na. 4, 2016 34567download-a.akamaihd.net/files/media_magazines/55/wp_cn...of south africa npc, 1...

16
34567 Na. 4, 2016 BAIBULO BUKU LOMWE LINAPULUMUKA M’ZAMBIRI

Upload: vanphuc

Post on 22-Mar-2018

418 views

Category:

Documents


6 download

TRANSCRIPT

34567Na. 4, 2016

BAIBULOBUKU LOMWELINAPULUMUKAM’ZAMBIRI

The Watchtower (ISSN 0043-1087) Issue 10July 2016 is published monthly with an additionalissue published in January, March, May, July,September, and November by Watchtower Bibleand Tract Society of New York, Inc.; L. Weaver, Jr.,President; G. F. Simonis, Secretary-Treasurer;1000 Red Mills Road, Wallkill, NY 12589-3299,and printed by Watch Tower Bible and Tract Societyof South Africa NPC, 1 Robert Broom Drive East,Rangeview, Krugersdorp, 1739. � 2016 Watch TowerBible and Tract Society of Pennsylvania. Printed inSouth Africa.

34567Vol. 137, Na. 10 CHICHEWA

Makope 58,987,000 a MagaziniyiAsindikizidwa M’ZINENERO 267 Na. 4, 2016���������������������������������������������������������������������������������������������������������������

MAGAZINI ya Nsanja ya Olonda ima-lemekeza Yehova Mulungu, yemwe ndiWolamulira wa chilengedwe chonse.Imalimbikitsa anthu ndi uthenga wabwi-no wakuti Ufumu wa Mulungu posache-dwapa uchotsa zoipa zonse n’kusinthadziko lapansili kukhala paradaiso. Imali-mbikitsa anthu kukhulupirira Yesu Khri-stu yemwe anatifera kuti tipeze moyowosatha ndipo panopo akulamulira mo-nga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ma-gaziniyi yakhala ikufalitsidwa kuyambiramu 1879 ndipo si yandale. Mfundo zakezimachokera m’Baibulo.

Magaziniyi sitigulitsa. Timaiperekangati njira imodzi yophunzitsira anthuBaibulo padziko lonse ndipo ndalamazoyendetsera ntchitoyi ndi zimeneanthu amapereka mwa kufuna kwawo.Ngati mukufuna kupereka ndalama zo-thandizira pa ntchito yolalikira pitanipa www.jw.org.

Malemba onse m’magaziniyi akuchokera mu Ba-ibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika,kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina.

Kodi mukufuna kudziwa zambiri ka-pena kuphunzira Baibulo kwaulere?Pitani pa www.jw.org/ny kapena tu-mizani pempho lanu pogwiritsantchito adiresi yoyenera pa maadi-resi omwe ali m’munsiwa.

KODI MUKUGANIZA BWANJI?Ngati Baibulo si buku lochokera kwaMulungu, kodi likanapulumuka m’zinthuzonsezi?Baibulo limanena kuti: “Udzuwobiriwirawo wauma. Maluwawo afota.Koma mawu a Mulungu wathu adzakhalampaka kalekale.”—Yesaya 40:8.Nkhanizi zikufotokoza mfundo zochititsachidwi zokhudza mmene Baibulolinapulumukira m’zinthu zosiyanasiyana.

Kodi Mukudziwa? 9

Kodi Zachiwawa Zidzatha Padzikoli? 10Baibulo Limasintha AnthuNdinasintha Khalidwe Langa Movutikira Kwambiri 12

Kodi Mungayerekezere Zimene Mumakhulupirira ndi ZimeneBaibulo Limaphunzitsa? 14

Kodi Baibulo Limanena Zotani? 16

�������������������������������������������������������������������������������������������������������������������������

M’MAGAZINIYI MULINSO NKHANI IZI

Baibulo—Buku Lomwe LinapulumukaM’zambiriKodi Kudziwa Mmene Baibulo LinapulumukiraN’kothandiza? 3Baibulo Linasungidwa Bwino Kuti Lisawole 4Baibulo Linapulumuka Ngakhale Kuti Ena Sankalifuna 5Baibulo Linapulumuka Ngakhale Kuti Ena AnkafunaKusintha Uthenga Wake 6N’chifukwa Chiyani Baibulo Linapulumuka? 8

s MUNGAWERENGENSO NKHANI ZINAPAWEBUSAITI YATHU

MUNGAPEZE YANKHO LAM’BAIBULO LA FUNSO ILI

Kodi Baibulo NdiLochokera kwa Mulungu?(Pitani pamene palembedwa kuti, ZIMENEBAIBULO LIMAPHUNZITSA ˛ KUYANKHAMAFUNSO A M’BAIBULO)r

Na. 4, 2016 3

Palibe buku lina lililonse la chipembedzo lomwe linga-pose Baibulo, chifukwa lakhala likuthandiza anthu kutiazikhulupirira zinthu zolondola. Komanso ndi buku lo-khalo limene anthu alifufuza kwambiri ndiponso kuli-pezera zifukwa.

Akatswiri ena amakaikira ngati uthenga wa m’Maba-ibulo a masiku ano ulidi wofanana ndi womwe una-li m’mipukutu yoyambirira. Mwachitsanzo, pulofesawina wamaphunziro azachipembedzo ananena kuti:“Sitinganene motsimikiza kuti tinakoperadi uthengawa m’Baibulo molondola chifukwa Mabaibulo ambiriali ndi zinthu zolakwika zokhazokha. Komanso anale-mbedwa patadutsa zaka zambiri kuchokera pamenemipukutu yoyambirira inalembedwa, choncho uthengawake ndi wosiyana kwambiri ndi womwe unali m’mipu-kutuyi.”Anthu enanso amakhulupirira kuti uthengawam’Ba-

ibulo unasinthidwa chifukwa ndi zomwe anaphunzitsi-dwa kuzipembedzo zawo. Mwachitsanzo Faizal, ana-uzidwa ndi anthu a m’banja lake omwe si Akhristu,kuti Baibulo ndi buku lopatulika koma linasinthidwa.Iye anati: “Chifukwa cha zimenezi, anthu akamandifo-tokozera zokhudza Baibulo ndinkakayikira kwambiriuthenga wake. Ndinkaona kuti si lolondola chifukwa li-nasinthidwa.”Kodi kudziwa ngati Baibulo linasinthidwa kapena ayi

kuli ndi phindu lililonse? Kuti mupeze yankho la funso-li, taganizirani mafunso awa: Kodi zikanakhala kuti zi-nthu zabwino zimene Baibulo limalonjeza sizinalembe-dwe m’mipukutu yoyambirira, mukanazikhulupirira?(Aroma 15:4) Zikanakhala kutimfundo zonse zam’Ma-baibulo a masiku ano ndi zolakwika, kodi mukanazi-gwiritsa ntchito posankha zochita pa nkhani zokhudzantchito, banja kapena kupembedza Mulungu?Ngakhale kuti mipukutu yoyambirira ya Baibulo si-

kupezeka, pali zolemba zina zakale komansomipukutuina yambiri ya Baibulo imene imatithandiza. Kodi zina-theka bwanji kuti mipukutuyi izipezekabe masiku ano?Funsoli ndi lofunika chifukwa anthu ena ankafuna ku-ithetseratu, kusintha uthenga wake komanso ikanathakuwola. Kodi kupezeka kwa mipukutuyi kungakutha-ndizeni bwanji kukhulupirira kuti uthengawam’Baibu-lo ndi wolondola? Kuti mudziwe mayankho a mafu-nsowa, werengani nkhani zokhudza mmene Baibulolinapulumukira ku zinthu zonsezi.

