atero…zimene iwoakanati achite kwa iwo ngati iwo akanati azilalikiranso muDzina la Yesu. Ndipo iwo anasonkhana limodzi anthu awo,ndipo iwo onse ankapemphera mwa mtima umodzi, ndipoanapemphera mwa chifuniro cha Mulungu, ndipo ankabwerezaLemba, “Nchifukwa chiani achikunja akuchita ukali ndianthu kulingalira chinthu chachabe?” Ndipo pamene iwoanapemphera, Mzimu Woyera unagwedeza pa malopo pameneiwo anali atasonkhana palimodzi.274 Uwo ndi mtundu wa kusonkhana kumene ife tikukusowa.Icho ndi chimene ife tikuyenera kukhala nacho, abale. Tiyenitikhale oyikiridwa linga ndi Mawu a Mulungu, mwa Mzimu waMulungu, mwa mphamvu ya Mulungu. Ndipo tiyeni Kuwalakwathu kuwale kwambiri tsopano, kuti ife tikhale mongaStefano.275 Iye anaima pamenepo, munthu mmodzi, yekha, pamasopa bungwe la Sanhedrin lija la anthu theka la milioni,mwinamwake, ataima pamenepo. Aliyense wa iwo akulozetsachala chawo momutsutsa pa nkhope yake. Pamene munthuwamng’ono uyo ankayenda kupita kumeneko, anati, “Iyeankawala ngati mngelo.” Ine sindikutanthauza, mwinamwake,kuwala kuli pa nkhope yake, monga choncho. Mngelo samasowakuti akhale ndi kuwala pa iye. Koma mngelo ndi mwamunakapena…Mngelo ndi mtumiki, mtumiki amene amadziwachimene iye akuchiyankhula.

Anayenda napita kumeneko ndipo anati, “Amuna, ndiabale, ndi makolo, makolo athu ku Mesopotamia, momweiwo anatulutsidwirako, ndi Abrahamu,” ndi ena otero, ndipompaka Kwakuti-n-kwakuti. Ndiyeno iye anafika mpaka pamalo owononga, anati, “O, inu a makosi owuma, osadulidwamu mtima ndi makutu, chifukwa chiani inu nthawizonsemumawukanizaMzimuWoyera?Mongamakolo anu ankachitira,inunso mukutero.” Iye ankadziwa ndendende pamene iye analiataimapo. Icho ndi chifukwa chake iye anali kuwala. Iyesanali kuwopa mpang’ono. Iye ankadziwa mwa Yemwe iyeankakhulupirira.276 Ngakhale pamene imfa inkagogoda pa chitseko chamtima wa Paulo Woyera. [M’bale Branham agogoda paguwa—Mkonzi.] Ndipo iye anati, “Ine ndikudziwa mwa Yemweine ndamukhulupirira, ndipo ine ndikukakamizika kuti Iyendi wokhoza kusunga icho chimene ine ndachipereka kwa Iyemotsutsana ndi tsikuli.” Ameni.277 Ambuye akudalitseni inu, abale. Ine ndikupepesa inendakusungani inu pano mpaka maminiti twente faifi kutiikwane leveni koloko. Ine ndikudziwa ichi si chachizolowezikwa inu. Ine ndikupepesa kuti ndachita zimenezo. Koma inumwakhala muli abwino kwenikweni usikuuno; palibe wa inu

866 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

anachoka. Inu munakhala ndipo mumapereka chidwi chanuchosagawanika.

Ndipo ine ndikudalira ndi kuyembekeza kuti,mwakuyankhula kwanga kwakung’ono, koduka duka,kwamanjenje, kuti Mulungu, Mzimu Woyera, penapakewatsanulira apo Mbewu yaing’ono mu mtima wanu, kutimphamvu ya Mulungu iyikhudza ndi kuibweretsa Iyo ku Moyo,basi monga mkazi pa chitsime, ndi ena omwe anakonzedweratukuMoyoWamuyaya. Mulungu akudalitseni inu.278 M’bale Neville, inu mukuti mutibalalitse, kapena kodi inumukufuna muchite chiani? Inu muchita motani? Basi mu…[M’bale Neville ati, “Ine ndingopemphera.”—Mkonzi.]

Kodi inu mukumkonda Iye? [Osonkhana ati,“Ameni.”—Mkonzi.] Kodi inu muzimutumikira Iye? [“Ameni.”]Kodi inumuzimukhulupirira Iye? [“Ameni.”] Ameni.

Mukumukonda Iye? Ameni.Mumutumikira Iye? Ameni.Mumkhulupirira Iye? Ameni.Ameni, Ameni.Tikufuna tiyiimbe iyo. Ameni.Ameni. Ameni. Ameni. Ameni.Baibulo ndi loona, Ameni.Ndilikhulupirira. Ameni.Ndi Mawu a Mulungu. Ameni.Ameni. Ameni.

Tiyeni ife tiime.Ameni. Ameni. Ameni. Ameni. Ameni.Ambuye, tikukukondani. Ameni.Ameni. Ameni. Ameni. Ameni.Tikukhulupirira mukubwera. Ameni.Takonzeka tikomane Nanu. Ameni.Bwerani, Ambuye Yesu. Ameni.Ameni. Ameni.

Ife tikupemphera Mulungu kuti mutilole ife tizikhalamwakukhoza kwathu nthawi zonse, kuti tizimtumikira Iye.

Ameni. Ameni. Ameni. Ameni. Ameni.Ine ndikudalira kuti Iye akudalitsani inu, ndi kukusungani

inu, ndi kukusamalirani inu, ndi kuyang’anira pakati pa ife, ndikukudzozani inu kuti mulowe mu Ufumu Wake, kuti muzichitantchito zazikulu, ndi kuti andithandize ine mu ntchitoyi mpakapamene ife tidzakomananso.

Ameni. Ameni. Ameni. Ameni. Ameni.Ine ndikupemphererani. Inumuzindipempherera?

Ameni. Ameni. Ameni. Ameni. Ameni.

KUTENGA MBALI NDI YESU 867

279 Atate athu, ife tasonkhana usikuuno mu Dzina la AmbuyeYesu wolemekezeka, Dzina lokondedwa ndi lachikondilija limene ife tonse timalikonda ndi kulipembedza. Inendikulingalira momwe magulu a anthu kudutsa mu zakazi,kwa zaka makumi atatu kapena kupitirira, ife timasonkhanamu nyumba yaing’ono yakale ino. Momwe ife timakhalatitazungulira mbaula ndi mapazi athu akuzizidwa, pafupifupi,ndi kukhala pamenepo ndi mapazi athu pamwamba pa mbaula,ndi kumayankhula za Ambuye Yesu.

Ine ndikulingalira za mapazi ena ofunikira amene nthawiina anayendapo pa dziko lapansi, amene anakhala ndimapazi amenewo apo. Ine ndikuganiza za M’bale Sewardwachikulire, M’bale Sparks, M’bale George DeArk, miyoyoina yambiri yofunikira imene nthawi ina inakhala ndimapazi awo moyang’anizana ndi mbaula, inapita kalekukakomana ndi Ambuye wawo usikuuno, akupuma kutsidyakomu manda, kuyembekezera kuitanidwa kwakukulu kujakuchokera Mmwamba. Iwo anamenya nkhondo. Iwo anasungaChikhulupiriro. Iwo atsirizitsa ulendowo. Ndipo tsopano iwoakuyembekezera korona wa chilungamo, Ambuye Woweruzawolungama, ati adzawapatse iwo tsiku limenelo.280 Atate, Mulungu, ife tinapemphera pamene tinkadalitsatchalitchi chaching’ono chino pa ngodyapa, ndipo ndinati,“Ambuye Yesu, mulole icho chiime ndipo anthu adzakhale alimmenemo pamene Inu mudzang’amba mlengalenga, kubwerakwachinsinsi kuja, kupita mwamsanga kwa Mpingo. Mulungu,ine ndikupemphera kuti miyoyo imene yabwera ku guwa ili,miyoyo imene yakutumikirani Inu, Mbewu ya Uthenga imeneyafesedwa mmbuyo ndi mtsogolo, ndi mmbuyo ndi mtsogolo,ndi mmbuyo ndi mtsogolo, kudutsa apa, kwa zaka sate, chimeneife tikukhulupirira kuti ambiri a anthu ofunika awo adzakhalaali kumeneko Tsiku limenelo, chifukwa cha kuyesetsa kofookauku kumene ife takuika, kuti tibweretse Mawu kwa Moyowokonzedweratu uwo. Ife tikukuthokozani Inu chifukwa chaizo. Ndipo tikudalira, Mulungu, usikuuno, kuti pasakhalemmodzi amene alipo tsopano koma amene ati adzakhale alipo paTsiku limenelo, ataphimbidwa ndi Magazi, atazikika mwa Yesu.Perekani izi, Atate. Ife tikudalira mwa Iye.281 Tsopano ife ndife oti tikomananso muno Lamlungu mmawa,ambiri a ife. Ndipo ife tikupemphera, Mulungu, kuti Inumudzakomane nafe ndipo mudzatinyemere Mkate wa Moyokwa ife.

Mulungu, ife tikumukumbukira M’bale Ruddell ndi maloake kumtunda uko, kumene iwo amene akuyenda mnjirayi ndiiye. Khalani ndi mnyamata wofunika ameneyo, Ambuye, inendikupemphera. Pamene ine ndikumuwona iye akubwerapo,kuwawona anyamata aang’ono awa, ine ndikumverera ngatiiwo ndi a Timoteo anga. Ine ndikupemphera, Atate, kuti Inu

868 KHALIDWE DONGOSOLO NDI CHIPHUNZITSO CHA MPINGO

mumudalitse M’bale Ruddell ndi utumiki wake. MudalitseniM’bale Junie Jackson. O Mulungu, ife tikupemphera kutimadalitso Anu akhale pa iye, akhale pa M’bale wathu Crase,akhale pa M’bale Snelling, akhale pa m’bale wina uyu ukoamene akutenga malo ake, ndi M’bale Beeler, ndi M’bale,abale onse awa kuno, Ambuye, ndi M’bale Neville, ndi aliyensewa ife, Ambuye. Ife tikungopemphera kuti madalitso Anuamwetuliridwire pa ife, kuti chisomo Chanu chikhale zonsezimene ife tikuzisowa, Ambuye, kuti tizipitirira nazo.