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Kudziwa Mmene BaibuloLinapulumukira N’kothandiza?

VUTO LIMENE LINALIPO: Anthu omwe ankalembakomanso kukopera mipukutu ya Baibulo ankagwiri-tsa ntchito gumbwa komanso zikopa. (2 Timoteyo4:13) Komatu zimenezi zikanachititsa kuti mipukutu-yi iwonongeke mosavuta. N’chifukwa chiyani tiku-tero?Gumbwa amang’ambika, kusuluka komanso kutha

mosavuta. Richard Parkinson ndi Stephen Quirke,anaphunzira zinthu zosiyanasiyana za ku Egypt ndi-po anati: “Gumbwa akhoza kuwola n’kutsala ulu-si kapenanso fumbi lokhalokha. Mpukutu ukakhalanthawi yaitali umachita nkhungu kapenanso kuwolachifukwa cha chinyezi ndipo akaukwirira umadye-dwa ndi chiswe.” Komanso mipukutu ina ya gumbwaitapezeka, sinasungidwe bwino ndipo inawonongekachifukwa cha chinyezi komanso kuwala.Mipukutu ya chikopa imakhala yolimba kusiya-

na ndi ya gumbwa. Koma nayonso imawonongekaikasungidwa pamalo otentha, achinyezi kapenansoowala kwambiri.�Mipukutuyi imadyedwanso ndi tizi-lombo. Buku lina linanena kuti: “Kawirikawiri mi-pukutu yakale siikhalitsa.” (Everyday Writing in the

�Mwachitsanzo, chikalata cholengeza kuti dziko la United Statesndi lodziimira palokha (U.S. Declaration of Independence), chinale-mbedwa pachikopa. Panopa padutsa zaka zosapitirira 250 kuchoke-ra nthawi yomwe chikalatachi chinalembedwa, koma zilembo zakezimavuta kuwerenga chifukwa zinafufutika.

Graeco-Roman East) Choncho zikanakhala kuti mipu-kutu ya Baibulo inawola, uthenga wake ukanathera-nso pomwepo.

ZIMENE ZINATHANDIZA KUTI BAIBULO LISUNGIKE:Lamulo lachiyuda linkalimbikitsa mfumu iliyonsekuti izikopera “buku lakelake la chilamulo” lomwendi mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo. (Deuterono-mo 17:18) Komanso pofika chakumapeto kwa nthawiya atumwi n’kuti akatswiri okopera malemba atako-pera mipukutu yambiri. Zimenezi zinathandiza kutimalemba azipezeka m’masunagoge a ku Isiraeli nga-khalenso kumadera akutali monga ku Makedoniya.(Luka 4:16, 17; Machitidwe 17:11) Komano zinathekabwanji kuti mipukutuyi isungidwe mpaka pano?Katswiri wina wa Chipangano Chatsopano dzina

lake PhilipW. Comfort ananena kuti: “Ayuda ankako-nda kusunga mipukutu m’mitsuko n’cholinga chotiisawonongeke.” Ndipo zikuoneka kuti Akhristu na-wonso ankachita zomwezo chifukwa mipukutu inayoyambirira ya Baibulo inapezeka m’mitsuko, m’zipi-nda zamdima ndi m’mapanga a m’madera otenthakwambiri.

ZOTSATIRA ZAKE: Mipukutu yambiri ya Baibulo ida-kalipo ndipo yakhalapo kwa zaka zoposa 2,000. Ku-nena zoona palibenso mipukutu ya mabuku ena aka-le yomwe yakhalapo kwa nthawi yaitali chonchi.

Baibulo Linasungidwa BwinoKuti Lisawole

Mipukutu ya ku NyanjaYakufa inasungidwa kwazaka zambiri m’mitsukoyomwe inaikidwam’mapanga, m’maderaoumaPh

otog

raph

take

nby

courtesy

oftheBr

itish

Mus

eum

Shrine of the Book, Photo � The Israel Museum, Jerusalem

Na. 4, 2016 5

VUTO LIMENE LINALIPO: Atsogoleri ambiri andale ko-manso azipembedzo sankafuna kuti anthu adziwe uthe-nga wa m’Baibulo. Choncho iwo ankagwiritsa ntchitoudindo wawo poletsa anthu kumasulira, kusindikiza nga-khalenso kukhala ndi Baibulo. Tiyeni tione zitsanzo zi-wiri:

˙ Cha m’ma 167 B.C.E.: Mfumu Antiyokasi Epifanasiyemwe ankafuna kukakamiza Ayuda kuti azitsatira chi-pembedzo chachigiriki, analamula kuti Malemba onseAchiheberi awonongedwe. Wolemba mbiri wina dzinalake Heinrich Graetz, ananena kuti nduna za mfumuyi“zikapezamipukutu ya Chilamulo, zinkaing’amba ndipo-nso kuitentha nthawi yomweyo. Komanso zinkapha ali-yense amene wapezeka akuwerenga Baibulo pofuna kuli-mbikitsidwa ndiponso kutonthozedwa.”

˙ Zaka za m’ma 500 mpaka 1500: Atsogoleri ena achi-katolika ankakhumudwa chifukwa choti anthu a m’chi-pembedzochi ankalimbikitsa ena kutsatira mfundoza m’Baibulo m’malo mwa zikhulupiriro zachikatoli-ka. Iwo ankafuna kuti anthu aziwerenga buku la Ma-salimo la m’Chilatini basi. Ndipo anthu wamba omweanali ndi mabuku ena a m’Baibulo, ankawanena kutindi ampatuko. Pamsonkhano wina wa tchalitchichi ana-sankha anthu oti “azifufuza mwakhama anthu ampa-tuko . . . m’nyumba ndiponso m’zipinda zonse zapa-nsi, zomwe ankazikayikira kuti akusungirako mabukua m’Baibulo. . . . Ndipo nyumba iliyonse yomwe apezakowampatuko, aziigwetsa.”

Anthuwa akanakwanitsadi kuwononga Baibulo, ndiyekuti uthenga wake ukanatheranso pomwepo.

ZIMENE ZINATHANDIZA KUTI BAIBULO LISUNGIKE:Ngakhale kuti Mfumu Antiyokasi inkafuna kuti Baibulolisapezekenso ku Isiraeli, Ayuda ambiri anali atasamuki-ra m’mayiko osiyanasiyana. Ndipotu akatswiri amanenakuti pomwe inkafika nthawi ya Yesu, n’kuti Ayuda opo-sa 60 pa 100 alionse akukhala m’madera a kunja kwa dzi-ko la Isiraeli. Ayudawa ankasunga mipukutu ya Malembam’masunagoge awo ndipo ndi yomwenso anthu ena ku-phatikizapo Akhristu, ankaigwiritsa ntchito.—Machiti-dwe 15:21.