Ndipo mulole ife tisaiwale konse ndemanga yaing’ono,usikuuno. Ngakhale monga mkazi wamng’ono uja ataimaapo, asakudziwa chomwe mathero akanati akhale; koma Yesuankasowa tcheru, ndipo iye amapereka icho kwa Iye, inde,kusambitsa mapazi Ake. Chinachake chosasamalidwa chimenengakhale iwo amene ankadzinenera kuti anali antchito Akeanalephera kuti achite icho, ndipo iwo anali akuyesera kutiazimutonza Iye. Koma mkaziyo anamuchitira Iye ntchito, asalikuyembekezera mphotho, ndipo apo sipakanakhala chachikuluchikanapatsidwa.282 Mulungu, mulole ife tichite mofanana, tizingokankhirapatsogolo pomwe ndi kumachita ntchito ya Mulungu. Ndipozonse zimene ife tikukhumba kuti tichite, Ambuye, ndi kutitidzamve, pa Tsiku limenelo, “Wachita bwino, wantchito Wangawabwino ndi wokhulupirika. Lowa mu zisangalalo za Ambuyezimene zinakonzedwera kwa iwe chikhazikitsireni maziko adziko.” Mulungu, tipatseni ife kuti tizichita izo ndi kusungachiyanjano wina ndi mzake. Ndipo mulole Mzimu Woyeraukhale ndi ife ndipo uzititsogolera ife ndi kutilondolera ife muzonse zimene ife tikuchita. Ndipo tipatseni ife moyo wautali,mwinamwake, ngati nkotheka, tidzawone Kudza kwa AmbuyeYesu. Ife tikupempha izi muDzina Lake. Ameni.

Chodala ndi chimangoMu chikondi cha Chikhristu;Chiyanjano cha apaubaleNchonga chija Kumwamba.Pamene ife tisiyana,Zitipatsa kupweteka mkati;Tidzalumikizanabe mu mtima,Kuyembekeza kudzakomananso.

283 Baibulo linati, “Iwo anaimba nyimbo ndipo anapita panja.”Mulungu akudalitseni inu tsopano, mpaka ine ndidzakuonanikachiwiri, Lamlungu mmawa, Ambuye akalola. Ndapita-ndapita.284 Jim, ine sindinagwedeze dzanja lako, usikuuno. Mulunguakudalitseni inu. Ambuye akudalitseni inu.

Khalidwe Dongosolo ndi Chiphunzitso cha Mpingo, Bukhu Lachiwiri(Conduct, Order And Doctrine Of The Church, Volume Two)

Mauthenga awa a M’bale William Marrion Branham olalikidwa ku BranhamTabernacle mu Jeffersonville, Indiana, U.S.A., anatengedwa kuchokera pamatepi ojambulidwa ndi maginito ndipo anadindidwa mosachotsera mawuena mu Chingelezi. Ndipo kumasulira kwa Chichewa uku kunadindidwa ndikugawidwa ndi Voice of God Recordings.

CHICHEWA

©2009 VGR, ALL RIGHTS RESERVED

VOICE OF GOD RECORDINGS, MALAWI OFFICE

P.O. BOX 51453, LIMBE, MALAWI

VOICE OF GOD RECORDINGS

P.O. BOX 950, JEFFERSONVILLE, INDIANA 47131 U.S.A.www.branham.org

Chidziwitso kwa ofuna kusindikiza

Maufulu onse ndi osungidwa. Bukhu ili mukhoza ku printa kunyumba kwanu ngati mutafuna kuti mugwiritse ntchito inuyo kapena kuti mukawapatse ena, ulere, ngati chida chofalitsira Uthenga wa Yesu Khristu. Bukhu ili simungathe kuligulitsa, kulichulukitsa kuti akhalepo ambiri, kuikidwa pa intaneti, kukaliika pakuti ena azitengapo, kumasuliridwa mu zinenero zina, kapena kugwiritsidwa ntchito ngati njira yopezera ndalama popanda chilolezo chochita kulembedwa ndi a Voice Of God Recordings®.

Ngati mukufuna kuti mumve zambiri kapena ngati mukufuna zipangizo zina zimene tiri nazo, chonde mulembere ku:

Voice of God RecoRdinGsP.o. Box 950, JeffeRsonVille, indiana 47131 U.s.a.

www.branham.org