M’zaka za m’ma 500 mpaka 1500, anthu ena analimbamtima n’kulolera kuzunzidwa ndipo anapitiriza kumasu-

lira ndi kukopera Baibulo pamanja. Zikuoneka kuti pofi-ka cha m’ma 1400, mabuku ena a m’Baibulo ankapeze-ka m’zinenero pafupifupi 33, ngakhale kuti pa nthawiyikunalibe makina osindikizira mabuku. Patapita nthawi,anthu anayamba kumasulira komanso kusindikiza Maba-ibulo m’zinenero zinanso zambiri.

ZOTSATIRA ZAKE: M’nkhaniyi taona kuti atsogoleriena andale komanso azipembedzo ankafuna kuwonongaBaibulo, koma sizinatheke. Baibulo lamasuliridwa koma-nso kufalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse. La-thandizanso mayiko ambiri pa nkhani zokhudza mala-mulo ndi zinenero. Komanso lathandiza anthu ambirikusiya makhalidwe oipa.

Baibulo Linapulumuka NgakhaleKuti Ena Sankalifuna

Baibulo lachingelezi lomasuliridwandi William Tyndale, linapulumukangakhale kuti pa nthawiyi Mabaibuloena analetsedwa komanso kuwotchedwa.William anaphedwa mu 1536.

6 NSANJA YA OLONDA

VUTO LIMENE LINALIPO:M’nkhani zapitazi taona kutiBaibulo linasungidwa bwino ngakhale kuti likanawo-la komanso panali anthu omwe sankalifuna. Komabepali anthu ena omwe ankafuna kusintha uthenga wake.Nthawi zina m’malo mophunzitsa mfundo za m’Baibu-lo, iwo ankasintha uthenga wake kuti ugwirizane ndi zi-phunzitso zawo. Taonani zitsanzo izi:

˙ Malo olambirira: M’zaka za pakati pa 300 ndi100 B.C.E., Asamariya ena omwe anamasulira Pentatu-keWachisamariya (mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo),anawonjezera mawu patsogolo pa Ekisodo 20:17 akuti:“Ku Gerizimu mudzamangako kachisi.” Iwo ankafunakuti Malemba azigwirizana ndi zimene ankafuna zotiadzamange kachisi m’phiri la “Aargaareezem,” kapenakuti Gerizimu.

˙ Chiphunzitso cha utatu: Pasanathe zaka 300 ku-chokera pamene Baibulo linamalizidwa kulembedwa,wolemba mabuku wina yemwe ankakhulupirira uta-tu anawonjezera mawu pa 1 Yohane 5:7, akuti, “Ku-mwamba kuli Atate, Mawu, komanso Mzukwa Woyera:onsewa ndi mmodzi.” Katswiri wina wa Baibulo dzinalake Bruce Metzger, ananena kuti, “Kungoyambira mu500 C.E., mawu amenewa ankapezeka kwambiri m’mi-pukutu yachilatini chakale komanso m’Baibulo lachila-tini lotchedwa Vulgate.”

˙ Dzina la Mulungu: Omasulira Baibulo ambiri anaga-niza zochotsa dzina la Mulungu m’Baibulo chifukwacha zomwe Ayuda ankakhulupirira zoti akatchula dzi-na la Mulungu akhoza kuona malodza. Ndiyeno ana-yamba kumangogwiritsa ntchito maina audindo mo-nga “Mulungu” kapena “Ambuye.” Komatu nthawi zinam’Baibulo mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena zaanthu, mafano ngakhalenso Mdyerekezi.—Yohane 10:34, 35; 1 Akorinto 8:5, 6; 2 Akorinto 4:4.�

ZIMENE ZINATHANDIZA KUTI BAIBULO LISUNGIKE:Choyamba, ngakhale kuti anthu ena ankafuna kusinthauthenga wa m’Baibulo, panali ena ambiri amene anka-kopera Malemba mwaluso komanso mosamala. Mwa-chitsanzo, m’zaka za m’ma 500 ndi 900 C.E., Amaso-

� Kuti mudziwe zambiri, Onani Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawua Mulungu tsamba 1-13. Kabukuka kakupezekanso pawebusaiti yathuya www.jw.org/ny.

Baibulo Linapulumuka Ngakhale Kuti EnaAnkafuna Kusintha UthengaWake

Mpukutu wa Baibulo wopangidwandi gumbwa wa m’ma 200 C.E.,womwe unasungidwa mu Laibulaleya Chester Beatty P46.�The Trustees of the Chester Beatty Library, Dublin

Na. 4, 2016 7

rete anakopera Malemba Achiheberi n’kupanga bukulomwe limadziwika kuti Zolemba za Amasorete. Iwoakamakopera, ankawerenga liwu lililonse pofuna ku-tsimikizira kuti sanawonjezeremo mfundo zolakwika.Ngati akukayikira kuti mumpukutu womwe akugwiritsantchitowomuli mfundo zolakwika, ankalemba mfundo-zo m’mphepete mwa mpukutuwo. Amasorete sankafu-na kusintha uthenga wa m’Baibulo ngakhale pang’ono.Pulofesa wina dzina lake Moshe Goshen-Gottstein ana-lemba kuti: “Iwo ankadziwa kuti kusintha uthenga wam’Baibulo mwadala unali mlandu waukulu.”

Chachiwiri, masiku ano pali mipukutu yambiri yo-mwe inapezeka. Choncho akatswiri a Baibulo savutikakudziwa ngati pali mfundo zina zosiyana ndi za m’mi-pukutu yoyambirira. Mwachitsanzo, kwa zaka zambi-ri atsogoleri azipembedzo ankaphunzitsa kuti Maba-ibulo awo Achilatini anali odalirika kwambiri. Komachodabwitsa n’choti pa 1 Yohane 5:7 anaphatikiza-po mawu olakwika aja omwe tawatchula kumayambiri-ro kwa nkhaniyi. Ndipotu mawuwa anawaphatikizansom’Baibulo la King James. Komano mipukutu ina itape-zeka, m’pamene anazindikira kuti m’mipukutu yaka-

le munalibe mawuwa. Bruce Metzger analemba kuti:“M’mipukutu yakale (monga ya Chiameniya, Chiiti-opiya, Chikoputiki, Chiarabu ndi Chisilaviki), mulibemawu omwe anawawonjezera [pa 1 Yohane 5:7], kupa-tulapo m’mpukutu wa Chilatini tautchula uja. N’chifu-kwa chake m’mabaibulo ena okonzedwanso monga laKing James anachotsamo mawu olakwikawa.

Kodi mipukutu yakale imatsimikiziradi kuti uthengawam’Baibulo sunasinthe?Mipukutu ya ku NyanjaYaku-fa itapezeka mu 1947, akatswiri anali ndi mwayi wo-yerekezera Zolemba za Amasorete ndi zimene zinalim’mipukutuyi, yomwe inalembedwa zaka zoposa 1,000m’mbuyomo. Munthu wina yemwe anakonza nawo mi-pukutu ya ku Nyanja Yakufa ananena kuti mpukutuumodzi wokha “unapereka umboni wosatsutsika woso-nyeza kuti ntchito yokopera Malemba yomwe okoperaAchiyuda anagwira m’zaka zopitirira 1,000, inachitikamwaluso ndiponso mosamala kwambiri.”

Mumzinda wa Dublin, ku Ireland muli Laibulale yo-tchedwa Chester Beatty komwe anasungako pafupifupimipukutu yonse ya Malemba Achigiriki Achikhristu yo-pangidwa ndi gumbwa. Ina mwa mipukutuyi ndi yam’zaka za m’ma 100 C.E., zomwe zikusonyeza kuti ya-ngokhalapo kwa zaka 100 zokha, kuchokera pameneBaibulo linamalizidwa kulembedwa. Buku lina linane-nanso kuti, “mipukutu ya gumbwa imatsimikizira kutiuthenga wa m’Baibulo unalembedwa mwatsatanetsata-ne komanso kuti uthengawu sunasinthidwe paliponse.”—The Anchor Bible Dictionary.

ZOTSATIRA ZAKE: Mipukutu yambiri yakale yomweinapezeka yathandiza kuti uthenga wa m’Baibulo ukha-le wolondola. Katswiri wina dzina lake Frederic Kenyonanalemba zokhudza Malemba Achigiriki Achikhristukuti: “Palibenso buku lina lakale lomwe lili ndi umboniwotsimikizira kuti ndi lolondola kuposa Baibulo, ndipopalibe katswiri aliyense woganiza bwino yemwe anga-tsutse zoti uthenga womwe tili nawowu ndi wodali-rika.” Ponena za Malemba Achiheberi, katswiri winadzina lakeWilliam Henry Green, ananena kuti: “Tinga-nenedi motsimikiza kuti palibenso buku lina lakale lo-mwe linamasuliridwa ndi kukopedwa molondola kupo-sa Baibulo.”

“Tinganenedi motsimikiza kuti palibenso buku lina lakalelomwe linamasuliridwa ndiponso kukopedwa

molondola kuposa Baibulo”

Amasorete ankakopera Malembamosamala kwambiri

8 NSANJA YA OLONDA

Masiku ano mukhoza kupeza ndiponso kuwerengaBaibulo mosavuta. Ndipo ngati mwasankha Baibu-lo lomwe linamasuliridwa molondola, m’posavutakutsimikizira kuti uthenga wake ndi wochokera-di m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo.� M’nkhani

� Onani nkhani yakuti, “Kodi Mungadziwe Bwanji Baibulo Lomasuli-ridwa Bwino?” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008.

zapitazi taona kuti Baibulo linapulumuka ngakha-le kuti likanatha kuwola, anthu ena ankalitsutsa,komanso ankafuna kusintha uthenga wake. Koman’chifukwa chiyani linapulumuka modabwitsachonchi?Anthu ambiri amene akuphunzira Baibulo ama-

vomereza zomwe mtumwi Paulo analemba kuti:“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Ti-moteyo 3:16) Anthuwa amakhulupirira kuti Bai-bulo linapulumuka chifukwa chakuti ndi Mawu aMulungu komanso Iye analiteteza. Faizal yemwewatchulidwa m’nkhani yoyambirira, anaganiza zo-yamba kuphunzira Baibulo pofuna kutsimikizirazimenezi. Iye anadabwa ataona kuti zinthu zambi-ri zimene anthu amaphunzitsa m’matchalitchi awosizichokera m’Baibulo. Faizal anachita chidwi kwa-mbiri ataphunzira cholinga cha Mulungu chokhu-dza dziko lapansi kuchokera m’Baibulo.Iye ananena kuti: “Panopa sindikukayika nga-

khale pang’ono kuti Baibulo lomwe ndili nalondi mphatso yochokera kwa Mulungu. Komansongati Mulungu yemwe ndi Wamphamvuyonse ana-kwanitsa kulenga chilengedwechi, kodi angalephe-re kutipatsa buku ndi kuliteteza kuti tiziliwere-nga? Munthu yemwe angatsutse zimenezi ndiyekuti akuderera mphamvu za Mulungu, yemwe ndiWamphamvuyonse, nanga ine ndani kuti ndichitezimenezi?”—Yesaya 40:8. ˇ

N’chifukwa Chiyani BaibuloLinapulumuka?

“Panopa sindikukayika ngakhalepang’ono kuti Baibulo lomwendili nalo ndi mphatsoyochokera kwa Mulungu”

Nkhanizi zafotokoza zomwezinathandiza kuti Baibulolisawonongedwe. Koman’chiyani chingakutsimikizirenikuti Baibulo ndi “mawu aMulungu” osati buku la nthanozongolembedwa ndi anthu?

(1 Atesalonika 2:13) Tikukulimbikitsani kuti muonerevidiyo ya pa jw.org/ny yakuti, Kodi TingadziweBwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? (Pitani pamenepalembedwa kuti, MABUKU � MAVIDIYO)

w

Na. 4, 2016 9

Kale atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankasiyana maganizo pankhani ya zifukwa zomwe mwamuna angathetsere ukwati. Mwa-chitsanzo, nthawi ina Afarisi anafunsa Yesu kuti: “Kodi n’kololekakuti mwamuna asiye mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”—Mateyu19:3.

Chilamulo cha Mose chinkalola mwamuna kusiya mkazi wake nga-ti “wam’peza ndi vuto linalake.” (Deuteronomo 24:1) M’nthawi yaYesu, kunali sukulu ziwiri zomwe ankaphunzitsirako arabi kapenakuti aphunzitsi achiyuda. Kusukuluzi ankaphunzitsa mfundo zosiya-na zokhudza lamuloli. Mwachitsanzo, kusukulu ya Shammai anka-phunzitsa mfundo zokhwima ndipo ankati ukwati ukhoza kutha po-khapokha ngati wina wachita chigololo. Pomwe kusukulu ya Hillelankaphunzitsa kuti mwamuna akhoza kusiya mkazi wake chifukwacha vuto lina lililonse la m’banja ngakhale laling’ono. Mwachitsanzo,ankaphunzitsa kuti mwamuna akhoza kuthetsa ukwati ngati mkaziwake sanaphike bwino chakudya kapenanso akaona mkazi wina wo-kongola.

Kodi Yesu anayankha bwanji funso la Afarisi? Iye ananena mosa-bisa mawu kuti: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachi-ta chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”—Ma-teyu 19:6, 9. ˇ

Kodi atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankalolakuti mwamuna asiye mkazi wake pa zifukwa ziti?

KALATAYOTHETSERA UKWATI YAZAKA ZA M’MA 71 KAPENA 72 C.E.

Courtesy Israel Antiquities Authority

Kale Ayuda ankachita mantha kwambiri ndi matenda a khate omweamatchulidwa m’Baibulo. Matendawa anali oopsa chifukwa anka-gwira mitsempha yotumiza uthenga ku ubongo ndipo zinkachititsakuti munthu alumale. Pa nthawiyi kunalibe mankhwala a khate.Ndipo odwala matendawa ankawaika kwaokha komanso ankayene-ra kuchenjeza ena za matenda awowo.—Levitiko 13:45, 46.

Atsogoleri achiyuda anakhazikitsa malamulo okhwima koma-nso osagwirizana ndi zomwe Mawu a Mulungu ankanena zokhu-dza anthu akhate. Zimenezi zinkachititsa kuti anthuwa azivutikakwambiri. Mwachitsanzo, arabi anakhazikitsa malamulo akuti mu-nthu aliyense akaona wakhate azitalikirana naye mamita awiri.Komanso ankanena kuti ngati kukuwomba mphepo, azitalikirananaye mamita 45. Buku la malamulo ndi miyambo ya Ayuda (Tal-mud), linati lamulo la m’Baibulo loti akhate “azikhala kunja kwamsasa,” linkatanthauza kuti sayenera kukhala mumzinda uliwonsewampanda. Arabi akaona wakhate ali mumzinda, ankamugendan’kumuuza kuti: “Pita kumalo ako, usapatsire anthu ena matendaakowo!”

Komatu Yesu ankachita zinthu zosiyana kwambiri ndi atsogole-riwa. Iye sankathamangitsa akhate, koma ankafunitsitsa kuwakhu-dza ndiponso kuwachiritsa.—Mateyu 8:3. ˇ

KODI MUKUDZIWA?

Kodi Yesu ankasiyana bwanji ndi Arabi pochitazinthu ndi anthu akhate?

10 NSANJA YA OLONDA

KODI N’ZOTHEKA KUTHETSA ZACHIWAWA?N’chifukwa chiyani zachiwawa zikuchitika padziko

lonse? Pali zifukwa zambiri monga izi: Kupondereza-na pakati pa anthu olemera ndi osauka, uchidakwa,kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, ku-ona moyo wa anthu ena ngati wosafunika komansokukulira m’banja kapena m’dera lomwe anthu amako-nda zachiwawa. Anthu enanso amachita zachiwawachifukwa chakuti anthu ambiri ochita khalidweli sa-patsidwa chilango chokhwima.Komabe mayiko ena akuyesetsa kuchepetsa zachi-

wawa. Mwachitsanzo, mumzinda wa Sao Paulo, kuBrazil, chiwerengero cha anthu ophedwa mwachisa-wawa chatsika kwambiri m’zaka 10 zapitazi. Ngakha-le zili choncho, zauchifwamba zimachitikabe mobwe-rezabwereza moti anthu 10 pa 100,000 amaphedwa.

Ndiyeno funso n’kumati, n’chiyani chingathandizekuti zachiwawa zitheretu padziko lonse?Kuti zachiwawa zitheretu, anthu afunika kusintha

mmene amaonera zinthu komanso khalidwe lawo.Mwachitsanzo, ayenera kusiya kunyada, umbombondi kudzikonda, n’kuyamba kukhala achikondi, aule-mu ndiponso oganizira ena.Kodi n’chiyani chingathandize munthu kuti asiye

makhalidwe oipa? Taonani zimene Baibulo limaphu-nzitsa:

ˇ “Chifukwa kukonda Mulungu kumatanthauzakusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndiosalemetsa.”—1 Yohane 5:3.

ˇ “Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoi-pa.”�—Miyambo 8:13.

� Dzina la Mulungu ndi Yehova ndipo limapezeka m’Baibulo.

KODI ZACHIWAWA ZIDZATHAPADZIKOLI?Kodi inuyo kapena munthu wina wa m’banja lanu anachitiridwapo zinthu zachiwawa?Kodi mumachita mantha kuti tsiku lina zidzakuchitikirani? Anthu ena amanena kuti zachiwawa“zikuchuluka padziko lonse ndipo zikuchititsa kuti anthu azikumana ndi mavuto azaumoyo.”Taonani zitsanzo izi:

NKHANZA ZAM’BANJAKOMANSOZOKHUDZAKUGONANA: Lipoti lina labungwe la United Nations linanena kuti: “Mayi mmodzi pa atatu alionseanamenyedwapo ndi mwamuna wake kapenanso kuchitiridwa nkhanza zokhudzakugonana ndi munthu womudziwa. Komanso mayi mmodzi pa amayi 5 alionseakhoza kugwiriridwa.”

UCHIFWAMBANDI UMBANDA:Malipoti amasonyeza kuti ku United Stateskokha kuli magulu a zauchifwamba oposa 30,000. Ndipo ku Latin Americapafupifupi munthummodzi pa atatu alionse anachitiridwapo zauchifwamba.

KUPHAANTHU MWACHISAWAWA: Kafukufuku amasonyeza kuti m’chakacha 2012 chokha, anthu pafupifupi 500,000 anaphedwa ndi zigawengapadziko lonse. Chiwerengerochi ndi chachikulu poyerekezera ndi anthu omweanaphedwa pa nkhondom’chakachi. Mayiko a kum’mwera kwaAfrica komansoku Central America ndi omwe anali ndi chiwerengero chokwera kwambiricha anthu ophedwa. Mwachitsanzo, ku Latin America kunaphedwa anthuoposa 100,000 m’chaka cha 2013, ndipo ku Brazil kunaphedwa anthuoposa 50,000. Kodi pamenepa tinganene kuti zachiwawa zidzatha padzikoli?

Anthu achiwawa angasinthe khalidwe lawo ngatiatamakonda Mulungu komanso kupewa zinthu zo-mwe zingamukhumudwitse. Ndipotu zimenezi n’zo-theka.Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Alex,� amene anakhala

m’ndende ina ya ku Brazil kwa zaka 19, chifukwa chamilandu yosiyanasiyana yomenya ndi kuvulaza anthu.Iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Ye-hova ndipo anabatizidwa mu 2000. Kodi anasinthadikhalidwe lakeli? Alex anasinthiratu ndipo anati: “Pa-nopa ndimakonda kwambiri Mulungu chifukwa ndi-madziwa kuti anandikhululukira. Komatu ndinasiyamakhalidwewa chifukwa chokonda Mulungu koma-nso kusafuna kumukhumudwitsa.”Cesar wa ku Brazil ankathyola nyumba za anthu ko-

manso kuba moopseza ndi mfuti. Iye anachita zime-nezi kwa zaka 15. Ndiye n’chiyani chinamuthandizakuti asinthe? Pa nthawi imene anali kundende, anaku-mana ndi a Mboni za Yehova ndipo anayamba ku-phunzira Baibulo. Cesar anafotokoza kuti: “Ndita-ngoyamba kuphunzira, ndinazindikira cholinga chamoyo ndiponso ndinayamba kukonda Mulungu ko-manso kumuopa. Zimenezi zinandithandiza kuti ndi-siyiretu kuchita zinthu zoipa zomwe amadana nazo.Sindinkafunanso kuchita chilichonse chosonyeza kutisindikuyamikira chifundo chake. Choncho ndinasi-ntha khalidwe langa.”Zimene zinachitikira Alex ndi Cesar, zikusonyeza

kuti Baibulo lili ndi mphamvu zothandiza anthu kusi-ntha zochita komanso maganizo oipa. (Aefeso 4:23)Alex ananenanso kuti: “Zimene ndinaphunzira m’Ba-ibulo zinali ngati madzi oyera bwino omwe ankayere-tsa makhalidwe anga pang’onopang’ono. Ndinali ndi-sanaganizepo kuti ndingadzasinthe chonchi.” Uwundi umboni wakuti tikamawerenga uthenga wa m’Ba-ibulo womwe ndi woyera, tingathe kuchotsa magani-zo alionse oipa mumtima mwathu. Mawu a Mulungualidi ndi mphamvu yoyeretsa maganizo a anthu. (Ae-feso 5:26) Monga mmene taonera, anthu omwe kaleanali ndi makhalidwe oipa akhoza kusintha n’kukhalaachifundo komanso amtendere. (Aroma 12:18) Ndipoakamatsatira mfundo za m’Baibulo, amakhalanso ndimtendere wamumtima.—Yesaya 48:18.A Mboni za Yehova opitirira 8 miliyoni omwe aku-

pezeka m’mayiko oposa 240, akudziwa bwino chime-ne chingathandize kuti zachiwawa zitheretu. Ngakha-le kuti ndi ochokera m’mitundu yosiyanasiyana, onse

�Mayina asinthidwa.

amakonda Mulungu komanso kumuopa. Amakonda-nanso kwambiri ndipo amakhala mwamtendere ngatibanja limodzi. (1 Petulo 4:8) Umenewutu ndi umbo-ni wakuti n’zotheka kuthetsa zachiwawa padzikoli.

ZINTHU ZACHIWAWA ZITHA POSACHEDWAPABaibulo limalonjeza kuti posachedwapa Mulungu

athetsa zachiwawa zonse padzikoli. Ndipo limatitsi-mikizira kuti anthu onse okonda zachiwawa adza-phedwa “m’tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko chaanthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 3:5-7) Pa nthawi-yi sikudzakhalanso anthu ozunza ena. Koma kodi ti-ngatsimikize bwanji kuti Mulungu ndi wofunitsitsakuthetseratu zachiwawa?Baibulo limanena kuti “Mulungu amadana kwambi-

ri ndi aliyense wokonda chiwawa.” (Salimo 11:5) Mle-ngi wathu amakonda mtendere ndi chilungamo. (Sa-limo 33:5; 37:28) N’chifukwa chake sadzalola kutianthu ochita zachiwawa akhalepo mpaka kalekale.Dziko latsopano komanso lamtendere layandiki-

ra. (Salimo 37:11; 72:14) Choncho tikukulimbikitsanikuti muyambe kuphunzira Baibulo ndi a Mboni zaYe-hova kuti mudziwe zimene mungachite kuti mudza-khale nawo m’dziko limeneli. ˇ

Phunzirani zimene mungachite kuti mudzakhalem’dziko lopanda chiwawa

Onerani vidiyo yakuti,“Zinthu Zinayamba KuyendaBwino” pawebusaiti yawww.jw.org/ny, kuti muonezimene bambo wina ankachitaasanaphunzire Baibulo.(Pitani pamene palembedwakuti MABUKU � MAVIDIYO)

w

12 NSANJA YA OLONDA

KALE LANGA: Bambo anga anachoka ku Germany kupita ku Austra-lia mu 1949, kukafufuza ntchito m’makampani a migodi ndi mage-tsi. Iwo anakakhala m’mudzi wina wotchedwa Victoria, ndipo n’ko-mwe anakwatirana ndi mayi anga. Ineyo ndinabadwa mu 1953.

Patangodutsa zaka zochepa, mayi anga anayamba kuphunziraBaibulo ndi a Mboni za Yehova. Choncho ndinayamba kumva mfu-ndo za m’Baibulo ndili wamng’ono. Koma bambo anga ankadanandi chipembedzo chilichonse, ndipo anayamba kutichitira nkhanzakwambiri. Mayi anga ankakhala mwamantha moti ankaphunzira Ba-ibulo mobisa. Komabe anayamba kukonda zomwe ankaphunzirazo.Bambo akachoka, amayi ankapeza mpata wofotokozera ineyo ndimchemwali wanga zimene aphunzira m’Baibulo. Ankatiuza kuti dzi-koli lidzakhala paradaiso komanso kuti tingakhale osangalala nga-ti titamatsatira mfundo za m’Baibulo.—Salimo 37:10, 29; Yesaya48:17.

Ndili ndi zaka 18, ndinachoka pakhomo chifukwa cha nkhanza zabambo anga. Ngakhale kuti ndinkakhulupirira zonse zomwe amayianandiphunzitsa, sindinkazigwiritsa ntchito. Kenako ndinayambantchito ya zamagetsi m’migodi ya malasha. Ndinakwatira ndili ndizaka 20, ndipo patadutsa zaka zitatu, tinabereka mwana wamkazi.Kenako ndinaganiza zoyambiranso kuphunzira Baibulo chifukwandinkadziwa ndithu kuti mfundo zake zikhoza kuthandiza banjalathu. Choncho ndinayamba kuphunzira ndi a Mboni za Yehova.Koma mkazi wanga ankadana nawo kwambiri. Tsiku lina nditapitakumisonkhano ya Mboni zaYehova, anandiuza kuti ngati ndikufunabanja ndisiye kuphunzira. Ndinasowa chochita moti ndinasiyadi ku-phunzira komanso kucheza ndi a Mboni. Komabe patapita nthawindinadzimvera chisoni chifukwa cholephera kutsatira zinthu zomwezikanandithandiza.

Tsiku lina ndili kuntchito anzanga anandionetsa zithunzi zolaula.Nditangoziona zinandisangalatsa komabe nthawi yomweyo zinandi-nyansa ndipo ndinayamba kudziimba mlandu kwambiri. Ndinaku-mbukira zimene ndinaphunzira m’Baibulo ndipo ndinkadziwa kutiMulungu akhoza kundilanga. Koma nditayamba kuzionera mobwe-rezabwereza, ndinaona kuti zinalibe vuto lililonse moti chinango-khala chizolowezi.

Ndinachita zimenezi kwa zaka 20 ndipo ndinkanyalanyaza mfu-ndo zabwino zimene amayi anandiphunzitsa, kenako ndinaziiwali-

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinasintha khalidwe langamovutikira kwambiri

YOFOTOKOZEDWA NDIJOSEF MUTKE

CHAKA CHOBADWA1953

DZIKOAUSTRALIA

POYAMBANDINKAKONDA KUONERA ZOLAULA

Na. 4, 2016 13

ratu. Khalidwe langa linaipa chifukwa choonera zolau-la. Ndinali wowola mkamwa ndiponso ndinkakondanthabwala zotukwana. Ndinkaona kuti palibe vuto ku-gonana ndi wina aliyense moti ndinkagonananso ndiakazi ena. Tsiku lina nditadziyang’ana pagalasi ndi-nadzimvera chisoni ndiponso ndinadziona kuti ndinewachabechabe.

Banja langa linatha ndipo moyo wanga unangokha-la ngati nsanza zokhazokha. Ndiyeno ndinapempherakwaYehova mochokera pansi pamtima. Kenako ndina-yambiranso kuphunzira Baibulo ngakhale kuti panalipatadutsa zaka 20. Pa nthawiyi n’kuti bambo anga ata-mwalira ndipo mayi anga anali atabatizidwa.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Zo-mwe ndinkachita zinali zosemphana kwambiri ndimfundo zapamwamba za m’Baibulo. Pa nthawiyi ndi-nkafunitsitsa kukhala ndi mtendere wa m’magani-zo womwe Baibulo limanena. Choncho ndinaganizazosintha mmene ndinkayankhulira komanso khalidwelokwiya msanga. Ndinaganizanso zosiya kuchita za-chiwerewere, kutchova njuga, kumwa mwauchidakwakomanso kubera abwana anga.

Anzanga akuntchito sankamvetsa chifukwa chime-ne ndinkafunira kusiya makhalidwe oipawa. Ndipokwa zaka zitatu anayesetsa kuchita zinthu zofunakundigwetsa ulesi. Nthawi zina akandimva ndikuya-nkhulanso mawu owola kapenanso ndikakwiya, anka-sangalala ndipo ankanena kuti: “Eya! Ameneyo ndeJoe timamudziwa ife.” Kunena zoona mawu amenewaankandilasa mumtima. Ndipo ndinkaona kuti ndinewolephera basi.

Kuntchito kwathu kunkapezeka mabuku ndiponsomavidiyo ambiri a zithunzi zolaula. Ndipo anzangaankakonda kutumizirana zithunzizi pamakompyuta

monga mmene ndinkachitira poyamba. Ndinkafuni-tsitsa nditasiya kuonera zolaula koma nthawi zonseanzangawo ankandikakamiza kuti ndizionerabe. Ndi-yeno ndinafotokozera munthu yemwe ankandiphu-nzitsa Baibulo kuti andithandize. Iye anandimvetseramoleza mtima n’kundiwerengera mavesi a m’Baibuloomwe anandithandiza kudziwa mmene ndingathetse-re vutolo. Anandilimbikitsanso kuti ndisasiye kupe-mphera kwa Yehova.—Salimo 119:37.

Tsiku lina ndinaitanitsa anthu onse omwe ndinka-gwira nawo ntchito. Kenako ndinawauza kuti ate-nge mowa n’kupatsa anzathu ena awiri amene anasi-ya uchidadwa. Komano chodabwitsa n’choti aliyenseanadzuma n’kunena kuti: “Sitingachite zimenezo! Iwesukudziwa kuti anthuwa akhala akuvutika ndi uchida-kwa?” Ndiye nanenso ndinawayankha kuti: “Eetu, ine-nso ndikulimbana ndi vuto loonera zolaula.” Pompoanasiyiratu kundikakamiza.

Patapita nthawi Yehova anandithandiza kusiyiratukhalidwe loipali. Mu 1999, ndinabatizidwa n’kukhalawa Mboni za Yehova ndipo ndimasangalala kwambirikuti Yehova wandipatsanso mwayi wokhala ndi moyowosangalala.

Panopa ndimamvetsa chifukwa chake Yehova ama-dana ndi khalidwe loonera zolaula lomwe ndinkaliko-nda. Iye ndi Atate wachikondi ndipo ankafuna ku-nditeteza kuti ndisakumane ndi mavuto omwe anthuamene akhalidweli amakumana nawo. Ndaona kutimfundo ya palemba la Miyambo 3:5, 6 ndi yoona.Lembali limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wakowonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu.Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adza-wongola njira zako.” Choncho mfundo za m’Baibulozanditeteza kwambiri komanso zandithandiza kuti zi-nthu zizindiyendera bwino.—Salimo 1:1-3.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Nthawi yomwe ndinkao-nera zolaula, ndinkadziona kuti ndine wachabechabe.Koma panopa ndimaona kuti ndine munthu wofunika,wamakhalidwe abwino, ndili ndi mtendere wamumti-ma, komanso ndimadziwa kuti Yehova anandikhulu-lukira ndiponso amandithandiza. M’chaka cha 2000,ndinakwatira mkazi wokongola dzina lake Karolin. Na-yenso amakonda kwambiri Yehova ndipo timakhalamwamtendere. Timaona kuti ndi mwayi waukulu ku-khala m’gulu la Akhristu amakhalidwe abwino koma-nso okondana, omwe ali padziko lonse. ˇ

KODI ndinu Mkhristu? Ngati ndi choncho, dziwanikuti simuli nokha. Padziko lonse pali anthu opo-

sa 2 biliyoni omwe amati amatsatira Khristu, ndipo izizikusonyeza kuti pafupifupi munthu mmodzi pa atatualionse, ndi Mkhristu. Masiku ano pali zipembedzo za-mbiri zachikhristu, koma zimasiyana pa nkhani ya zi-khulupiriro. Choncho zimene mumakhulupirira zinga-siyane ndi zomwe anthu ena omwe amati ndi Akhristuamakhulupirira. Kodi kukhulupirira zilizonse kuli ndivuto? Inde, chifukwa Akhristu amayenera kutsatiramfundo zopezeka m’Baibulo.

Anthu omwe ankatsatira Yesu Khristu anayamba ku-dziwika kuti “Akhristu.” (Machitidwe 11:26) Iwo sa-nkadziwika ndi maina ena chifukwa panali chikhulupi-riro chimodzi chokha chachikhristu. Popeza kuti YesuKhristu ndi yemwe anayambitsa Chikhristu, Akhristuonse ankatsatira malangizo komanso zimene iye anka-waphunzitsa. Kodi zimene amaphunzitsa kutchalitchikwanu zimagwirizana ndi zimene Khristu ankaphunzi-tsa, komanso zomwe otsatira ake oyambirira ankakhu-lupirira? Kodi mungadziwe bwanji ngati zimagwiriza-na? Njira yabwino kwambiri n’kudziwa zimene Baibulolimanena.

KODI MUNGAYEREKEZERE ZOMWEMUMAKHULUPIRIRA NDI ZIMENEBAIBULO LIMAPHUNZITSA?

1 FUNSO: Kodi Mulungu ndi ndani?

YANKHO: Ndi Yehova amenenso ndiAtate ake aYesu, alibe mapetokomanso ndi Mulungu yemweanalenga zinthu zonse.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:˙ “Nthawi zonse tikamakupemphererani, timayamika Mulungu,

Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.”—Akolose 1:3.˙ “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu,

kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthuzonse.”—Chivumbulutso 4:11.

˙ Onaninso Aroma 10:13; 1 Timoteyo 1:17.

2 FUNSO: Kodi Yesu Khristu ndi ndani?YANKHO: Ndi Mwana woyamba waMulungu. Yesu anachita kulengedwa,choncho tingati ali ndi chiyambi.Ndipo amamvera mokhulupirikazimene Mulungu akufuna.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:˙ “Atate ndi wamkulu kuposa ine.”—Yohane 14:28.˙ “[Yesu] ndiye chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo, woyamba

kubadwa wa chilengedwe chonse.”—Akolose 1:15.˙ Onaninso Mateyu 26:39; 1 Akorinto 15:28.

3 FUNSO: Kodi mzimu woyera n’chiyani?YANKHO: Mzimu woyera ndi mphamvuyomwe Mulungu amagwiritsa ntchitokuti akwaniritse zomwe akufuna.Koma si munthu. Anthu akhozakudzozedwa ndi mzimu woyerakomanso kupatsidwa mphamvu.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:˙ “Tsopano Elizabeti atamva moni wa Mariya, khanda limene linali

m’mimba mwakemo linadumpha. Ndipo Elizabeti anadzazidwandi mzimu woyera.”—Luka 1:41.

˙ “Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandiramphamvu.”—Machitidwe 1:8.

˙ Onaninso Genesis 1:2; Machitidwe 2:1-4; 10:38.

14 NSANJA YA OLONDA

Taganizirani izi: Yesu Khristu ankalemekeza kwa-mbiri Malemba chifukwa ndi Mawu a Mulungu. Iyeankadana ndi anthu omwe ankalimbikitsa miyamboya anthu m’malo mophunzitsa mfundo za m’Baibulo.(Maliko 7:9-13) Choncho tinganene kuti otsatira enie-ni a Yesu amayenera kutenga zikhulupiriro zawo m’Ba-ibulo. Ndiyetu Mkhristu aliyense ayenera kudzifunsakuti, ‘Kodi zimene amaphunzitsa kutchalitchi kwathuzimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena?’ Kuti mu-yankhe funsoli, mungachite bwino kuyerekezera zime-ne mumaphunzira ku tchalitchi kwanuko ndi zimeneBaibulo limanena.Yesu ananena kuti tiyenera kulambira Mulungu

m’choonadi ndipo choonadi chimenechi chimapezekam’Baibulo. (Yohane 4:24; 17:17) Nayenso mtumwi Pa-ulo ananena kuti tidzapulumuka ngati timadziwa “cho-onadi molondola.” (1 Timoteyo 2:4) Choncho zimenetimakhulupirira ziyenera kugwirizana ndi mfundo zo-londola za m’Baibulo. Zimenezitu n’zofunika kwambi-ri chifukwa kupanda kutero sitingadzapulumuke.

KODI ZIMENE TIMAKHULUPIRIRATINGAZIYEREKEZERE BWANJI NDI BAIBULO?Tikukupemphani kuti muwerenge mafunso 6 amene

ali m’nkhaniyi komanso muone mmene Baibulo likuya-nkhira mafunsowo. Muwerengemavesi amene aikidwa-wo ndipo muone ngati akugwirizana ndi mayankhoamene ali pansi pa mafunsowo. Kenako mudzifunsekuti, ‘Kodi zimene ndimaphunzira kutchalitchi kwathuzikugwirizana ndi zimene Baibulo likunenazi?’Mafunso komanso mayankho omwe ali m’nkhaniyi

akuthandizani kwambiri. Kodi mukufuna kuyerekezerazinanso zimene mumaphunzira kutchalitchi kwanu ndizomwe Baibulo limanena? A Mboni za Yehova akho-za kukuthandizani kuti mudziwe mfundo zolondola zam’Baibulo. Mungachite bwino kupempha wa Mboni zaYehova kuti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere. Mu-khozanso kupita pawebusaiti yathu ya jw.org/ny. ˇ

4 FUNSO: Kodi Ufumu wa Mulungun’chiyani?YANKHO: Ufumu wa Mulungundi boma lakumwamba. Mfumu yakendi Yesu. Posachedwapa Ufumuwuukwaniritsa cholinga cha Mulungupadziko lonse.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:˙ “Mngelo wa 7 analiza lipenga lake. Ndipo kumwamba

kunamveka mawu osiyanasiyana, akunena mokweza kuti: ‘Ufumuwa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake.Iye adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.’ ”—Chivumbulutso11:15.

˙ Onaninso Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.

5 FUNSO: Kodi anthu onse abwinoamapita kumwamba?YANKHO: Ayi. Mulungu anasankhaanthu ochepa otchedwa “kagulu kankhosa” kuti akakhale kumwamba.Iwo akakhala mafumu limodzi ndiYesu ndipo adzalamulira anthupadziko lonse.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:˙ “Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu

wavomereza kukupatsani Ufumu.”—Luka 12:32.˙ “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira

monga mafumu limodzi naye.”—Chivumbulutso 20:6.˙ Onaninso Chivumbulutso 14:1, 3.

6 FUNSO: Kodi cholinga cha Mulunguchokhudza anthu komanso dzikolapansili n’chotani?YANKHO: Mu Ufumu wa Mulungu,dziko lapansili lidzakhala paradaisondipo anthu okhulupirika adzakhalandi moyo wathanzi, mtenderewochuluka ndipo sadzafanso.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:˙ “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi

mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.˙ “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo

imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula,ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

˙ Onaninso Salimo 37:29; 2 Petulo 3:13.

wp

16

.4-C

N1

60

32

2Zimene Baibulo

Limaphunzitsa

Kodi anthu ndi ameneanayambitsa kupembedza?ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti anthu anaya-mbitsa okha zoti azipembedza. Ena amakhulu-pirira kuti Mulungu amagwiritsa ntchito chipe-mbedzo pofuna kuthandiza anthu kuti akhalenaye pa ubwenzi.Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENAPali “kupembedza koyera ndi kosaipitsidwakwa Mulungu ndi Atate wathu.” (Yakobo 1:27)Mfundoyi ikusonyeza kuti pali chipembedzochoona chimene Mulungu anayambitsa.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE BAIBULO LIMANENA˙ Mulungu amasangalala ndi chipembedzo chimenechimaphunzitsa mfundo za m’Baibulo.—Yohane 4:23, 24.

˙ Zipembedzo zimene zimaphunzitsa mfundo zaanthu n’zosathandiza.—Maliko 7:7, 8.

Kodi munthu ayenera kukhalam’chipembedzo chinachake?KODI MUNGAYANKHE BWANJI?˙ Inde ˙ Ayi ˙ Mwina

ZIMENE BAIBULO LIMANENA“Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pachikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kuso-nkhana pamodzi.” (Aheberi 10:24, 25) Cho-ncho Mulungu amafuna kuti anthu ameneamamulambira azisonkhana pamodzi mogwiri-zana.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE BAIBULO LIMANENA˙ Anthu omwe amalambira Mulungu mogwirizanaamayenera kukhulupirira mfundo zofanana.—1 Akorinto 1:10, 11.

˙ Anthu a m’chipembedzo chimene Mulungu ama-vomereza ndi ogwirizana padziko lonse.—1 Petulo2:17.

KODI BAIBULO LIMANENA ZOTANI?

Nditumizireni buku lakuti, ZimeneBaibulo Limaphunzitsa?Kuti mudziwe zambiri, werenganimutu 15 m’buku ili, lofalitsidwa ndia Mboni za YehovaBukuli likupezekanso pawebusaitiyathu ya www.jw.org/ny

CHINENERO ����������������������������������������������������������������������������������������������

DZINA �������������������������������������������������������������������������������������������������������

ADIRESI ����������������������������������������������������������������������������������������������������

�����������������������������������������������������������������������������������������������������������������

�����������������������������������������������������������������������������������������������������������������

Kuti mupeze adiresi yoyenera, onani tsamba 2

sMungapange dawunilodimagaziniyi ndi enanso am’mbuyomu kwaulere

Baibulo likupezeka paIntaneti m’zinenerozoposa 130

Pangani sikanikachidindo akakapena pitanipawebusaitiyathu yawww.jw.org/ny

no

p